Dziko Lotchova Njuga
MAKINA otchovera njuga nthaŵi zambiri amatchedwa achifwamba adzanja limodzi. Koma mosiyana ndi achifwamba enieni, iwo samakakamiza ndalama kuchoka kwa munthu; anthu amandandama monga nkhosa kuti adyeredwe ndi iwo.
Mu Fedulo Ripabuliki ya Jeremani muli pafupifupi makina oterowo okwanira 420,000, otanganitsidwa kulanda ndalama zokwanira pafupifupi $900,000,000 kuchokera kwa anthu a ku Jeremani chaka chirichonse. Anthu mamiliyoni asanu kumeneko amathera ola limodzi mlungu uliwonse kuika ndalama m’makinawo; anthu okwanira 80,000 amawononga maola oposa asanu pamlungu kumeneko.
Spanya tsopano ikunyadira makina otchovera njuga okwanira 750,000. Kutchova njuga kunaikidwa kukhala kwalamulo kumeneko mu 1977. Pofika mu 1988, Aspanya anali kale kuwononga ndalama zokwanira $25,000,000,000 pachaka pamitundu yonse yakutchova njuga. Kukusimbidwa kuti Aspanya okwanira 200,000 ndianthu otchova njuga omwerekera. Anthu a ku Italiya anatchova njuga ndi ndalama zokwanira $12,000,000,000 mu 1989—kapena pafupifupi $210 kaamba ka munthu aliyense, kuphatikizapo ana. M’mlungu umodzi wokha mu 1990, Ataliyana anawononga $70 miliyoni kubetchera maseŵera a mpira.
Otchova njuga mu United States amawononga ndalama zoposa $200,000,000,000 pachaka pamitundu yalamulo yokha ya kutchova njuga! Pulezidenti wa malo ambirimbiri otchovera njuga kumeneko anadzitama posachedwapa nati: “Kutchova njuga m’dziko lino ndiko indasitale yokula mofulumira koposa, njaikulu mofanana ndi bajeti yapachaka ya [gulu lankhondo la U.S.].” Iye analinganiza kukonda kutchova njuga kwa nzika za ku Amereka kukhala kofanana ndi “chisonkhezero cha nthanthi” ndi kufunitsitsa kuika moyo pachiswe kumene kunasonkhezera otumba malo ndi akalambula bwalo a dzikolo kalelo. Koma lingaliro la wotchova njuga lakupeza chuma panthaŵi yomweyo nlosiyana kwenikweni ndi zaka za kukha thukuta ndi kuvutika zimene ofufuza ndi akalambula bwalo anaika m’ntchito yawo.
Katswiri wa mayanjano a anthu Vicki Abt anati: “Malottery amaloŵetsa lingaliro lakuti mfupo nzosagwirizana ndi zoyesayesa zanu.” Kulingalira koteroko kungawononge moipa mtundu wa moyo. Ngongole, umphaŵi, zizoloŵezi za ntchito zoipitsidwa, mabanja osweka—izi ndizo zotulukapo zochepa za kutchova njuga. Kwa anthu mamiliyoni ambiri, chiŵerengero chomakulakula chikumakhala achichepere, kutchova njuga kumasanduka chisonkhezero chokakamiza chosalamulirika. Zowonadi, Baibulo nlolondola pamene likuti ‘muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama.’—1 Timoteo 6:10.