Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 8/8 tsamba 23-24
  • Makolo Ankhanza Opsinja Maganizo Oipitsitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Makolo Ankhanza Opsinja Maganizo Oipitsitsa
  • Galamukani!—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nkhanza ya Mawu
  • Nkhanza ya Kumenyedwa
  • Nkhanza ya Kugonedwa
  • Sikumaiŵalika
  • Mmene Mungatetezere Ana Anu
    Galamukani!—2007
  • Chitetezo m’Nyumba
    Galamukani!—1993
  • Mabala Obisika a Kuchitira Nkhanza Ana
    Galamukani!—1991
  • Kodi Ndiyenera Kudziwa Zotani Zokhudza Nkhanza za Kugonana?​—Gawo 2: Zimene Mungachite Ngati Munachitidwapo Nkhanza Zotere
    Zimene Achinyamata Amafunsa
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 8/8 tsamba 23-24

Makolo Ankhanza Opsinja Maganizo Oipitsitsa

“Popeza kuti [ana] amadziŵa zochepa za kunja kwa banja lawo, zinthu zimene amaphunzira panyumba ponena za iwo eni ndi anthu ena ndizo zokha zimakhala zenizeni zokhomerezedwa zolimba m’maganizo mwawo.”—Dr. Susan Forward.

WOUMBA mbiya akhoza kutenga nchinchi ya dongo, naithira madzi oyenera, ndi kuiumba kukhala mbiya yokongola. Mofananamo, makolo amaumba kalingaliridwe ka mwana ponena za iye mwini ndi dziko. Ngati amapatsidwa chikondi, chitsogozo, ndi chilango, mwanayo amakula kukhala munthu wanzeru.

Komabe, kaŵirikaŵiri malingaliro ndi mtima wa mwana zimaumbidwa ndi makolo ankhanza. Nkhanza ya mawu, ya kumenyedwa ndi ya kugonedwa imaumba kalingaliridwe kopotoka kamene kamakhwima kwambiri ndi kovuta kuwongolera.

Nkhanza ya Mawu

Mawu angakhale opweteka kuposa kumenyedwa. “Ndikukumbukira kuti panalibe tsiku limene [amayi] sanandiuzepo kuti anakhumba kuti bwenzi sindinabadwe,” akutero Jason. Karen akukumbukira kuti: “Nthaŵi zonse ndinauzidwa zinthu zondipangitsa kulingalira kuti ndinali woipa kapena wosakwana bwino.”

Ana kaŵirikaŵiri amakhulupirira zimene amanenezedwa. Ngati mnyamata nthaŵi zonse amatchedwa wopusa, potsirizira pake amadziona kukhaladi wopusa. Mukatcha mtsikana kukhala wopanda pake, ndipo adzakhulupiriradi zimenezo. Ana ali ndi malingaliro ochepa ndipo kaŵirikaŵiri samasiyanitsa chimene chili chenicheni ndi chongowaneneza kapena chonama.

Nkhanza ya Kumenyedwa

Joe akukumbukira atate wake a nkhanza ya kumenya: “Iwo anali kuyamba kundimenya kufikira atandikanikiza kuchipupa. Anali kupitiriza kundibwanyula zolimba kufikira nditalefuka . . . Chowopsa kwambiri chinali chakuti sindinali kudziŵa konse kuti chimene chidzaputa mkwiyo wawo nchiyani!”

Jake anali kumenyedwa nthaŵi zonse ndi atate ake. Tsiku lina pomumenya motero, pamene iye anali wa zaka zisanu ndi chimodzi zokha, dzanja lake linathyoka. “Sindinafune kuti iwo kapena alongo anga kapena Amayi andiwone ndikulira,” Jake akukumbukira motero. “Ndicho chinthu chokha chimene ndinatsala nacho chochinyadira.”

Buku lakuti Strong at the Broken Places limanena kuti nkhanza yomenya mwana imafanana ndi “kukhala m’ngozi ya galimoto tsiku lililonse, mlungu uliwonse kapena mwezi uliwonse.” Nkhanza yoteroyo imaphunzitsa mwana kuti dziko lili malo opanda chisungiko ndi kuti palibe munthu amene angakhulupiriridwe. Ndiponso, chiŵaŵa kaŵirikaŵiri chimabala chiŵaŵa. “Ngati ana samatetezeredwa kwa owachitira nkhanza,” akuchenjeza motero magazini a Time, “pamenepo chitaganya tsiku lina chidzafunikira kutetezeredwa kwa anawo.”

Nkhanza ya Kugonedwa

Malinga ndi kuyerekezera kwina, mtsikana 1 mwa 3 ndi mnyamata 1 mwa 7 anakakamizidwa kugonana podzafika panthaŵi imene ali ndi zaka 18. Ambiri a ana ameneŵa amavutikira mumtima. “Mofanana ndi asilikali osochera m’nkhondo,” limatero buku lakuti The Child in Crisis, “iwo amakhalabe osochera kwa zaka m’nkhalango yodziŵa okha ya mantha ndi liwongo.”

“Ndinawada kwambiri atate wanga chifukwa chomandigona komanso ndinamva kukhala wa liwongo kwambiri chifukwa cha kuwada,” akutero Louise. “Ndinamva chisoni kwambiri chifukwa chakuti mwana ayenera kukonda makolo ake koma ine sindinatero nthaŵi zonse.” Malingaliro osokoneza oterowo ali omvekera bwino pamene mtetezi wa mwanayo asanduka kukhala womuukira. Beverly Engel akufunsa m’buku lakuti The Right to Innocence kuti: “Kodi tingavomereze bwanji kuti kholo lathu lenilenilo, munthu amene ayenera kukhala wotikonda ndi wotisamalira, akhale wosatisamala motero?”

Nkhanza ya kugonedwa imapotozeratu mmene mwana amaonera moyo. “Munthu wamkulu aliyense amene anagonedwa paubwana amakula ndi malingaliro opotozedwa akudziona kukhala wosakwanira, wopanda pake, ndi woyenerera kukhala woipa,” akulemba tero Dr. Susan Forward.

Sikumaiŵalika

“Sithupi lokha la mwana limene limaluluzidwa kapena kunyanyalidwa,” akulemba motero wofufuza Linda T. Sanford. “Mabanja omavutana amaluluza maganizo a mwana.” Pamene mwanayo achitiridwa nkhanza, kaya yamawu, ya kumenyedwa, kapena ya kugonedwa, iye angakule ndi malingaliro akuti ali wosayenera kukondedwa ndi wopanda pake.

Jason, wotchulidwa poyambapo, anali ndi malingaliro odzitsitsa oterowo monga munthu wamkulu kwakuti ananenedwa kukhala wokhoza kudzipha nthaŵi iliyonse. Iye anali kudziloŵetsa m’mikhalidwe yoika moyo wake paupandu, chifukwa chakuti anaona moyo wake mogwirizana ndi zimene amayi ake ankamuuza kuti: ‘Zikanakhala bwino ngati sukanabadwa konse.’

Polingalira ziyambukiro za nkhanza yakumenyedwa monga mwana, Joe akunena kuti: “Kuchoka panyumbapo kapena kukwatiwa sikumaiŵalitsa konse zimenezo. Nthaŵi zonse ndimaopa chinthu china chake, ndipo ndimadzida ndekha chifukwa cha kuchita mantha motero.” Kuipidwa kwa ana ochitiridwa nkhanza ya kumenyedwa m’banja kumachititsa ana ambiri kukula ndi ziyembekezo za kukumana ndi nkhanza ndipo amakhala ndi malingaliro amphamvu ofuna kudzitetezera amene amawaika muukapolo m’malo mowatetezera.

Kwa Connie, kugonedwa ndi wachibale kunakulitsa malingaliro opotoka mwa iye amene anakhwima pamene anakula: “Ndikulingalirabe za nthaŵi zambiri pamene anthu amaonekera kukhala akuona mkati mwanga ndi kuona mmene ndiliri wonyansa.”

Mitundu yonse ya kuchitiridwa nkhanza imaphunzitsa maphunziro oluluzika amene angazike mizu mwakuya podzafika m’nthaŵi ya uchikulire. Nzowona, zimene zimaphunziridwa zingachotsedwe. Ambiri amene achira nkhanza ya paubwana akuvomereza zimenezo. Koma nkwabwinopo chotani nanga ngati makolo azindikira kuti kuyambira panthaŵi yakubadwa kwa mwana wawo, iwo amakhala akuumba mbali yaikulu ya kalingaliridwe ka mwanayo ponena za iyemwini ndi dziko. Ubwino wa mwana wakuthupi ndi malingaliro umadalira kwakukulukulu pachisamaliro cha makolo.

[Chithunzi patsamba 24]

Mawu angakhale opweteka kuposa kumenyedwa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena