Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 4/8 tsamba 3-5
  • Kodi Sayansi Ingakhoze Kuchita ndi Mavuto a m’Zaka za Zana la 21?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Sayansi Ingakhoze Kuchita ndi Mavuto a m’Zaka za Zana la 21?
  • Galamukani!—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mavuto Sakuchepekera
  • Kufunafuna Njira Zochitira Nawo
  • Iyang’anizana ndi Vuto Lake Lalikulu Koposa
  • Sayansi—Kufunafuna Chowonadi kwa Mtundu wa Anthu Komapitirizabe
    Galamukani!—1993
  • Pulaneti Lathu Lokhala Pangozi—Bwanji za Mtsogolo?
    Galamukani!—1996
  • Kodi Anthu Angadzetse Mtendere Wosatha ndi Chisungiko?
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Kodi Posachedwapa Dzikoli Liwonongekeratu?
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 4/8 tsamba 3-5

Kodi Sayansi Ingakhoze Kuchita ndi Mavuto a m’Zaka za Zana la 21?

“Tsopano pali umboni wa sayansi wochuluka wosonyeza kuti Mayi Dziko Lapansi sangathe kupirira kwa nthaŵi yaitali ndi ana ake osaweruzika, ndi osasamala.”—The European, March 19-25, 1992.

AKATSWIRI a zamoyo ndi malo ake okhala akulingalira mowonjezereka kuti kuwopsezedwa kwa dziko lapansi, kumene sikuli kukuza mawu ndi mkamwa, kuli kowopsa ndi kuti kufunikira chisamaliro. Ndipotu, iwo amanena kuti kuchitapo kanthu kwamwamsanga kuli kofunika ngati tsoka liti lipeŵedwe. “Sitili ndi mibadwo,” anatero prezidenti wa Worldwatch Institute kumapeto kwa ma 1980. “Tangotsala ndi zaka, mmene tiyenera kuyesa kusintha zinthu.”

Akonzi a buku lamutu wakuti 5000 Days to Save the Planet analondola kwambiri mu 1990 pamene anafalitsa buku lawo. Kuyambira panthaŵiyo kuŵerengera kwawo masiku otsala kwapitiriza. Nthaŵi yotsala yopulumutsira pulaneti lino, malinga ndi pogomera pamene iwo anaika, tsopano ikuyandikira pafupi ndi muyezo wa masiku 4,000. Ndipo podzafika m’zaka za zana la 21, ngati palibe kanthu kena kozizwitsa kamene kadzachitika pakali pano, nambalayo idzakhala itatsika kukhala masiku pafupifupi 1,500.

Kodi ndimikhalidwe yachilendo yotani imene yachititsa tsoka lowonekeratu limeneli? Kodi ndimavuto otani amene adzakhala m’zaka za zana likudzalo?

Mavuto Sakuchepekera

Anthu okonda mtendere akukondwa chifukwa Nkhondo ya Mawu yatha. Koma vuto la kupeza mtendere wa dziko lonse ndi kuusungitsa nlalikulu ndithu. Prezidenti Mitterrand wa ku Falansa, polankhula mu January 1990 za mavuto a kugwirizanitsa Ulaya, anati: “Tikusiya dziko lopanda chilungamo koma labata, pakuti dziko limene tikuyembekezera lidzakhala lolungama kwambiri, koma mosakaikira silidzakhala labata konse.” Ndipo nyuzipepala ya The European inati: “Zotsatirapo za ufulu [m’maiko amene anali kumbali ya dziko limene kale linali Soviet Union] ndizo kusoŵa bata komawonjezereka, kumene kwawonjezera kuthekera kwa nkhondo yanyukliya, ngakhale kuti kuthekerako kuli kochepa.”

Ndithudi, ena a mavuto amene dziko likuyang’anizana nawo tsopano anali osadziŵika konse pamene Nkhondo ya Mawu inayamba. Kuli monga mmene buku la 5000 Days to Save the Planet likunenera: “Zaka zosakwanira makumi asanu zapitazo malo a dziko anali abwino kwambiri. . . . Dziko linali malo aakulu, okongola ndi olimba; kodi tikanaliwononga motani? Lerolino tikuuzidwa kuti pulaneti lathu lili pangozi, kuti tikuwononga ndi kuipitsa njira yathu kupita ku tsoka la padziko lonse.”

Zotchedwa masoka achilengedwe—zigumula, mikuntho, zivomezi, kuphulika kwa mapiri—zimachitika kulikonse. Kukula kwa thayo limene anthu ali nalo chifukwa chowononga malo a dziko kungakhale kosatsimikizirika. Pali umboni wakuti muyalo wotetezera dziko lapansi wa ozone wakhala wochepa kowopsa m’malo ena. Tsopano, asayansi ena akuchenjeza kuti kusintha kwa mkhalidwe wa mphepo kokhoza kuchititsa masoka kungachitike mwadzidzidzi mmalo mwa kuchitika pang’onopang’ono.

Kansa, nthenda ya mtima, mavuto a kusayenda bwino kwa mwazi, ndi matenda ena ambiri akhala chopinga cha maluso a akatswiri azamankhwala kwa nthaŵi yaitali. Mosasamala kanthu za zaka zochuluka za kupita patsogolo kwa zamankhwala, matenda ameneŵa akali kupha anthu. Mu Ulaya mokha, anthu ongoyerekezera 1,200,000 amafa ndi kansa pachaka, pafupifupi 65 peresenti kuposa zaka khumi zapitazo. Chifukwa cha mantha a mliri watsopano—wa AIDS, umene wapha anthu oŵerengeka poyerekezera ndi kansa—chiŵerengero chachikuluchi cha anthu amene amafa ndi kansa sichimazindikiridwa kwambiri.

Nali vuto lina: M’zaka zosakwanira 200 zapita, chiŵerengero cha anthu cha dziko chakula kuchokera pa anthu mamiliyoni chikwi chimodzi kufika pafupifupi mamiliyoni zikwi zisanu ndi theka. Mosasamala kanthu za kutsika kwaposachedwapa kwa kukula kwa chiŵerengero cha anthu chapachaka, ena amayerekezera kuti podzafika chaka cha 2025, chiŵerengero cha anthu pa dziko mwina chidzakhala chitapyola mamiliyoni zikwi zisanu ndi zitatu, ndipo podzafika 2050 chidzakhala chikuyandikira chiŵerengero cha mamiliyoni zikwi khumi. Kodi anthu onseŵa adzakhala kuti? Kodi adzadya chiyani? Lipoti la Mitundu Yogwirizana loperekedwa mu 1991 linayerekezera kuti anthu mamiliyoni chikwi chimodzi ali kale osauka kwadzawoneni, akumakhala ndi moyo wa “manyutirishoni, kusadziŵa kulemba ndi kuŵerenga ndi matenda kotero kuti angayesedwe kusakhala anthu konse.”

Paul R. Ehrlich, profesa wa maphunziro a chiŵerengero cha anthu pa Stanford University ku United States, akufotokoza kukula kwa vuto limeneli, kuti: “Pamene kuchulukitsa kwa anthu m’maiko osauka kumawachititsa kukhalabe okanthidwa ndi umphaŵi, kuchulukitsa kwa anthu m’maiko olemera kumaluluza mphamvu yochilikiza moyo ya pulaneti lonse.”

Kuthekera kwakuti zinthu zotchulidwa poyambazo—kapena zinthu zina zonga kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka, kupereŵera kwa nyumba, upandu, ndi kukangana kwa mafuko—zingayambitse tsoka la pa dziko lonse patsogolopa kumadzetsa nkhaŵa yaikulu. Vutolo nlodziŵika bwino lomwe. Njira yochitira nalo njosadziŵika.

