Tchalitchi cha Anglican cha ku Australia Nyumba Yogaŵanika
Ndi mtolankhani wa Galamukani! ku Australia
MKANGANO wakuti kaya akazi ayenera kuikidwa monga ansembe m’Tchalitchi cha Anglican suli watsopano. Koma nkhaniyi posachedwapa yakhala yaikulu m’Australia.
M’January 1992 bishopu wa ku Canberra ndi Goulburn analengeza makonzedwe a kuika akazi angapo kukhala ansembe a Tchalitchi cha Anglican. Iye sanayembekezere msonkhano wotsatira wa tchalitchi. Ndi iko komwe, misonkhano yapapitapo inali itakana kale maikidwe amenewo katatu.
Monga momwe zinachitikira m’kupita kwa nthaŵi, akazi khumi anaikidwa kukhala ansembe a Anglican kuchiyambiyambi kwa March ku Perth, Australia, mosasamala kanthu za chitsutso. Pamenepa, mposadabwitsa kuti chidwi chachikulu chinasumikidwa pamsonkhano wa tchalitchi wotsatira. Msonkhano wa m’July sunagamule motsimikiza, chotero “msonkhano wapadera” unalinganizidwa kudzachitika pa November 21, 1992.
Mlungu woposa umodzi tsikulo lisanafike, Msonkhano Waukulu wa Tchalitchi cha Mangalande unagamula moyanja kuikidwa kwa akazi. Ambiri anayembekezera kuti chosankha chimenechi chikakhala ndi chiyambukiro chabwino m’Australia. Pamene msonkhano wa ku Australia unachitika, nyuzipepala ina inati: “Panali mkangano ndi makani patsiku limene nthaŵi zina linali losakondweretsa.” Asanavumbule zotulukapo za chisankho, mkulu wa msonkhanowo anapempha kuti chilengezocho chilandiridwe mwakachetechete. Pamene zinadziŵika kuti kuikidwa kwa akazi kunavomerezedwa, ena mwa omvetsera anayesayesa kubisa mkwiyo wawo. Nkhaniyo itafalikira kunja, kunali chikondwerero chachikulu, ndipo anaulutsa timbendera.
Sikuti chimwemwecho chinali chisonyezero cha mgwirizano. The Sydney Morning Herald inagwira mawu akibishopu wa ku Sydney akumati: “Sitidzakhalira limodzi mwachimwemwe . . . Mudzakhala magulu aŵiri ogaŵanika m’Tchalitchi cha Anglican chimodzimodzichi.” Mtsogoleri wina wachipembedzo anafikira ngakhale pakunena kuti kuikidwa kwa akazi kukhala ansembe kunapereka chizindikiro chakuti “Tchalitchi cha Anglican m’Australia chikuyamba kunyonyotsoka.”
Baibulo limapereka maziko okwanira a nkhaŵa zoterozo. Yesu Kristu mwiniyo anati: “Ufumu uliwonse wogaŵanika pa wokha umapita kuchiwonongeko; palibe tawuni, palibe nyumba, imene ili yogaŵanika pa yokha ikhoza kuima.”—Mateyu 12:25, The New English Bible.
Zimenezi zimadzutsa funso limene lioneka kuti linasoŵa pamkangano wonse wa tchalitchi lakuti, Kodi Baibulo limanenanji za mbali ya akazi mumpingo? Pamene kuli kwakuti limanenadi kuti Yehova Mulungu amaŵerengera akazi ndi amuna odzipatulira mofanana, limapatsabe amuna ndi akazi mbali zosiyana mumpingo. (Agalatiya 3:28) Zimatchulidwa motere pa 1 Akorinto 11:3: “Pamene kuli kwakuti mwamuna aliyense ali ndi Kristu monga Mutu wake, mutu wa mkazi ndiye mwamuna, monga momwe Mutu wa Kristu ndiye Mulungu.” (NEB) Chotero, ponena za kuphunzitsa kwanthaŵi zonse mumpingo, Paulo anauziridwa ndi Mulungu kulemba kuti: “Mkazi ayenera kukhala wophunzira, womvetsera mwakachetechete ndi kugonjera koyenera. Sindilola mkazi kukhala mphunzitsi, ndipo mkazi sayenera kulamulira mwamuna.”—1 Timoteo 2:11, 12, NEB.
Komabe, zimenezi siziyenera kukwiyitsa akazi Achikristu pakuti ali ndi ufulu wa kuphunzitsa muutumiki wapoyera monga momwe anachitira akazi onga Loisi, Yunike, Euodiya, ndi Suntuke m’nthaŵi zoyambirira Zachikristu.—Afilipi 4:2, 3; 2 Timoteo 1:5.