Mmene Adokotala Amapeŵera Aids
UPANDU wa kuyambukiridwa ndi AIDS kupyolera m’mwazi wachititsa akatswiri ena akutumbula kutenga chimene The New York Times imatcha “chida chatsopano chotumbulira cha nyengo ya AIDS.” Kwa katswiri wotumbula chidacho chimaphatikizapo “nsapato zamphira, nkhwindi yaitali yosakhoza kugwira madzi, mapeya aŵiri a maglovu, zovala kumanja zosakhoza kugwira madzi ndi magalasi akumaso.” Ndipo pochita ndi matenda ogwira mwazi kwenikweni, ikutero Times, “amavala chisoti chokhala ndi chotetezera kumaso.”
Kwakukulukulu, chakumapeto kwa 1990, Federal Centers for Disease Control inanena kuti mwa matenda 153,000 ochitiridwa lipoti a AIDS, 637 anali asing’anga amchipatala, 42 anali akatswiri otumbula, 156 anali adokotala amano ndi akatswiri a zaukhondo, ndipo 1,199 anali anamwino.
AIDS inazindikiridwa kwanthaŵi yoyamba mu 1981. Kwakanthaŵi iyo inali makamaka kwa ogonana ofanana ziŵalo aamuna ndi kwa omwerekera ndi mankhwala ogodomalitsa amene anayambukiridwa kupyolera mwa nsingano zoipitsidwa. Koma kufalikira kwake pakati pa akazi kwakhala kofulumira. World Health, magazini a WHO (World Health Organization), anasimba motere m’kope lake la November-December 1990: “Chiŵerengero cha akazi [padziko lonse] oyembekezeredwa kudwala nthenda ya AIDS m’zaka ziŵiri zirikubwera chidzapambana chiwonkhetso chonse cha odwala nthenda ya AIDS chochitiridwa lipoti ku WHO mkati mwa zaka khumi zoyambirira za mliriwu.”
Ku United States, Federal Centers for Disease Control inachitira lipoti kuti podzafika chakumapeto kwa 1990, panali anthu 15,696 amsinkhu woposa zaka 50 amene anakhala ndi zizindikiro za AIDS. Chimenecho nchiŵerengero chachikulu poyerekezera ndi ana 2,686 amsinkhu wochepera pa zaka 13 odwala nthenda ya AIDS, gulu la minkhole ya AIDS limene lafalitsidwa koposa.
Kodi ndimotani mmene achikulire amatengera nthenda ya AIDS? Ambiri amatero chifukwa cha machitachita a kugonana kwa ofanana ziŵalo. Komabe, mogwirizana ndi The New York Times, “pafupifupi 17 peresenti ya minkhole anayambukiridwa ndi kachiromboko kupyolera m’kuthiridwa mwazi woipitsidwa.” Chimenecho ndipafupifupi chiŵerengero chimodzimodzicho cha odwala AIDS pakati pa achikulire chifukwa chothiridwa mwazi monga chiwonkhetso cha odwala nthenda ya AIDS pakati pa ana a zaka zochepera pa 13!