Kufunafuna Njira Zochitira Nawo

Chikhalirechobe, polingalira za kukula kwa mavutowo, maboma, paliŵiro losiyanasiyana, akufunafuna zothetsera. Mwachitsanzo, ponena za malo a dziko, msonkhano wa zamoyo ndi malo awo okhala waukulu koposa wina uliwonse umene unakhalako unachitika mu June wachaka chatha ku Rio de Janeiro. Msonkhano wotchedwa Earth Summit umenewu wochilikizidwa ndi Mitundu Yogwirizana unali wachiŵiri, pambuyo pa umene unachitika mu 1972 ku Stockholm, Sweden. Panthaŵiyo wandale wotchuka wa ku Jeremani anati: “Msonkhano uno ungakhale posinthira ponena za mtsogolo mwa pulaneti lino.”

Mwachiwonekere, msonkhano wa mu 1972 unalephera kukwaniritsa ziyembekezozo. Maurice F. Strong, wolinganiza wamkulu wa misonkhano yonse iŵiri wa mu 1972 ndi wa mu 1992, anavomereza kuti: “Taphunzira pa zaka 20 zapita kuyambira pa msonkhano wa ku Stockholm kuti lamulo la malo a dziko, limene lili chida chokha chimene mabungwe oyang’anira malo a dziko ali nacho, lili lofunika koma nlosakwanira. Liyenera kutsagana ndi kusintha kwakukulu kwa zolinga zazikulu za mkhalidwe wathu wachuma.”

Komabe, kodi msonkhano wa mu 1992 udzakhala utapeza chipambano chilichonse pakuchititsa “kusintha kwakukulu” kumeneku koposa uja wa mu 1972? Ngati sudzatero, kodi pulaneti lathu lidzakhozabe pambuyo pa zaka zina 20, mu 2012, kukhala malo a Msonkhano wa Earth Summit wothekera wachitatu?

Iyang’anizana ndi Vuto Lake Lalikulu Koposa

Anthu ambiri ayamba kukaikira kwambiri za mphamvu ya chipembedzo ndi ndale ya kuthetsa mavuto a dziko. Koma ngati chipembedzo ndi ndale sizingatero, kodi nchiyani chimene chingakhoze kuchita ndi mavuto owopsa a m’zaka za zana la 21?

Brosha lofalitsidwa ndi German Federal Ministry for Research and Technology likuyankha funsolo. “Kuchita ndi mavuto ameneŵa kumafuna maluso a ndale amene sangathandize chabe kupeŵa kusintha kulikonse kochitidwa ndi munthu komanso kuletsa zotsatirapo zoipa za kusintha kwa dziko lonse. Polingalira za kukula kwa mavuto amene tikuyang’anizana nawo, zosankha zanzeru za ndale zidzakhala zotheka zitazikidwa kokha pamaumboni a sayansi otsimikizirika ndi njira zodalirika zofufuzira zinthu. Imeneyi ikuwoneka kukhala njira yokha yopeŵera zochitika zofuna ndalama zambiri kapena ngakhale zosakhumbika ndi zatsoka. Kuperekedwa kwa chidziŵitso chimenechi kukudzetsa vuto lalikulu koposa kwa asayansi panthaŵi ino.”

Sayansi yayang’anizanapo kale ndi mavuto aakulu ndipo, ku mlingo wakutiwakuti, yakhoza kuchita nawo. Komabe, sikuli kolakwa kufunsa ngati sayansi ingakhoze kuchita ndi mavuto apadera amene adzakhala m’zaka za zana la 21 likudzalo. Kodi pali chifukwa choyembekezerera zabwino?

Galamukani! ali wokondwa kulengeza nkhani yopenda zinthu zazikulu zimenezi, imene idzafotokozedwa mumpambo wa nkhani kuyamba ndi kope lino. Gawo 1 likutsatira.

[Zithunzi patsamba 4]

Kodi nchiyani chimene sayansi ingachite ponena za kuipitsa, matenda, ndi kuchulukitsa kwa chiŵerengero cha anthu?

[Mawu a Chithunzi]

Chithunzithunzi cha WHO cha P. Almasy

Chithunzithunzi cha WHO cha P. Almasy

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena