Chifukwa Chimene Ndinasiyira Unsembe Kuyamba Utumiki Wabwino Koposa
NDINAIKIDWA monga wansembe Wachikatolika pa July 31, 1955, pausinkhu wa zaka 24. Kunali kumaliza maphunziro anga a zaka 12 za kukula paseminale ya aakibishopu, ku Rachol, Goa, India. Ndipo kodi nchiyani chimene chinandipatsa chikhumbo cha kukhala wansembe?
Ndinabadwira ku Bombay, India, pa September 3, 1930. Chaka chotsatira, atate anapuma pantchito, ndipo monga banja tinakakhala ku Salvador do Mundo, Bardez, Goa, ku gombe lakummwera koma chakumadzulo kwa India. Ndinali wamng’ono pa ana onse anayi. Kuyambira ukhanda ndinaleredwera m’miyambo ndi kakhalidwe Kachikatolika koma Kachipwitikizi, zimene zakhala m’Goa kuyambira mu 1510, pamene analamulidwa ndi Portugal.
Makolo anga, pokhala okhulupirika pazikhulupiriro zawo, anali Akatolika achangu amene chaka ndi chaka ankachita phwando la Krisimasi, Lent, Isitala, ndi mapwando olemekeza Namwali Mariya ndi “oyera mtima” angapo. Ansembe amene anali ndi mbali m’mapwando ameneŵa kaŵirikaŵiri anali kugona m’nyumba mwathu, nthaŵi zina kwa masiku oposa khumi panthaŵi imodzi. Motero, timacheza nawo kwambiri, ndipo monga mnyamata anandichititsa chidwi kwambiri.
Utumiki Wanga ku Goa, Salamanca, ndi Rome
Ndinayamba utumiki wa unsembe ndi chikondwerero chachikulu, ndipo ndinalibe zikayikiro zilizonse ponena za kulondola kwa ziphunzitso ndi madzoma a Tchalitchi cha Katolika. M’zaka zanga zoyambirira zisanu ndi ziŵiri za kutumikira ku Goa, ndinachita ntchito yothandiza anthu ndi ubusa pa St. Thomas Chapel ku Panaji, likulu la Goa. Panthaŵi imodzimodziyo, pa imene kale inali Polytechnic Institute ya boma la Apwitikizi, ndinali ndi udindo wina wosakhala waubusa umene unali ndi mbali ziŵiri—profesa ndiponso mkulu wa pamalopo.
Mu 1962, ndinatumizidwa ku Yunivesite ya Salamanca, ku Spain, kumene ndinapeza digiri ya PhD (Doctor of Philosophy) m’maphunziro otchedwa Philosophy of Law ndi Canon Law. Mkati mwa kuphunzira kwanga zamalamulo, maphunziro ena amene ndinaphunzira, makamaka a Roman Law ndi History of Canon Law, anandisonkhezera kufufuza mmene chilamulo cha Tchalitchi cha Katolika chinayambira ndi kukula kufikira pakuzindikiritsa papa kukhala woloŵa m’malo wa Petro wokhala ndi ‘mphamvu pa tchalitchi chonse.’
Ndinali wokondwa kuti makonzedwe anali kupangidwa akuti maphunziro anga a digiri ya ukatswiri wazaumulungu akachitidwire ku Rome, Italy, kumene ndikakhala ndi mpata wakuphunzira zochuluka ponena za utsogoleri wa tchalitchi. Ndinasamukira ku Rome m’chilimwe cha 1965.
Panthaŵiyi msonkhano wa bungwe logwirizanitsa matchalitchi wa Vatican II unali utatha. Pamene ndinapitirizabe ndi maphunziro anga azaumulungu, ndinali ndi makambitsirano osangalatsa ndi akatswiri azaumulungu angapo ndi “Oyambitsa Bungwelo” amene anatsutsa osunga mwambo mopambanitsa a m’bungwelo. Papa wolamulira panthaŵiyo anali Paul VI, amene ndinali kukambitsirana naye mwachindunji pokhala wachiŵiri kwa mkulu wa Bungwe la Ansembe la India m’Rome.
Mikangano ndi Zikayikiro Zoyambirira
M’nyengo yonse ya makambitsirano ameneŵa ndi maphunziro anga ndi kufufuza kwanga malingaliro aukatswiri, ndinali ndi mpata wa kukhala ndi chidziŵitso chozama cha mbiri ndi makulidwe a mpangidwe wonse a Tchalitchi cha Katolika.a Mosiyana ndi malingaliro a osunga mwambo m’bungwelo, amene anali ozoloŵerana ndi mtundu wa ulamuliro wosatsutsika wa Pius XII (1939-58), okonda kusintha anadzakhoza kuchititsa bungwelo kuvomereza Chilamulo cha Ziphunzitso pa Tchalitchi (Dzina la Chilatin, Lumen Gentium, Kuunika kwa Amitundu). Pakati pa nkhani zina, chinafotokoza m’chaputala 3 kuyenera kwa bungwe la abishopu kukhala muulamuliro wonse waukulu koposa wa papa pa tchalitchi. Chiphunzitsochi chinali chozikidwa mwakuya m’miyambo koma osunga mwambo anachiyesa kukhala champatuko ndi chodzetsa kusintha kwakukulu.
Ndinapeza malingaliro onse aŵiri kukhala osavomerezeka, popeza kuti analibe chowonadi cha m’Mauthenga Abwino. Amapotoza Mateyu 16:18, 19 napereka maziko a zikhulupiriro ndi ziphunzitso zonse za tchalitchi zosakhala za malemba zakale ndi zamtsogolo.b Ndinaona kuti mawu Achigiriki ogwiritsiridwa ntchito m’lembali, peʹtra (liwu lachikazi), lotanthauza “thanthwe,” ndi peʹtros (liwu lachimuna), lotanthauza “benthu la thanthwe,” sanagwiritsiridwe ntchito ndi Yesu monga mawu ofanana. Ndiponso, ngati Petro adapatsidwa ukumu kukhala thanthwe, monga mwala wapangondya, sipakadakhala mkangano pambuyo pake pakati pa atumwi wonena za amene anali wamkulu mwa iwo. (Yerekezerani ndi Marko 9:33-35; Luka 22:24-26.) Ndiponso, Paulo sakanayesa konse kudzudzula Petro poyera chifukwa “sanalikuyenda kowongoka, monga mwa chowonadi cha uthenga wabwino.” (Agalatiya 2:11-14) Ndinafika pakuzindikira kuti otsatira a Kristu odzozedwa ndi mzimu onse mofanana ali ngati miyala, Yesu nkukhala mwala wa pangondya.—1 Akorinto 10:4; Aefeso 2:19-22; Chivumbulutso 21:2, 9-14.
Pamene ndinapeza malo apamwamba m’maphunziro anga ndi ubusa, ndiponso pamene ndinagaŵana kwambiri malingaliro anga ndi ena, mpamenenso ndinakhala wotalikirana kwambiri m’maganizo ndi mtima ndi ziphunzitso zaukumu za Tchalitchi cha Katolika, makamaka zija zokhudza kuikidwa kwa ansembe mogwirizana ndi “Nsembe Yopatulika ya Misa” ndi “Sakalamenti Yodalitsika Koposa ya Ukalisitiya”—yotchedwa kusandulika kwa mkate ndi vinyo.
Malinga nkunena kwa Akatolika, “Nsembe Yopatulika ya Misa” ili chikumbutso chosatha ndi kuperekedwanso kwa nsembe ya Yesu pa “mtanda” popanda kukhetsa mwazi. Koma Malemba Achikristu Achigiriki onse ndipo makamaka kalata ya Paulo kwa Ahebri anali omvekera bwino lomwe kwa ine moti ndinafikira pakuzindikira kuti nsembe ya Yesu inali nsembe yangwiro. Ntchito yake inali yokwanira. Sinafunikire kuwonjezeredwa, kubwerezedwa, kapena kuwongoleredwa ndipo inali yosakhoza kutero. Nsembeyo inaperekedwa “kamodzi, kwatha.”—Ahebri 7:27, 28.
Kufunafuna Kwanga Chowonadi Kupitiriza
Kuti ndidziyese, ndinapitiriza kugwirira ntchito zigawo za tchalitchi zoyang’aniridwa ndi abishopu ndi aakibishopu ku Kumadzulo kwa Ulaya, chigawo choyang’aniridwa ndi akibishopu cha New York, ndi chigawo choyang’aniridwa ndi bishopu cha Fairbanks, ku Alaska. Kunali kudziyesa kopweteka kwa zaka zisanu ndi zinayi pakufunafuna kwanga chowonadi. Kwakukulukulu ntchito yanga inali yauyang’aniro, ya za malamulo a tchalitchi, ndi zachiweruzo. Ndinayesa mwanjira iliyonse kusaloŵerera m’miyambo ndi madzoma akulambira. Vuto lalikulu koposa linali la kudalitsa Misa masiku onse. Zimenezi zinandiika pankhondo yaikulu yolimbana ndi malingaliro ndi maganizo otekeseka chifukwa sindinakhulupirire m’nsembe ya Kristu yobwerezabwereza yopanda kukhetsa mwazi kapena kusandulika kwa mkate ndi vinyo kapena ansembe opatulika a padziko lapansi ofunikira kuchita mwalamulo ndi moyenera “chozizwitsa” cha kusandulika kwa mkate ndi vinyo.
Pamsonkhano Wachiŵiri wa Bungwe la Vatican, panali mkangano pa “chozizwitsa” chimenechi. Okonda kusintha otsogozedwa ndi ansembe Achikatolika a ku Holland anachilikiza “phiphiritso la mkate ndi vinyo,” ndiko kuti, mkate ndi vinyo zimangotanthauza kapena kuimira thupi ndi mwazi wa Kristu. Komabe, osunga mwambo mopambanitsa, otsogozedwa ndi ansembe Achikatolika a ku Italy, mouma khosi anachilikiza “kusandulika kwa mkate ndi vinyo,” ndiko kuti, kusintha kwa mkate ndi vinyo kukhaladi thupi ndi mwazi weniweni wa Kristu mwa “mawu odalitsa” onenedwa pa Misa. Chotero, panakhala mwambi wakuti: ‘Ku Holland zinthu zonse zimasintha kusiyapo mkate ndi vinyo, pamene ku Italy palibe chimene chimasintha kusiyapo mkate ndi vinyo.’
Kuchoka Kwanga m’Tchalitchi
Polingalira za kuimira molakwa Kristu ndi uthenga wake wabwino kumeneku, ndinagwiritsidwa mwala moipa ndi kulefulidwa kuti chonulirapo changa cha kulemekeza Mulungu ndi kupulumutsa miyoyo chinadodometsedwa ndi ziphunzitso zonama. Chotero, m’July 1974, ndinasiyiratu kuchita utumiki ndikumapempha kupuma pantchito kwa nyengo yosadziŵika. Kunali kopanda pake ndi kosafunika kwa ine kupempha kumasulidwa ku zoŵinda za unsembe umene unalibe maziko a m’Baibulo. Chotero, kuyambira m’July 1974 mpaka December 1984, ndinakhala wosagwirizana ndi chipembedzo chilichonse. Sindinagwirizane ndi chipembedzo chilichonse cha Dziko Lachikristu chifukwa chakuti zonse sizinagwirizane ndi zimene ndinapeza zotsutsa Utatu, kusafa kwa moyo, chiphunzitso chakuti anthu onse olungama adzalandira moyo wosatha kumwamba, ndi chilango chosatha cha moto wa helo. Ndinaona ziphunzitso zimenezi kukhala zotengedwa ku chikunja.
Mtendere wa Maganizo ndi Chimwemwe
Kudzilekanitsa kwanga ndi chipembedzo kunatha m’December 1984. Pokhala ndi malo aumanijala m’dipatimenti ya Credit and Accounts Receivables ya bizinesi ya ku Anchorage, ku Alaska, ndinafunikira kukambitsirana za mainvoisi angapo ndi kasitomala wina, Barbara Lerma. Iye anali wofulumira ndipo ananena kuti anali kupita ku “phunziro la Baibulo.” Mawuwo “phunziro la Baibulo” anandikopa, ndipo ndinamfunsa mafunso angapo a m’Baibulo. Panthaŵi yomweyo ndipo mogwira mtima anandipatsa mayankho a m’Malemba amene anali ogwirizanako ndi malingaliro anga a ziphunzitso za Malemba. Poona kuti ndinali ndi mafunso ambiri, Barbara anandidziŵikitsa kwa Gerald Ronco, amene anali paofesi yanthambi ya Mboni za Yehova m’Alaska.
Makambitsirano okhudza Baibulo omangirira amene anatsatirapo anandidzetsera mtendere wa maganizo ndi chimwemwe. Iwowa anali mtundu wa anthu amene ndinali kufunafuna—anthu a Mulungu. Ndinapemphera kwa Mulungu kuti anditsogoze ndipo m’kupita kwa nthaŵi ndinayamba kugwirizana ndi Mboni za Yehova monga wofalitsa wosabatizidwa wa mbiri yabwino. Ndinadabwa kwambiri kudziŵa kuti malikulu a gulu limeneli anali ku Brooklyn, New York, makilomita angapo kuchokera ku Holy Family Church ku Manhattan, kumene ndinatumikira (mu 1969, 1971, ndi 1974) monga mmodzi wa apasitala pa Parish Church ya United Nations.
Kuthandiza Banja Langa Kuzindikira Chowonadi
Pambuyo pogwirizana ndi Mboni za Yehova ku Anchorage kwa miyezi isanu ndi umodzi, ndinasamukira ku Pennsylvania pa July 31, 1985. Kunoko ndinali ndi mwaŵi wa kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Yehova kwa mwana wamkazi wa achemwali, Mylene Mendanha, amene anali kuchita maphunziro apamwamba a biochemistry pa Yunivesite ya Scranton. Pamene Mylene anadziŵa kuti ndinali kufunafuna Mboni za Yehova, anadabwa kwambiri, popeza kuti anauzidwapo molakwa kuti gululo nlampatuko. Poyamba sananene kalikonse kwa ine chifukwa anandilemekeza monga amalume ake ndi wansembe ndipo analemekeza kwambiri zipambano zanga m’maphunziro ndi ubusa.
Sande yotsatira, Mylene anapita ku Tchalitchi cha Katolika ku Misa, ndipo ine ndinapita ku Nyumba Yaufumu kukamvetsera nkhani ya Baibulo ndi Phunziro la Nsanja ya Olonda. Tsiku limenelo madzulo tinakhala pamodzi, iye anali ndi Jerusalem Bible la Akatolika ndipo ine ndi New World Translation of the Holy Scriptures. Ndinamsonyeza dzina la Yahweh m’Baibulo lake ndi la Yehova lolingana nalo, mu New World Translation. Anakondwera kudziŵa kuti Mulungu ali ndi dzina ndi kuti amafuna tonsefe kumuitana ndi dzina lake. Ndinamsonyezanso kuti ziphunzitso za Utatu, kusandulika kwa mkate ndi vinyo, ndi kusafa kwa moyo sizili za m’malemba ndipo ndinamsonyeza malemba oyenera. Iye anangodabwa!
Chikondwerero cha Mylene chinakulirapo pamene ndinamuuza za chiyembekezo cha moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi. Asanadziŵe zimenezo anada nkhaŵa ponena za zimene zikamchitikira atafa. Anaganiza kuti sanali woyera kwambiri moti nkukhoza kupita kumwamba mwachindunji, komanso sanaganize kuti anali woipa kwambiri moti anayenera kuweruzidwira kuchilango chosatha cha moto wa helo. Chotero, zokha zimene zinali m’maganizo mwake zinali kupita kupuligatoriyo, kumene akayembekezera moleza mtima mapemphero a anthu ndi Misa kumpititsa kumwamba. Komabe, nditamsonyeza ndi kumfotokozera malemba angapo onena za chiyembekezo cha moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi, anali wofunitsitsa kuphunzira zambiri ponena za mbiri yabwino koposa imeneyi. Mylene anapita nane kumisonkhano ku Nyumba Yaufumu. Tinayamba phunziro la Baibulo lanthaŵi zonse ndi Mboni zakwathu. Mwamsanga pambuyo pake, tinadzipatulira kwa Yehova Mulungu ndi kubatizidwa pa May 31, 1986.
Banja langa, makamaka achimwene anga aakulu, a Orlando, anakwiya atamva za kusiya kwanga unsembe. Anafunsa achemwali anga a Myra Lobo Mendanha, amene anawatonthoza, kuti: “Tisavutike kwambiri ndi nkhaniyi, pakuti Alinio sakanataya m’madzi zaka 43 zimene anagwira ntchito zolimba popanda chifukwa chabwino.” M’September 1987, Myra ndi banja lake anadzakhala nane ku Wisconsin, U.S.A. Sindinavutike kuwaonetsa kuti ziphunzitso ndi madzoma ambiri Achikatolika sizinali za m’malemba. Iwo anali ofunitsitsa kuphunzira chowonadi cha m’Baibulo. Pomwepo, ine ndi Mylene tinayambitsa phunziro la Baibulo kwa iwo. Atasamukira ku Orlando, Florida, anapitiriza phunziro lawo.
Mtendere ndi chimwemwe zimene tinakhala nazo zinatisonkhezera kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Yehova kwa achemwali anga aakulu, a Jessie Lobo, amene amakhala ku Toronto, Canada. Umboni udaperekedwapo kwa iwo mu 1983. Komabe, pokhala ndi mchimwene wansembe, anakhulupirira kuti palibe chilichonse chimene chikawasinthitsa chikhulupiriro chawo. Patapita zaka zinayi kuchokera pakukambitsirana koyambako ndi Mboni za Yehova, pamene anadziŵa kuti ndinakhala mmodzi wa Mboni za Yehova ndi kuti Myra ndi banja lake anali alaliki a mbiri yabwino, anakakambitsirana ndi Mboni imene inalinganiza phunziro la Baibulo mwamsanga. A Jessie anabatizidwa pa April 14, 1990; Myra, alamu anga a Oswald, mwana wamkazi wa achemwali Glynis anabatizidwa pa February 2, 1991. Iwo ali achimwemwe kutumikira Yehova, Wam’mwambamwamba.
Ansembe osunga mwambo ndi okonda kusintha m’Tchalitchi cha Katolika alidi anthu anzeru. Amakhulupirira kuti akuchita chifuniro cha Mulungu. Komabe, sitiyenera kunyalanyaza mfundo yakuti “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano [a]nachititsa khungu maganizo awo a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha uthenga wabwino wa ulemerero wa Kristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire.” (2 Akorinto 4:4) Pamenepa, nkoonekeratu kuti nzeru ya dongosolo ili la zinthu ili kupusa m’maso mwa Mulungu. (1 Akorinto 3:18, 19) Ndine woyamikira ndi wachimwemwe chotani nanga kuti Yehova ‘amapatsa opusa nzeru’ kupyolera mwa chidziŵitso cholongosoka cha Mawu ake.—Salmo 19:7.
Zaka zanga 19 za kutumikira monga wansembe Wachikatolika zangokhala mbiri yakale. Tsopano ndine mmodzi wa Mboni za Yehova. Cholinga changa ndicho kuyenda m’njira za Yehova ndi kutsatira Mwana wake, Yesu Kristu, Mfumu ndi Mpulumutsi wathu. Ndikufuna kuthandiza ena kudziŵa Yehova kuti nawonso angakhale oyenerera mphotho ya moyo wosatha padziko lapansi laparadaiso, kuulemerero wa Mulungu wowona, Yehova.—Yosimbidwa ndi Alinio de Santa Rita Lobo.
[Mawu a M’munsi]
a Ndinachoka ku Salamanca ndikufufuzabe malingaliro anga pa Canon Law, amene ndinapereka mu 1968.
b Malinga ndi New American Bible Lachikatolika, mbali ya lemba limeneli imati: “Ine pandekha ndinena kwa iwe kuti, ndiwe ‘Thanthwe,’ ndipo pathanthwe ili ndidzamangapo tchalitchi changa . . . Chilichonse chimene unena kuti chamangidwa padziko lapansi chidzamangidwa kumwamba; chilichonse chimene unena kuti chamasulidwa padziko lapansi chidzamasulidwa kumwamba.”—Onani bokosi, patsamba 17.
[Bokosi patsamba 17]
Mfungulo za Ufumu
Ponena za “mfungulo za ufumu wa kumwamba,” tanthauzo lake limakhala lomvekera bwino pamene tipenda mawu amene Yesu anadzudzula nawo atsogoleri achipembedzo kuti: “Munachotsa chifungulo cha nzeru; inu simunaloŵamo nokha, ndipo munawaletsa iwo analinkuloŵa.” (Luka 11:52) Lemba la Mateyu 23:13 likumveketsa bwino lomwe liwulo ‘kuloŵamo’ kusonyeza kuloŵa mu “ufumu wakumwamba.”
Mfungulo zimene Yesu analonjeza Petro zinali ntchito yapadera yophunzitsa imene ikatsegulira anthu mpata wapadera wa kuloŵa mu Ufumu wakumwamba. Petro anagwiritsira ntchito mwaŵi umenewu pazochitika zitatu, kuthandiza Ayuda, Asamariya, ndi Akunja.—Machitidwe 2:1-41; 8:14-17; 10:1-48; 15:7-9.
Cholinga cha lonjezolo sichinali chakuti Petro akalamulira miyamba ponena za chimene chinali choyenera kapena chosayenera kumangidwa kapena kumasulidwa, koma kugwiritsiridwa ntchito kwa Petro monga chiŵiya cha miyamba chochitira magawo atatu amenewo. Ndimmene ziliri popeza kuti Yesu anakhalabe Mutu wa mpingo.—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 11:3; Aefeso 4:15, 16; 5:23; Akolose 2:8-10; Ahebri 8:6-13.
[Chithunzi patsamba 18]
Alinio de Santa Rita Lobo tsopano ndi Mboni