Kuyamba Mwamsanga Kuli Kofunika
ANA ACHICHEPERE ayenera kupatsidwa malongosoledwe okwanira a mmene mathupi awo amagwirira ntchito ndi mmene angadzichinjizirire kwa anthu amakhalidwe oipa. Koma kodi malangizowo ayenera kuyamba liti? Mwamsanga kuposa ndi mmene ambiri amaganizira.
Nyengo yakuyamba kukhwima imayambira paunamwali, msinkhu umene zizindikiro za kukula m’zakugonana zimayamba kuwonekera. Msungwana angayambe kusamba pamsinkhu wazaka 10 kapena ngakhale asanafikepo kapena pazaka 16 kapena pambuyo pake. Mnyamata angayambe kutulutsa ubwamuna kutulo pamsinkhu wazaka 11 kapena 12. Kodi ana anu adzakhala akudziŵa zimenezo panthaŵiyo, tinene kuti pamsinkhu wazaka zisanu ndi zinayi?a Kodi iwo adzadziŵanso pausinkhu waung’ono umenewo kufunika kwa kusunga chinamwali chawo?
Azoloŵetseni ndi Masithidwe Athupi
Mwana wanu wamkazi ali nako kuyenerera kwakudziŵa masinthidwe operekedwa ndi Mulungu amene adzachitika kuthupi lake. Amayi angamuuze za kusamba kwawo ndi kusonyeza mwanayo zimene iwo amagwiritsira ntchito kuchinjiriza mwaziwo. Ayenera kufotokoza kuti masinthidwe ameneŵa ali zochitika za thupi zachibadwa. M’njira yotsimikizira kwambiri, amayi akhoza kufotokoza kuti thupi lamwanayo lidzakhala likukonzekera, kwa zaka zakutizakuti kuchokera tsopano, pamene angadzakwatiwe ndi kukhala amayi nayenso. Amayi akhoza kulongosolera mwana wawo wamkazi kuti thupi limakonzera mwana m’mimba ganda lapadera lofeŵa, lokhala ndi mitsemba yambiri yamwazi. Ngati mimba yamwana sinakhale, gandalo limachoka ndi kutulukira pa mpheto yachikazi, ndipo kachitidwe kameneka kamatchedwa kusamba.
Mofananamo, mwana wanu wamwamuna ayenera kudziŵiratu ponena za kutulutsa ubwamuna kutulo. (Deuteronomo 23:10, 11) Iye ayenera kumvetsetsa kuti kutulutsa madzi otelera, nthaŵi zina pamene akulota, kuli chabe njira yathupi yotaila ubwamuna wochulukitsitsa m’thupi. Ponse paŵiri ana anu aamuna ndi aakazi ayenera kudziŵa kuti palibe cholakwa ndi masinthidwe ameneŵa ochitika m’mathupi awo. Mathupi awo akungodzikonzekeretsa ukwati umene ungakhaleko mtsogolo ndi ukholo.b
Monga makolo, muyenera kuwona nkhani zimenezi mwamphamvu, popeza kuti ndinkhani zaumulungu. Ndipo ndinu aphunzitsi amene Mulungu waika.
Kodi Kugonana Kotetezereka Nkotani?
Pamene zaka zikufulumira ndipo achichepere anu akuloŵa muunyamata wawo, muyenera kutsimikizira kuti iwo akudziŵa kuti kugonana kwa anthu osakwatirana nkwaupandu, mosasamala kanthu ndi zosiyana zimene angakhale anazimva. Matenda opatsirana mwakugonana, kuphatikizapo AIDS, akhala mliri wadziko lonse. Matenda oterowo angapangitse munthu kuleka kubala, kubala mwana wopunduka, kansa, ndipo ngakhale imfa. Ndiponso, matendawo angapatsiridwe ndi anthu amene sakudziŵa kuti ali nawo.
Ana anu ayenera kudziŵa kuti palibe njira yochinjiriza iriyonse imene yatsimikizira kukhala yodalirika kotheratu kaya m’kuletsa kutenga mimba kapena matenda. Kwenikweni, chiŵerengero chachikulu kwambiri cha achichepere amene amagwiritsira ntchito njira zochinjiriza zosiyanasiyana amatenga mimba. Ndipo ngakhale kuti makondomu (condom) amalengezedwa kukhala otetezera kutenga matenda a AIDS pogonana ndi wowadwala, The New England Journal of Medicine inanena kuti makondomu amalephera kuchinjiriza kachirombo ka AIDS paukulu wa 17 peresenti panthaŵiyo.
Chotero, wolemba nkhani m’magazini a New York Post Ray Kerrison anatsutsa kunena kwakuti makondomu ‘amachepetsa upandu wakutenga AIDS’ pamene analemba kuti: “Kuchepetsa! Ngati musopera chipolopolo m’mfuti, ndiyeno nkumaiseŵeretsa mwakumaizunguza ndi kudziloza nayo, mudzakhala ndi mpata umodzi mwa isanu ndi umodzi wakudzipha nokha. Ponena za kondomu, mumakhala ndi mpata umodzi mwa isanu wakutenga AIDS. Tsopano tikhoza kutcha kondomu ndi dzina lake lenileni lakuti bodza la AIDS. Ndiyo mfuti yakugonana.”
Ana anu ayenera kudziŵa kuti mankhwala a vuto la matenda akupatsirana mwakugonana ngosavuta. Ndiwo kutsatira makonzedwe a Mulungu akugwiritsira ntchito mphatso yaumulungu yakubalana. Ndithudi, kugonana kotetezereka kuli muukwati, umodzi wa moyo wonse ndi munthu mmodzi yekha wokondana naye amene nayenso sakhala ndi ogonana nawo ena.
Malangizo a Mulungu ndiwo Chitetezo
Baibulo limanena kuti: “Mwamuna . . . adzadziphatika kwa mkazi wake.” ‘Usachite chigololo.’ ‘Koma dama . . . lisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu.’ ‘Wadama yense . . . alibe choloŵa muufumu wa Kristu ndi Mulungu.’—Genesis 2:24; Mateyu 5:27; Aefeso 5:3, 5.
Malangizo ameneŵa sali otsendereza. Mmalomwake, kuwatsatira kudzapangitsa banja kukhala lachimwemwe ndi logwirizana mwathithithi. Mwana woyembekezeredwa kubadwa adzapatsidwa kanthu kena komwe akukayenerera—makolo aŵiri, amayi ndi atate. Aliyense wa iwo ali ndi mikhalidwe yosiyana, ndipo aliyense angathandizire ku moyo wa mwana zinthu zimene winayo alibe.
Monga makolo, ponse paŵiri mwakuphunzitsa kwanu ndi chitsanzo chimene muchipereka, muyenera kukhomereza zolimba mumtima ndi maganizo a mwana wanu malamulo amakhalidwe abwino ozikidwa pa Baibulo. Muyenera kumanga ndi milimo yolimba—yosagwira moto. Monga momwe Baibulo limanenera kuti: ‘Ntchito ya yense idzawonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, chifukwa kuti yavumbuluka m’moto; ndipo moto wokha udzayesera ntchito ya yense ikhala yotani.’ Ngati mumanga zolimba ndipo ntchito yanu siwonongeka, mudzadalitsidwa molemera.—1 Akorinto 3:13.
Koma funso lofunika kwambiri ndi ili: Kodi mungasungitse motani kuphunzitsa kumeneku pamene ana anu akupyola m’zaka zawo zaunyamata kulinga ku uchikulire?
[Mawu a M’munsi]
a Dr. Leon Rosenberg wa pa Yunivesiti ya Johns Hopkins, Baltimore, Maryland, ku U.S.A., anati: “Pamene mwana afika zaka 9, makolo ayenera kuti anayamba kukhala naye pansi ndi kukambitsirana kwa tsatanetsatane ponena za zinthu zakugonana ndi makhalidwe. Pamene ana apeza chidziŵitso chochuluka kwa makolo awo mpamenenso amakhala abwinopo.”
b Mungapeze chidziŵitso chowonjezereka m’mitu yakuti “Growing Into Manhood” ndi “Moving Into Womanhood” m’bukhu lakuti Your Youth—Getting the Best Out Of It, limene mukhoza kulipeza kwa ofalitsa magazini ano.
[Chithunzi patsamba 8]
Kukonzekeretsa ana anu masinthidwe athupi nkofunika kwambiri