Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 8/8 tsamba 21
  • Imfa Mliri Wadziko Lonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Imfa Mliri Wadziko Lonse
  • Galamukani!—1992
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Pali Chiyembekezo chotani cha Moyo Wotalikirapo?
    Galamukani!—1995
  • N’chifukwa Chiyani Timaopa Imfa?
    Galamukani!—2007
  • Kodi Munthu Akamwalira Amapita Kuti?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Okondedwa Akufa?
    Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Okondedwa Akufa?
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 8/8 tsamba 21

Imfa Mliri Wadziko Lonse

CHAKA ndi chaka anthu pafupifupi 50 miliyoni amafa padziko lonse. Zimenezo zimatanthauza anthu 137,000 patsiku, 5,700 paola, pafupifupi 100 pamphindi, kapena oposa anthu atatu patimphindi tiŵiri tiritonse. Palibe banja limene limasiyidwa ndi mliri wa imfa. Mfumu kapena munthu wamba, wachuma kapena wosauka, mwamuna kapena mkazi—onse amafa mofanana.

“M’dziko lino lapansi palibe chinthu chotsimikizirika monga imfa ndi misonkho,” analembera bwenzi lake motero wofalitsa nkhani wotchuka wa ku Amereka mu 1789, amene analinso wotulukira zinthu ndi nthumwi yaboma Benjamin Franklin. Komabe, lingaliro lake silinali lachilendo. Pafupifupi zaka 2,800 zapitazo, Solomo Mfumu yanzeru ya mtundu wakale wa Israyeli anati: “Amoyo adziŵa kuti tidzafa.” Komabe, iye anangotsimikizira zimene zinanenedwa zaka zokwanira 3,000 kalero kwa munthu woyamba padziko lapansi: “Chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.”—Mlaliki 9:5; Genesis 3:19.

Monga momwe imfa yakhalira yosapeŵeka m’mbiri yonse ya anthu, idakali magwero achisoni chachikulu. Kwanenedwa molondola kuti chikhumbo chathu chachibadwa ndicho kukhala ndi moyo, osati kufa. Maunansi amene tiri nawo ndi banja ndi mabwenzi ali zomangira zolimba zimene zimafuna kupitirizabe. Koma mmodzi ndi mmodzi, mkupita kwa zaka, maunansiŵa amaswedwa ndi imfa. Agogo athu, makolo athu, ndi mabwenzi amafa.

“Maumboni ali akuti ofikitsa zaka zana ali moyobe amene amapitirira chaka chawo chakubadwa cha 113 ali ochepa kwambiri ndipo malire otsimikizirika kotheratu autali wa moyo wamunthu walerolino samalola aliyense kuwona chaka chakubadwa chirichonse pambuyo pa chaka chake cha 120,” ikutero Guinness Book of World Records. Motero, palibe munthu amene ali ndi moyo lerolino amene anawona kubadwa kwa Winston Churchill (1874) kapena kwa Mohandas Gandhi (1869), kugulitsidwa kwa Alaska kwa United States kochitidwa ndi Russia mu 1867, kapena kuphedwa kwambanda kwa Abraham Lincoln mu 1865—kuphatikizapo zochitika zonse za m’mbiri zimene zinatsogolera izi za m’zaka za zana la 19.

Kwenikweni, mosasamala kanthu za zipambano zamakono m’zamankhwala ndi sayansi, utali wa moyo wa munthu udakali uja wotchulidwa ndi mwamuna wamakedzana Mose: “Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi aŵiri, kapena tikhala nayo mphamvudi zaka makumi asanu ndi atatu; Koma teronso kukula kwawo kumati chivuto ndi chopanda pake; Pakuti kumapitako msanga ndipo tithaŵa ife tomwe.” (Salmo 90:10) Kumeneku kunali kunena kwachisawawa. Mose iyemwini anakhala ndi moyo kwa zaka 120.

Monga momwe moyo ungakhalire wovuta, kufedwa kumadzetsa kupweteka mtima ndi chisoni chapadera. Kaŵirikaŵiri kumayambukira moipa kwambiri thanzi la otsalawo ndipo kwadziŵikanso kukhala kochititsa matenda ndi imfa. Mosasamala kanthu kuti ndi chiŵalo chiti cha banja chimene chamwalira, pamakhala lingaliro lakutaikiridwa kwakukulu. Monga momwe katswiri wina wa matenda amaganizo ananenera, “kholo lako likamwalira, wataya mbiri yako yakumbuyo. Mwana wako akamwalira, wataya mtsogolo mwako.” Chisoni ndi kupsinjika mtima zimene zimatsatirapo zingakhale zosaneneka. Kufedwa kaŵirikaŵiri kumadzetsa mavuto akulu azachuma, kuchititsa mkhalidwewo kuipirapo. Chitsenderezo chakuti mutsatire machitachita ena apamaliro ndi miyambo zingawonjezere chisoni.

Komabe, kodi pali njira iriyonse imene tingachepetsere kupsinjika maganizo ndi mavuto zimene zimatigwera pamene wokondedwa afa?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena