Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 7/8 tsamba 27-29
  • Perekani Chitsogozo Chomwe Afunikira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Perekani Chitsogozo Chomwe Afunikira
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chiyambukiro cha Chitsanzo
  • Kumvetsera Kwatanthauzo
  • Machenjezo Ofunika
  • Malangizo Amene Iwo Afunikira Mwapadera
  • Kuyamba Mwamsanga Kuli Kofunika
    Galamukani!—1992
  • Makolo Tetezerani Ana Anu!
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Baibulo ndi Makhalidwe Abwino a Achichepere
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi Ndani Amawaphunzitsa Nkhani za Kugonana?
    Galamukani!—1992
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 7/8 tsamba 27-29

Perekani Chitsogozo Chomwe Afunikira

KODI ana anu angaphunzire motani kudzitetezera kumakhalidwe achisembwere chowonjezerekawonjezereka chadziko? Osati mwawailesi yakanema, imene kagulu kamodzi ka achichepere kanatchula kukhala magwero achinayi ofunika koposa opereka chidziŵitso chonena za kugonana. Osati kumasukulu, kumene zimene aphunzitsi amaphunzitsa zimasonyeza kusintha kwamakhalidwe ndi miyezo ya dziko lachisembwere lino. Ndipo ndithudi osati m’nkhani zosimbidwa ndi anzawo a kusukulu a ana anu.

Ngati maphunziro m’zamakhalidwe abwino ndi moyo wabanja ati akhale achipambano, ayenera kuyambira m’banja. Monga momwe mphunzitsi wa sukulu yasekondale wodera nkhawa ananenera kuti: “Munthu wina ayenera kukhala ndi kulimba mtima kwa kunena kuti: ‘Tawonani, ananu, sikudzakuvulazani kuyembekezera!’”

Kodi mwaphunzitsa ana anu zimenezo? Polingalira za mpwechepweche wa nkhani za kugonana zotizungulira, kodi inu nthaŵi zina mumadabwa ngati mumadziŵadi mmene mungawaphunzitsire?

Chiyambukiro cha Chitsanzo

Monga momwe makolo anu anayambukira moyo wanu mwa njira imene anakhalira ndi moyo, chotero chitsanzo chanu chimayambukira mwamphamvu miyoyo ya ana anu. Chimavumbula zambiri ponena za mlingo wa chikondi chanu pa iwo ndi mtundu wa anthu umene mufuna kuti adzakhale.

Ngati munali namwali wosadziŵa mwamuna pamene munakwatibwa, mungachite kuti ana anu adziwe mmene zimenezo zinakusangalatsirani. Gogo wina wachimuna akukumbukira tsiku, pafupifupi zaka 60 zapitazo, pamene atate wawo anawauza za mmene anasangalalira kukwatira, akumadziŵa kuti anali asanaphatikizidwe m’kudzisungira kulikonse kwachisembwere kumene kukaipitsa ukwati wawo. Makambitsirano amenewo anasonkhezera kwambiri njira imene agogo amenewa anakhalira ndi moyo, ndipo amakhulupirira kuti chitsanzo chawo chayambukira mwamphamvu kwambiri miyoyo ya ana awo.

Komabe, ngati ana anu akudziŵa kuti moyo wanu woyambirira sunali wachitsanzo chabwino, muyenera kutsimikizira kuti iwo akudziŵa chifukwa chimene munasinthira. Sikuli kokha chifukwa chakuti mwakula koma kuti mwapeza mpambo wa miyezo yapamwamba yokhalira moyo.

Kumvetsera Kwatanthauzo

Makolo achipambano kaŵirikaŵiri amatchula za kuchuluka kwa nthaŵi imene amathera kumvetsera ana awo. Iwo amadziŵa chimene chikuchitika m’miyoyo ya ana awo. Karen anapanga kuyesayesa kwa kugwira ntchito m’khitcheni masana. Mwanjira imeneyi, pamene ana ake aakazi anadza panyumba, iwo akanatha kumuuza zimene zinachitika kusukulu mkati mwatsikulo.

Erline ankakonda kuyembekezera ana ake aakazi pamene anadza panyumba madzulo ndi kumvetsera kwa iwo akufotokoza zonse zimene anali atachita. “Ngati kanthu kena kanafunikira kuwongolera,” iye akutero, “ndinkatero pambuyo pake. Koma sindikanadziŵa konse ngati sindinamvetsere.” Anasungabe kulankhuliranaku kuli kotseguka mkati mwa zaka zonse zopita kusukulu za ana ake aakazi ndi mkati mwa nthaŵi yonse ya kutomeredwa. Nthaŵi yotero imene mumathera muli ndi ana anu ingapewetse mavuto ambiri pambuyo pake.

Koma bwanji ngati ana anu ali osalankhulalankhula? Ngati iwo samatero, mungadzifunse kuti, ‘Kodi iwo ali kokha achete mwachibadwa, kapena kodi akuwopa kundiuza zakukhosi chifukwa cha mmene ndinalabadirira papitapo? Kodi ndingakulitsenso chidaliro chawo mwa kupanga kuyesayesa kwapadera tsopano kusonyeza chikondwerero changa mwa iwo? Kodi ndingakupangitse kukhala kosavutirapo kwa iwo kutulutsa nkhani zazing’ono tsopano ndipo mwinamwake zazikulu koposerapo pambuyo pake?’

Machenjezo Ofunika

Ana anu afunikira kuchenjezedwa za zotulukapo za chisembwere. Mwachitsanzo, iwo ayenera kudziŵa, kuti mosasamala kanthu za zonse zimene amva zosiyana, palibe njira yopewera kutenga mimba imene iri yogwira mtima kwambiri kosakhoza kulephera. Mimba zosafunika ndi matenda opatsirana mwakugonana kaŵirikaŵiri zimakhalapo ngakhale pamene njira zotetezera kutenga mimba zigwiritsiridwa ntchito. Malinga ndi gulu lotchedwa Planned Parenthood, makondomu amalephera kupewetsa mimba 12 peresenti pakali pano, ndipo kulephera kwawo kungakhaledi kokulirapo kupewetsa kuyambukiridwa ndi kachirombo ka AIDS.

Achichepere ambiri amawonekera kukhala okhutiritsidwa maganizo kuti zoipa sizidzawachitikira. Komabe, matenda oyambukiridwa mwakugonana, ophatikizapo AIDS, angatengedwe kwa anthu amene adakalibe zisonyezero ndi amene sakudziŵa kuti akupatsira ena matenda. Ambiri a matenda oterowo amene akukantha achichepere lerolino angachititse kusabala, kubala ana opunduka, kansa, ngakhale imfa.

Mwachitsanzo, nzika za Amereka mamiliyoni 40 tsopano zikukhulupiriridwa kuti ziri ndi imodzi ya matendawa, matudza a kumpheto, amene alibe mankhwala odziŵika. Anakubala ogwidwa nawo angawapatsire kwa ana awo. Ana opanda liwongo amenewa angafikire kukhala opunduka maganizo, kuvulazikiratu kwa dongosolo lawo la minyewa, kapena kufa ndi kuyambukiridwa kwa ziwalo zawo zamkati. Ndimtengo woipa chotani nanga woulipilira kaamba ka mphindi zochepa chabe za chisangalalo choyembekezeredwa!

Kugonana kosaloledwa kumene kunapatsira nthendayi kungakhale kunali kosasangalatsa. Wofufuza wina amene anafunsa achichepere ambiri ananena kuti “kwa akazi, zokumana nazo zakugonana za azaka 13-19 kuwirikiza nthaŵi ziŵiri zinali zosakondweretsa koposa kukhala zokondweretsa.” Makolo ayenera kugogomezera kwa ana awo kuti kugonana—njira yodabwitsa imene Mlengi wathu analinganizira kuti dziko lathu lapansi lokongolali lidzazidwe ndi anthu—sikuyenera kuyambidwa mwakabisira kunja kwa zomangira zaukwati.

Malangizo Amene Iwo Afunikira Mwapadera

Ana anu afunikira kudziŵa kuti njira yotsimikizirika yokha yopewera mavuto amene amadza ndi kugonana kwa ukwati usanachitike ndiyo kutsatira malamulo amakhalidwe abwino otsimikiziridwa kwanthaŵi yaitali amene Mulungu anapereka. Malamulo amakhalidwe ati? A kusagonana kufikira ukwati, ndiyeno kukhulupirika kwanthaŵi zonse ndi kwa moyo wonse kwamunthu wokondedwayo amene, mumkhalidwe wabwino kwambiri, nayenso analibe mnzake wogonana naye.

Komabe, chifukwa chachikulu chothaŵira chisembwere sindicho chakuti chimapangitsa mavuto koma kuti Mlengi wathu amanena kuti ncholakwa. Baibulo limalimbikitsa kuti: “Mudzipatule kudama.” “Thawani dama.” Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti, awo amene akupitirizabe kuchita zinthu zimenezi “sadzalandira ufumu wa Mulungu.”—1 Atesalonika 4:3; 1 Akorinto 6:9, 10, 18.

Kutsatira malamulo amakhalidwe abwino aumulungu kumatsogolera kukukhala ndi miyoyo yachimwemwe kwambiri, yokhutiritsidwa kwambiri. Kumatitetezera kumatenda opatsirana mwakugonana, mimba zosafunika, mavuto a mabanja akholo limodzi, ndi kupwetekedwa mtima kochititsidwa ndi kusiyidwa ndi anthu amene mwadyera anatigwiritsira ntchito kaamba ka zifuno zawo zakugonana.

Kwazaka zoposa 2,500, mawu olembedwa ndi mneneri wa Mulungu wa m’nthaŵi zakale atsimikizira kukhala owona akuti: “Ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga! Mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.”—Yesaya 48:17, 18.

Koma kodi ndimotani mmene malamulo amakhalidwe abwino amenewa angagwirizanire ndi machitidwe amakono a kuyenda ndi msungwana kapena mnyamata? Funso limenelo lidzapendedwa tsopano.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena