Nthenda Zakupha Zabukanso
MARGARET anafunafuna mankhwala mothedwa nzeru pamene mwana wake wamwamuna Tito anagwidwa ndi malungo. Mitundu itatu ya mankhwala, kuphatikizapo mankhwala a “chloroquine” otamandidwa kwambiriwo anaperekedwa. Komabe, Tito anafa—pausinkhu wa miyezi isanu ndi inayi yokha.
Ku Kenya, kwawo kwa Margaret, tsoka lotero limachitika kaŵirikaŵiri. “Newsweek” ikusimba kuti: “‘Anopheles gambiae,’ mtundu waukulu wa udzudzu wa malungo, umapeza bwino kudera limeneli ladziko. Ana satero. Maperesenti asanu a iwo amafa chifukwa cha malungo asanafike pausinkhu wopita kusukulu.”
Mu 1991 “tuberculosis” (nthenda ya kholodzi) inapha akaidi 12 ndi mlonda wawo mu New York State, U.S.A. “Tidzailetsa m’ndende,” akutero Dr. George DiFerdinando, Jr., “komano vuto lalikulu ndilakuti ndimotani mmene mungailetsere tsopano popeza kuti yafalikira m’chitaganya?”
Gulu la World Health Organization likusimba kuti anthu mamiliyoni zikwi 1.7—pafupifupi chigawo chimodzi mwa zitatu cha chiŵerengero cha anthu—ali ndi kachilombo ka kholodzi. Chaka chilichonse, mamiliyoni asanu ndi atatu a ameneŵa amayamba kudwala nthendayo, ndipo mamiliyoni atatu amafa.
M’chipatala cha ku New York, munabadwa mwana wamkazi wosakwana masiku ndi milungu 11, koma limeneli sivuto lokha limene anali nalo. Kufundula kwa manja ake, zilonda kumapazi ake, kutupa chiŵindi ndi kapamba, zonsezo zinasonyeza kuti anagwidwa ndi chindoko pamene anali m’mimba mwa amake.
“Ana ena amavulazidwa kwambiri ndi nthendayo pamene ali m’mimba mwa amawo kwakuti amabadwa akufa,” ikusimba motero “The New York Times.” “Angapo amafa atangobadwa, ena amakhala ndi zilonda pathupi zimene zimatemeka pobadwa.”
Malungo, kholodzi, ndi chindoko—nthenda zitatu zonsezo zinalingaliridwa kukhala zitaletsedwa ndipo zinali pafupi kuthetsedwa zaka makumi angapo zapitazo. Kodi nchifukwa ninji zikubukanso?