Otsimikizira Kuthandiza Ana
DZULO ana 40,000 ausinkhu wosafikira zaka zisanu anafa m’maiko osatukuka. Ena 40,000 adzafa lero. Enanso 40,000 maŵa. Zambiri za imfa zimenezi zikanapewedwa.
Kwazaka zambiri mkhalidwe umenewu watchedwa kuti “mkhalidwe wamwamsanga wakachetechete” kapena “tsoka lakachetechete,” kutanthauza kuti wakhala wosadziŵika kwambiri ndi dziko. “Ngati akadzidzi amaŵangamaŵanga 40,000 anali nkufa tsiku lirilonse, pakanakhala mkwiyo. Koma ana 40,000 alinkufa, ndipo sizimadziŵika nkomwe,” anadandaula motero Peter Teeley, wolankhulira United States pa Msonkhano wa Ana wa Dziko Lonse Wochitidwira Kumalikulu a UN ku New York mu 1990.
Ena angalingalire kuti, msonkhanowo, m’kupita kwanthaŵi ungasinthe zonsezo. Nduna zamaboma, kuphatikizapo atsogoleri a Maiko 71, anafikapo kuchokera m’maiko 159. Onse pamodzi anaimira 99 peresenti ya chiŵerengero cha anthu cha padziko. Mkhalidwewo unafotokozedwa mwachidule ndi Mikhail Gorbachev, amene anati: “Mtundu wa anthu sunganyalanyazenso chenicheni chakuti mamiliyoni ambiri a ana amafa chaka chirichonse.”
M’masiku a msonkhanowo usanachitike, dziko linasonyeza chichirikizo chake. Misonkhano ya m’maiko ndi m’zitaganya mazana ambiri, maseminale, maprogramu othetsera vutolo, ndi makambitsirano zinasumikidwa pa vuto la ana. Anthu oposa miliyoni imodzi m’maiko 80 anayatsa makandulo kusonyeza chiyembekezo chawo chakuti mosasamala kanthu za mavuto ndi masoka amtsogolo, dziko lingapangidwe kukhala malo abwinopo.
Tsiku lotsiriza la msonkhanowo linatamandidwa ndi UNICEF (United Nations Children’s Fund) kukhala “mwinamwake tsiku la ana lofunika koposa kuzungulira dziko lonse.” Kodi nchifukwa ninji kutenthedwa maganizo konseku? Chifukwa chakuti atsogoleri adziko anali atavomereza “Makonzedwe a Kuchitapo Kanthu” otsimikizirika a kuchepetsa kuvutika ndi imfa za achichepere kuzungulira padziko lonse lapansi.
Ndithudi, mbiri yakale ya misonkhano ya atsogoleri aboma njodzaza ndi malonjezo oswedwa. Komabe, ambiri anawona lingaliro latsopano la kuwona mtima ndi kugwirizanika monga chotulukapo cha kutha kwa Nkhondo Yapakamwa. James Grant, dairekitala wa UNICEF, mwachidwi anafotokoza kuti: “Atsogoleri a Maiko ndi Maboma, kwenikweni, anatenga sitepe loyamba kulinga kukuyambitsa mkhalidwe wabwino wa anthu onse—wa ‘ana osinkhuka’ ndi wa aang’ono—monga cholinga chachikulu cha chitukuko m’dongosolo la dziko latsopano.”
Ndithudi, mkati mwa chaka chimodzi pambuyo pa msonkhanowo, mitundu yochulukitsitsa inali italinganiza kale makonzedwe a mafukowo a kugwiritsira ntchito zitsimikizo za msonkhanowo. Zimenezi zinasonkhezera Dairekitala Grant kunena kuti: “Tsopano tikuwona chiyembekezo chotsimikizirika chenichenicho chakuti umoyo kaamba ka ana onse chidzakwaniritsidwa podzafika m’chaka cha 2000.”
Koma kodi kwenikweni ndimkhalidwe wa ana wotani, chinsinsi cha banja chomvetsa chisoni cha dziko, umene wavumbulidwa ndi zoulutsira mawu za m’mitundu yonse? Kodi tsopano pali chifukwa chokhulupiririra kuti, mumkhalidwe wa pambuyo pa Nkhondo Yapakamwa wa kugwirizanika kwa maiko, Mitundu Yogwirizana idzayambitsa dongosolo la dziko latsopano labwino kwambiri? Kodi mowonadi tingayembekezere mtsogolo mosangalatsa mwa ana athu? Nkhani zotsatira ziŵiri zidzalingalira mafunso ameneŵa.