Zotulukapo Zoŵaŵa za Kutchova Juga
Bobby anapezedwa wakufa m’galimoto pamsewu wakumpoto kwa London. Anadzipha ali ndi zaka 23 zokha.
Mwamuna wina wachikulire anagona m’makwalala kwa masiku angapo asanapite kumalo othandiza anthu osauka. Anali wofooka kwambiri, pakuti sanadye kalikonse kwa masiku anayi, ndipo sanamwe mankhwala omwe anauzidwa othandiza mtima.
Emilio, tate wa ana asanu, anasweka mtima. Mkazi wake ndi ana adamthaŵa. Tsopano iwo sanafune ngakhale kulankhula naye.
WODZIPHA, wosoŵa kokhala, ndi atate wonyanyalidwa: ndinkhani zitatu zomvetsa chisoni, zomwe mwachiwonekere ziri zosiyana koma zofala m’chitaganya chathu chamakono. Koma masokawo anachititsidwa ndi chinthu chimodzi—kumwerekera m’kutchova juga.
Otchova juga omwerekera ambiri amakana kuvomereza kuti ali ndi vuto, ndipo kaŵirikaŵiri ziŵalo za banja zimabisa nkhaniyo kuwopa kusekedwa ndi anthu. Koma tsiku lirilonse mabanja mamiliyoni ambiri kuzungulira dziko lonse amavutika ndipo amasoŵa chochita chifukwa cha kumwerekera kosakaza kumeneko.
Palibe yemwe adziŵa unyinji wa otchova juga omwerekera omwe alipo. Ku United States, mamiliyoni khumi akulingaliridwa kukhala chiŵerengero chochepa chongoyerekezera. Ziŵerengerozo nzazikulu ndipo zikuwonjezereka kulikonse pamene mipata yakutchova juga ikuchulukirachulukira m’maiko osiyanasiyana. Kutchova juga kosalekeza kwanenedwa kukhala “kumwerekera kokula mofulumira.”
Ambiri a omwerekera atsopano anayamba monga otchova juga wamba amene anangofuna “kuyesa mwaŵi wawo kuwona ngati angapambane.” Ndiyeno analoŵa m’vuto lakumwerekera m’kutchova juga.
Pamene Kutchova Juga Kukhala Kosalamulirika
Kodi nchiyani chimasintha otchova juga wamba kukhala omwerekera? Zochititsa zimakhala zosiyanasiyana, koma mwanjira yakutiyakuti, otchova juga amafikira mlingo wina m’moyo wawo pamene amaganiza kuti sikothekanso kwa iwo kuleka kutchova juga. (Onani bokosi patsamba 7.) Ena amapeza kuti m’kutchova juga muli chisangalalo chomwe miyoyo yawo imachisoŵa. Wotchova juga wina anafotokoza kuti: “Ziribe kanthu kwa ine kaya ndipambane kapena ndilephere. Pobetcha, makamaka nditabetcha koposa enawo, ndimadziwona kukhala munthu wopambana m’dziko. Anthu amandilemekeza. Ndimasangalala ndithu!”
Ena amayamba kutchova juga chifukwa chosungulumwa kapena kuchita tondovi. Ester, mayi wa ana anayi, anali wokwatiwa kwa msirikali yemwe nthaŵi zambiri sankapezeka panyumba. Mkaziyo anasungulumwa chotero anayamba kuseŵera makina otchovera juga m’makonde oseŵerera. Posapita nthaŵi anayamba kuseŵera kwa maola angapo tsiku lirilonse. Ndalama zogulira zinthu zinatha mwamsanga, ndipo mavuto anachuluka. Anayesayesa kusauza mwamuna wake za ndalama zowonongedwa kwinaku akumabwereka ndalama kumabanki kapena kwa anthu ena kuti akhutiritse kumwerekera kwake kofuna madola 200 patsiku.
Palinso anthu amene anakhala omwerekera chifukwa chopambana kwambiri. Robert Custer, katswiri wa za kutchova juga kosalekeza, akufotoza kuti: “Kaŵirikaŵiri amene amayambirira kupambana mobwerezabwereza m’kutchova juga amakhala omwerekera.” Ndiyeno, chikhumbo chakupambanabe chimakula mosalamulirika.
Msampha wa Kukhulupirira Malaulo
Otchova juga ambiri amatengeka ndi chikhumbo chobukapo mmalo mwa kugwiritsira ntchito luntha. Kupenda kokhweka kungaletse munthu kukhala wotchova juga ngati amagwiritsira nzeru zake bwino. Mwachitsanzo, ku United States, kuthekera kwa kuphedwa ndi mphezi kuli pafupifupi 1 mu 1,700,000. Kupambana m’lotale ya Boma nkwapatali moti nkuŵirikiza kaŵiri chiŵerengerocho.
Kodi ndani angayembekezere kukanthidwa ndi mphezi? Kokha munthu wamantha kwambiri. Komabe, pafupifupi aliyense yemwe amagula tikiti la lotale amalota kuti nambala yake idzapambana. Zowona, chiyembekezo cha kupambana lotale chimapatsa chimwemwe chachikulu, koma kukhulupirira malaulo ndiko kumasonkhezera anthu kukhala ndi chiyembekezo m’zinthu zosatheka kwenikweni. Kusankha kwawo “manambala amwaŵi” apamtima kumawakhutiritsa kuti akhoza kupambana ngakhale kuti mwaŵiwo ngwapatali kwambiri.—Onani bokosi patsamba 8.
Claudio Alsina, katswiri wamasamu Wachispanya, ananena kuti ngati nyumba zotchovera juga ndi malotale zinati zigwiritsire ntchito zilembo za alufabeti mmalo mwa manambala m’maseŵera amwaŵi, kuthekera kwa kupambana sikukanasintha konse, koma sakanakhala okopa kwambiri—ndipo mwachiwonekere ndalama zolandiridwa ndi obetcha—zikanachepekera. Chidwi chomwe manambala ena amadzetsa nchodabwitsa. Ena amakonda nambala 9, 7, 6 ndi 0, pamene ena amasankha “nambala zamwaŵi” pa zinthu zonga tsiku lakubadwa kapena padanga lakupenda nyenyezi. Ndipo pali ena amene amatsogozedwa ndi chochitika chachilendo.
Tsiku lina mwamuna wina anawona zodabwitsa ndithu pamene anafika pafupi ndi nyumba yotchovera juga ya Monte Carlo. Nkhunda yomwe inali kuuluka inagwetsera chitosi pachipewa chake. Tsiku lomwelo anapambana $15,000. Pokhutira kuti chitosi cha nkhunda chinali mwaŵi wake, nthaŵi zonse akabwera kunyumba yotchovera juga sanalikuloŵa popanda kuyendayenda kunja choyamba kuti mwina angalandirenso “mwaŵi wochokera kumwamba.” Motero, kukhulupirira malaulo kumasokeretsa otchova juga ambiri kulingalira kuti nyengo yakupambana simatha konse. Komabe, zimenezi zimakhala ndi msampha woipa wa kumwerekera umene umawalamulira ndi umene potsirizira umawakola.
Chifukwa cha Chikondi cha pa Ndalama
Anthu amatchova juga kuti apambane ndalama, ndipo ndalama zochuluka ndithu ngati kutheka. Koma kwa wotchova juga womwerekera, ndalama zomwe amapambana zimakhala ndi chiyambukiro chinachake. Kwa iye, monga momwe Robert Custer akufotokozera, “ndalama zimampanga kukhala wofunika. . . . Ndalama zimampatsa mabwenzi. . . . Ndalama zimampezera mankhwala.” Ndipo kodi nchifukwa ninji ndalama zimakhala zofunika kwambiri kwa iye?
Mwa otchova juga, ambiri amakhumbira munthu wopambana kwambiri kapena wowononga ndalama zambiri. Amafuna kukhala pafupi naye. Motero, ndalama zimene amapambana zimauza wotchova jugayo kuti ndimunthu wofunika, katswiri weniweni. Ndiponso ndalamazo zimamuiŵalitsa mavuto ake, kumthandiza kupeza mpumulo, ndi kumsangulutsa. Kunena mogwirizana ndi mawu a wofufuza Jay Livingston, otchova juga omwerekera “amadalira pa kutchova juga kuti akhutiritse zosoŵa zawo zamaganizo.” Chimenecho ndicholakwa chodzetsa tsoka.
Pamene mwaŵi wachinyengo utha ndipo munthuyo ayamba kulephera mobwerezabwereza, ndalama zimakhala zofunika koposa. Tsopano mothedwa nzeru amafuna kuyesayesa kubwezeretsa ndalama zowonongedwazo. Kodi angapeze motani ndalama zokwanira kulipira omkongoletsa, kuti apezenso mwaŵi wake wakupambana? Mosataya nthaŵi amasintha nakhala ndi moyo wofunafuna ndalama nthaŵi zonse.
Tsoka lotero liri chochitika chenicheni m’moyo wa otchova juga mamiliyoni ambiri. Iwo amaphatikizapo amuna ndi akazi amisinkhu yonse, ndi amikhalidwe yosiyanasiyana. Ndipo aliyense akhoza kugweramo m’vutolo, monga momwe zasonyezedwera ndi kuwonjezereka kwaposachedwapa kwa kumwerekera ndi kutchova juga mwa achichepere ndi akazi okwatiwa.
Achichepere ndi Akazi Okwatiwa Omwerekera
Achichepere ndimikole yosavuta ya makina otchovera juga okopawo kapena maseŵera ena amwaŵi omwe amaŵapatsa chiyembekezo chopeza ndalama mofulumira. Kufufuza kochitidwa mumzinda wina ku Mangalande kunasonyeza kuti achichepere 4 mwa 5 azaka 14 anaseŵera makina otchovera juga mokhazikika ndi kuti ambiri anayamba ali ndi zaka 9. Ena anali kulova kusukulu kuti adzitchova juga. Kufufuza kochitidwa pa ana asukulu ya sekondale ku United States kunasonyeza kuti okwanira 6 peresenti “anasonyeza zizindikiro zothekera za kutchova juga kosakaza ndi kosalekeza.”
Manuel Melgarejo, mkulu wa gulu lothandiza lopangidwa ndi omwe kale anali otchova juga ku Madrid, Spanya, anafotokozera mlembi wa Galamukani! kuti wachichepere wokopeka mosavuta angamwerekere mwakungopambana jakipoti yaikulu imodzi pa makina otchovera juga. Mwamsanga, kutchova juga kumakhala kocheutsa ndi kosangalatsa. Posapita nthaŵi, wachichepere womwerekerayo angayambe kumagulitsa chuma cha banja kapena kubera banja zinthu, ngakhale kuba tinthu tating’ono kapena kuchita uchiwerewere kuti alipirire kumwerekerako.
Ndiponso akatswiri ochuluka akusonyeza kuwonjezereka kwakukulu kwa ziŵerengero za akazi okwatiwa omwe ali otchova juga omwerekera. Mwachitsanzo, ku United States, akazi tsopano akupanga pafupifupi 30 peresenti ya chiŵerengero chonse cha otchova juga omwerekera, koma kukuyerekezeredwa kuti podzafika chaka cha 2000, chiŵerengerocho chidzakula kukhala 50 peresenti.
María, amayi wogwira ntchito wa ana aakazi aŵiri, ali mmodzi wa akazi okwatiwa ochuluka omwe akhala otchova juga omwerekera. M’zaka zisanu ndi ziŵiri zapita, wathera ndalama zokwanira $35,000—kwenikweni ndalama zapanyumba—m’kuseŵera bingo ndi makina otchovera juga. “Ndalamazo zinapitiratu,” akudandaula tero. “Ndimangolakalaka tsiku pamene ndidzaloŵa m’kefi ndi $50 m’chikwama ndi kugulira ana anga zinthu [mmalo moiponya m’makina otchovera juga].”
Maloto Osanunkha Kanthu
Kutchova juga nkozikidwa pamaloto. Kwa otchova juga ena, maloto akulemera ngakanthaŵi, koma kwa omwerekera, malotowo amakhala chonulirapo chawo chomwe amachilondola mosalekeza, mpaka kuloŵa nacho muumphaŵi, m’ndende, ndipo ngakhale mu imfa.
Zowona, kutchova juga kumalonjeza kukhutiritsa zosoŵa zenizeni—kutaya nthaŵi koyenera, kusanguluka pang’ono, ndalama zowonjezereka, kapena kupeza mpumulo ku nkhaŵa za tsiku ndi tsiku—koma zotulukapo zobisika zingakhale zowopsa, monga momwe otchova juga omwerekera azindikirira momvetsa chisoni. Kodi zosoŵa zimenezo zingakhutiritsidwe ndi kanthu kena kosiyana?
[Bokosi patsamba 7]
Chithunzi cha Wotchova Juga Womwerekera
WOMWEREKERA amapitirizabe kutchova juga mosasamala kanthu ndi zimene amataya. Ndipo atapambana, amagwiritsira ntchito ndalamazo kupitiriza kutchova juga. Ngakhale anene kuti akhoza kuleka nthaŵi iriyonse imene afuna, wotchova juga womwerekera yemwe ali ndi ndalama m’thumba sangakhale masiku ambiri popanda kubetcha kanthu kena. Amakhala ndi chisonkhezero champhamvu cha kutchova juga.
Iye amadziloŵetsa m’ngongole nthaŵi zonse. Atalephera kubwezera omkongoletsa, amakongola ndalama zowonjezereka zolipirira ngongole zofunika kubweza mwamsanga ndi zopitirizira kutchova juga. Chotsatira amakhala wosawona mtima. Angatchovere juga ngakhale ndalama za womlemba ntchito. Kaŵirikaŵiri, amafikira pakuchotsedwa ntchito.
Kalikonse, ngakhale mkazi wake ndi ana omwe, samakhala ofunika mofanana ndi kutchova juga. Kumwerekera kwake kosalamulirikako kumanyonyotsola ukwati ndipo potsirizira pake kungachititse kulekana kapena chisudzulo.
Liŵongo lake lalikululo limampangitsa kungosunga zinthu mumtima. Amakupeza kukhala kovuta kuuzako anthu ena. Potsirizira pake, amachita tondovi kwambiri ndipo ngakhale kuyesadi kudzipha; samawona njira iriyonse yotulukira m’kupanikizika kwake.
[Bokosi patsamba 8]
Mwamuna Yemwe Anapambana Juga Modabwitsa ku Monte Carlo
CHARLES WELLS, Mngelezi, anapita kunyumba yotchovera juga ya Monte Carlo m’July 1891. M’masiku ochepa okha, anasanduliza ndalama za franc zikwi khumi kukhala miliyoni imodzi mwakutchova juga, ndipo modabwitsa, anabwereza ukatswiri wake patapita miyezi inayi. Otchova juga ena anayesa mosaphula kanthu kutulukira “njira [yake] yopezera ndalama.” Nthaŵi zonse Wells anakana kuti analibe njira iriyonse. Ndipotu, chaka chotsatira anataya ndalama zake zonse, ndipo anafa wopanda ndi khobiri yomwe. Mosiyana, chochitikacho chinachititsa nyumba yotchovera jugayo kukhala yotchuka. Yakhalabe yotchuka padziko lonse kufikira leroli.
Chinyengo cha Monte Carlo
Otchova juga ambiri amakhulupirira kuti zipangizo zotchovera juga za slot machine kapena roulette wheel zimatha kukumbukira. Chifukwa chake, woseŵera roulette amalingalira kuti ngati mpambo wakutiwakuti wa manambala watuluka, pali kuthekera kwakuti mbale yamanambalawo idzapitirizabe kusonyeza manambala omwe alingana ndi mpambowo. Mofananamo, ena omwe amaseŵera ma slot machine amalingalira kuti ngati jakipoti sinatengedwe kwa nthaŵi yakutiyakuti pamakina ena, iripafupi kutengedwa. Malingaliro olakwika otero amatchedwa chinyengo cha Monte Carlo.
Roulette wheel ndi njira yomwe slot machine imatulutsira jakipoti zimangogwira ntchito mwamwaŵi. Chifukwa chake, zimene zinachitika poyamba ziri zosatheka. M’maseŵera ameneŵa amwaŵi, monga momwe The New Encyclopædia Britannica ikunenera, “kuseŵera kulikonse kuli ndi kuthekera kofanana ndi kumene kuseŵera kwina kumakhala nako kwa kupereka zotulukapo.” Choncho mwaŵi wakupambana nthaŵi zonse umakhala wochepa mofananamo. Komabe, chinyengo cha Monte Carlo chawononga otchova juga ambiri pamene kuli kwakuti chalemeretsa eninyumba zotchovera juga.