Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 7/8 tsamba 12-14
  • Kununkhiza Glu Kodi Kungandivulazedi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kununkhiza Glu Kodi Kungandivulazedi?
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Imfa ya Mwadzidzidzi
  • Kuipitsa Thupi ndi Maupandu Ena
  • Musayese!
  • Kugwiritsa Ntchito Mankhwala Koyenera ndi Kosayenera
    Galamukani!—2009
  • Mankhwala Osokoneza Bongo Pakati pa Achinyamata
    Galamukani!—2003
  • Mabala Obisika a Kuchitira Nkhanza Ana
    Galamukani!—1991
  • ‘Nthaŵi ya Kuchira’
    Galamukani!—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 7/8 tsamba 12-14

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kununkhiza Glu Kodi Kungandivulazedi?

“NZABWINO kwambiri—kungokhala ngati ukuonerera zipukwa.” Akutero Sveta, mtsikana wazaka 13 wa ku Moscow, Russia.a Koma Sveta sakulankhula motenthedwa maganizo ponena za filimu kapena vidiyo yatsopano kwambiri. Iye akufotokoza chokumana nacho chake ndi mtundu wa kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka kumene kuli kofala pakati pa zikwi za achichepere padziko lonse—kununkhiza glu.

Komabe, glu ali kokha chimodzi cha zinthu zambiri zimene achichepere ena akununkhiza. Mwachitsanzo, m’Britain, zonunkhiritsira mpweya, mafuta okolezera, ndi “zogwiritsira ntchito m’nyumba zina kuchokera pa 20 kufika pa 30 . . . zikugwiritsiridwa ntchito molakwa,” malinga ndi kunena kwa magazini a Young People Now. Zimenezi zimaphatikizapo “zopopera zoletsa kupweteka, polishi wa mipando, ndi zinthu zomatira matayala.” Eya, achichepere ena amanunkhiza ngakhale utsi wa chozimitsira moto! Chotero nkolondola kwambiri kutcha chizoloŵezi chovulaza komanso chofala chimenechi kukhala “kugwiritsira ntchito molakwa zosungunulira” kapena “kugwiritsira ntchito molakwa zinthu zouluka,” monga momwe amachitira akatswiri ena.

Kaya akugwiritsira ntchito molakwa glu kapena polishi wa mipando, onunkhizawo amafunafuna zotulukapo zofanana. Malinga ndi kunena kwa buku lina, iwo amafuna “kukhala ‘oledzera’ kapena ‘ochangamuka’ mofanana ndi kuledzeretsa kwa moŵa.” Zosungunulira nzotsika mtengo ndi zosavuta kupeza kusiyana ndi anamgoneka omwerekeretsa monga ngati cocaine. Motero magazini a New Scientist a ku Britain anasimba kuti: “Zosungunulira zakhala anamgoneka a amphawi, ana ndi osoŵa pokhala: ana a m’khwalala a ku Guatemala ndi nzika za malo osungidwa a mu North America, limodzinso ndi achichepere okhala m’mahositelo ndi nyumba zogonako anthu opanda pokhala m’Britain.” Akuluakulu ena akukhulupirira kuti mu Britain, 1 mwa atsikana ndi anyamata 10 ausinkhu wa zaka zapakati pa 13 mpaka 19 ananunkhizapo zosungunulira. Ndipo ziyambukiro zake zili zovulaza ndithu.

Kabuku kakuti Drug Misuse kakufotokoza kuti “nthunzi wa zosungunulira umakokedwa kuloŵa kudzera m’mapapu ndipo mofulumira umafika ku ubongo.” Zosungunulira zimayambukira dongosolo lalikulu la minyewa, ndipo mofanana ndi moŵa, zingachititse lingaliro lakanthaŵi la kuchangamuka. Mwa ogwiritsira ntchito ena, izo zimatulutsa mitundu yosiyanasiyana ya kuona zideruderu—ndipo yonse sili yokondweretsa monga momwe walongosolera Sveta poyambapo. “Ndinaona makoswe ambirimbiri,” akutero wachichepere wotchedwa David amene ananunkhiza glu pamsinkhu wa zaka 14. “Analipo zikwizikwi—aang’ono akumatuluka mwa aakulu. Ndinalingalira kuti anali kudya bwenzi langa.” Wachichepere wa ku Japan wotchedwa Kazuhiko, amene anayamba kununkhiza glu pa msinkhu wa zaka 17, akukumbukira kuti: “Ndinaona nthaka ikung’aluka ndi zilombo zikundiukira.”

Pamenepo, kodi nchifukwa ninji kununkhiza zosungunulira kuli kokopa motero kwa achichepere ena? Lee, amene anayamba kununkhiza glu pamene anali ndi zaka 13, akuti: “Kwakukulukulu, chifukwa chimene anthu amachitira zimenezo ndi kuyesayesa kuthaŵa zenizeni.” Inde, kwa achichepere ena, kuchangamuka ndi zosungunulira kuli njira yoiŵalira mavuto. Ena amalakalaka chisangalalo; iwo amaganiza kuti kuona zideruderu zoopsa kuli ngati filimu yoopsa yosangulutsa. “Zifukwa zina,” ikutero Department of Health ya ku Ireland, “zimaphatikizapo chidwi, kuvomereza chitsenderezo cha gulu la ausinkhu wanu, kuyesayesa kupeza malo, kulipirira kuchepa kwa ulemu waumwini ndi malingaliro a kusakwaniritsa.”

Imfa ya Mwadzidzidzi

Kaya nkokondweretsa motani, kununkhiza zosungunulira kuli kachitidwe kakupha! Kunachititsa imfa 149 mu Britain mu 1990, ndipo nthaŵi zina kumapha m’mphindi zochepa chabe. Kukutchedwa “imfa yamwadzidzidzi ya kununkhiza.” Mwachitsanzo, Rachel, ankatsanulira madzi ofafanizira zilembo za taipi pa mkono wa malaya ake ndi kumawanunkhiza m’sukulu. Tsiku lina anawanunkhiza pamene anali paulendo wa pa basi. Anatsika basiyo ndi kugwa. Anadzuka kwa kamphindi ndi kugwanso—wakufa! Rachel anali ndi zaka 15.

Chowopsa kwambiri ndi chenicheni chakuti zosungunulira zingakupheni nthaŵi yoyamba yeniyeni imene mungazigwiritsire ntchito molakwa! Re-Solv, gulu lothandiza osauka la ku Britain limene linakhazikitsidwa kulimbana ndi kugwiritsira ntchito molakwa zosungunulira, likusimba kuti “18% ya imfa zonse za kugwiritsira ntchito molakwa zosungunulira pakati pa 1971 ndi 1989 inali ya ‘onunkhiza’ oyamba kumene.” Wamng’ono kopambana amene anafa anali wazaka zisanu ndi zinayi zokha. Mofanana ndi kugwiritsira ntchito molakwa zakumwa zoledzeretsa, kugwiritsira ntchito molakwa zosungunulira kunganenedwe kuti kumaluma ‘ngati njoka, ndi kujompha ngati mamba.’—Miyambo 23:32.

Onunkhiza angafenso chifukwa cha ngozi zochitika pamene ali pansi pa chisonkhezero cha zosungunulira. Ena agwa pa nyumba, kapena kumira. Ena akomoka ndi kutsamwa ndi masanzi awo. Ena afa chifukwa cha kununkhiza atavala kumutu thumba lapulasitiki; iwo analedzera kwambiri kolephera kuchotsa thumbalo, ndipo anapuya. Komabe ena apsa mpaka kufa pamene zosungunulirazo zinagwira moto.

Kuipitsa Thupi ndi Maupandu Ena

Ngakhale kuti zotulukapo zowopsa zotero sizimachitika kwa onse, katswiri wina akulemba kuti: “Wogwiritsira ntchito molakwa wanthaŵi zonse amadziŵa kuti ‘akuipitsa’ dongosolo lake ndipo amamva kupweteka m’chifuwa, kulephera kukhala wolinganizika, litsipa, kulephera kukumbukira ndi unyinji wa zizindikiro zina zimene samavomera kaŵirikaŵiri.” Lee (wogwidwa mawu poyambirira) akukumbukira motere: “Ndinadwala litsipa loipitsitsa limene sindinadwalepo m’moyo wanga.” Gulu la Re-Solv likunena kuti kununkhiza zosungunulira kungawononge impso ndi chiŵindi, kungasokoneze maganizo, ndipo kungachititse tondovi.

Ndiyeno pali maupandu a makhalidwe. Onunkhiza ena akhala mbala kuti achirikize chizoloŵezi chawo. Kapena talingalirani zimene zinasimbidwa mu Daily Yomiuri ya ku Japan: “Mmodzi wa achichepere atatu amene anapatsidwa mlandu wakupha mwambanda msungwana wazaka zapakati pa 13 ndi 19 [ananena] kuti analibe lingaliro la liwongo pamene anali kupha msungwanayo chifukwa chakuti anali pansi pa chisonkhezero cha [zosungunulira] pa nthaŵiyo.”

Pomalizira, kugwiritsira ntchito molakwa zosungunulira kungachititse kudalira zosungunulira—kumwerekera. “Pafupifupi 10% ya awo amene amagwiritsira ntchito molakwa zosungunulira amakhala onunkhiza ozoloŵera,” ikutero Glasgow Herald ya ku Scotland. Zimenezi zingangododometsa kukula kwa maganizo ndi kwa uzimu kwa munthu. Talingalirani mawu a Baibulo a pa 1 Akorinto 14:20 akuti: “Musakhale ana m’chidziŵitso, koma . . . m’chidziŵitso akulu misinkhu.” Kodi munthu amakula motani m’nkhani imeneyi? Baibulo likulongosola pa Ahebri 5:14 kuti: “Chakudya chotafuna chili cha anthu aakulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloweretsa zizindikiritso zawo kusiyanitsa chabwino ndi choipa.” Womwerekerayo amalephera kukulitsa zizindikiritso zake. Mmalo moyang’anizana ndi mavuto, iye amayesa kuwathaŵa mwa kuloŵa m’kuodzera kochititsidwa ndi anamgoneka. Magazini akuti Young People Now ananena kuti onunkhiza omwerekera “amagwidwa m’zaka zapakati pa 13 ndi 19—osakhoza kuloŵa mu uchikulire.”

Musayese!

Mungadziŵe ausinkhu wanu ena amene ayesa kununkhiza zosungunulira, ndipo nkwachibadwa kukhala wa chidwi. Koma Baibulo limati: “Tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuwopa Mulungu.” (2 Akorinto 7:1) Kodi nkuyeseranji chinthu chimene chimaipitsa thupi lanu kapena kukuchititsani kulephera kulamulira maganizo anu, ngakhale kwakanthaŵi? Uphungu wa Mawu a Mulungu kwa ife ngwakuti tiyenera “kusunga nzeru zathu.” (1 Atesalonika 5:6, NW) Mawu ameneŵa kwenikweni amatanthauza kuti “tisaledzere.” Mmalo moipitsa kulingalira kwa mtengo wake, Mkristu mwanzeru amakuchinjiriza.—Miyambo 2:11; 5:2.

Kazuhiko akuti: “Ndili wachisoni kuti ndinayamba chizoloŵezicho.” Lee akuvomereza, akumati: “Nzopusa. Nchinthu chowopsa koposa kuchichita.” Dzipatuleni ku kupweteka ndi chisoni chachikulu, ndipo musayese konse kununkhiza zosungunulira. Chitani monga momwe Baibulo likunenera kuti: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.”—Miyambo 22:3.

Komabe, kugwiritsira ntchito uphungu umenewu kungakhale kovuta. “Chitsenderezo cha gulu la ausinkhu wanu” chikunenedwa kukhala chimodzi cha zifukwa zofala kwambiri zimene achichepere amakodwera ndi kugwiritsira ntchito molakwa zosungunulira. “Mkulu wanga anandichititsa kukondwera ndi kununkhiza glu,” akutero David wachichepere. “Mabwenzi anga anandiyambitsa,” akuwonjezera motero Kazuhiko. Inde, monga momwe lemba la 1 Akorinto 15:33 limanenera, “mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” Kodi nkuloleranji ausinkhu wanu kuwononga moyo wanu? Yehova Mulungu, Atate wathu wakumwamba, akuchenjeza kuti: “Mwananga, akakukopa ochimwa usalole.”—Miyambo 1:10.

Mwanzeru, lolani makolo anu kudziŵa ngati ena akukutsenderezani kugwiritsira ntchito anamgoneka. Iwo angathandize kulimbitsa chosankha chanu cha kukana. Kumbali ina, mwinamwake mukuyesedwa kuyesa kununkhiza zosungunulira chifukwa chakuti mukulingalira kukhala wotsenderezedwa kapena wothedwa nzeru ndi mavuto. Chithandizo chabwino koposa cha kupsinjika maganizo ndicho kuuza makolo anu mavuto anu kapena wachikulire wina wokhwima maganizo, wachifundo. Mufunikira chitsogozo, osati kuwonjoka kupyolera mwa anamgoneka. Mungapindulenso ndi makonzedwe a pemphero kuti akuthandizeni kulaka. “Khulupirani pa [Mulungu] nyengo zonse,” akutero wamasalmo. “Tsanulirani mitima yanu pamaso pake.”—Salmo 62:8.

Kununkhiza zosungunulira kungaonekere kukhala kokondweretsa, koma sikudzathetsa mavuto anu. Ndithudi, kungawononge moyo wanu. Khalani anzeru. Musayese konse.

[Mawu a M’munsi]

a Ena a mainawo asinthidwa.

[Chithunzi patsamba 13]

Musalole chitsenderezo cha ausinkhu wanu kukunyengererani kuloŵa m’chizoloŵezi chakupha

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena