Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 1/8 tsamba 5-6
  • Kupsa ndi Ntchito—Kodi Ndani Ali Pangozi Ndipo Nchifukwa Ninji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupsa ndi Ntchito—Kodi Ndani Ali Pangozi Ndipo Nchifukwa Ninji?
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Amene Angapse ndi Ntchito Mosavuta
  • Chifukwa Chake Anthu Amapsa ndi Ntchito
  • Kupsa ndi Ntchito—Kodi Mungalimbane Nako Motani?
    Galamukani!—1995
  • Kupsa ndi Ntchito—Kodi Ndinu Wotsatira?
    Galamukani!—1995
  • Kodi Mungatani Ngati Mukupanikizika Chifukwa cha Ntchito?
    Galamukani!—2014
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndisamapanikizike Kwambiri?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 1/8 tsamba 5-6

Kupsa ndi Ntchito—Kodi Ndani Ali Pangozi Ndipo Nchifukwa Ninji?

TADZIYEREKEZERANI kuti mumagwira ntchito ya mu ofesi ndipo muli ndi banja—kapena mwinamwake ndimmene ziliri. Ntchito zangoti mulu ndu pathebulo lanu. Foni imangoimba kaŵirikaŵiri, makasitomala anu akumafunsira zochuluka kwambiri moti nkovuta kuzikwaniritsa zonse. Woyang’anira ntchito wanu ali wosakondwa chifukwa chakuti simumatsiriza ntchito yanu panthaŵi yake. Mwana wanu wamwamuna wapulupudza kusukulu. Mphunzitsi wake akufuna kuonana nanu mwamsanga. Kupempha kwanu thandizo kwa wa muukwati mnzanu kukunyalanyazidwa. Pamene mkhalidwewo uoneka kukhala wosalamulirika, kupsinjika kumakhala nsautso, ikumachititsa kupsa ndi ntchito.

Kodi kupsa ndi ntchito kumachititsidwa ndi kugwira ntchito kopambanitsa? Ann McGee-Cooper, wofufuza za ubongo, ananena kuti kupsa ndi ntchito “kumachititsidwa ndi kuchita zinthu mopambanitsa, makamaka kungogwira ntchito popanda kupumula.” Komabe, kugwira ntchito kopambanitsa sindiko kokha kumene kumachititsa zimenezo; m’mikhalidwe yopanikiza yofananayo, ena amapsa ndi ntchito pamene ena samatero.

Amene Angapse ndi Ntchito Mosavuta

Monga momwedi kulili anthu amene amayambukiridwa msanga ndi nthenda yakutiyakuti, kulinso anthu amene akhoza kupsa ndi ntchito mosavuta. “Kuti munthu apse ndi ntchito,” akutero Elliot Aronson, profesa wa za kakhalidwe ka anthu pa University of California, “ayenera kukhala ndi changu chamoto.” Chotero awo amene amakonda kupsa ndi ntchito ali ndi changu chamoto cha zonulirapo ndi zolinga zosafikirika. Kwanenedwa kuti aja amene amapsa ndi ntchito kaŵirikaŵiri ndi amene amakondedwa koposa ndi makampani awo.

Akumafotokoza mwachidule mikhalidwe ya anthu amene angapse ndi ntchito mosavuta, Profesa Fumiaki Inaoka wa pa Red Cross College of Nursing ya ku Japan, m’buku lakuti Moetsukishokogun, (Zizindikiro za Kupsa ndi Ntchito) analemba kuti: “Awo amene kaŵirikaŵiri amapsa ndi ntchito ali ndi chikhoterero champhamvu cha kukhala achifundo, okoma mtima, odera nkhaŵa za ena, odzipereka, ndi okhala ndi zolinga zabwino zosafikirika. Iwo ‘amakonda anthu’ kuposa makina, titero kunena kwake.”

Atapemphedwa kupeza njira yodziŵira ndi kuchotsa awo amene angapse ndi ntchito, katswiri wina ananena kuti njirayo m’malo mwake iyenera kugwiritsiridwa ntchito monga muyezo wopezera antchito. “Zimene makampani afunikira kuchita,” iye anatero, “ndizo kupeza anthu okonda kupsa ndi ntchito . . . ndiyeno kupeza njira zothetsera kupsa ndi ntchito.”

Amene ali pangozi makamaka ndi awo amene amachita mautumiki aumunthu, monga antchito othandiza osauka, madokotala, manesi, ndi aphunzitsi. Iwo amayesayesa mwamphamvu kuthandiza anthu, akumadzipereka pa kuwongolera moyo wa ena, ndipo angapse ndi ntchito pamene azindikira kuti sakufikira zonulirapo zimene adziikira zimene nthaŵi zina zili zosafikirika. Anakubala amene amasamala nawonso angapse ndi ntchito pachifukwa chimodzimodzicho.

Chifukwa Chake Anthu Amapsa ndi Ntchito

Kufufuza kochitidwa pakati pa manesi kunavumbula zinthu zitatu zimene zimachititsa kupsa ndi ntchito. Choyamba chinali unyinji wa zovuta za tsiku ndi tsiku zolefula. Mwachitsanzo, unyinji wa manesi anali ndi mathayo olemera, kulimbana ndi zovuta pochita ndi odwala, anafunikira kuzoloŵera makina atsopano, kuyang’anizana ndi kukwera kwa mitengo, ndi kupirira moyo wosazoloŵereka. “Zovuta za tsiku ndi tsiku zimenezi zimasonkhezera kwambiri kupsa ndi ntchito kwawo,” likutero buku lakuti Moetsukishokogun. Pamene mavuto sathetsedwa, kulefuka kumangokula ndipo kumachititsa kupsa ndi ntchito.

Chachiŵiri chimene chinatchulidwa ndicho kusoŵeka kwa chichirikizo, kusoŵa wina woululira zakukhosi. Chotero, nakubala amene amadzilekanitsa ndi anakubala ena akhoza kupsa msanga ndi ntchito. Kufufuza kotchulidwa pamwambapo kunasonyeza kuti manesi amene ali mbeta amakonda kwambiri kupsa ndi ntchito kuposa okwatiwa. Chikhalirechobe, kukwatiwa kungawonjezere zovuta za tsiku ndi tsiku ngati palibe kulankhulana kosabisa zakukhosi pakati pa mwamuna ndi mkazi wake. Ngakhale pamene aliyense ali panyumba, munthu angasungulumwebe chifukwa chakuti banja lake lamwerekera ndi kuonerera wailesi yakanema.

Chachitatu chinali kudzimva kukhala wosoŵa chochita. Mwachitsanzo, manesi akhoza kudzimva kwambiri kukhala osoŵa chochita kuposa madokotala chifukwa chakuti manesiwo alibe ukumu wa kusintha zinthu. Amanijala aang’ono angapse ndi ntchito pamene aona kuti zoyesayesa zawo zoposa sizikuphula kanthu. Monga momwe manijala wa zachithandizo chaumunthu ananenera, kupsa ndi ntchito kumachititsidwa ndi kukhala “wolefulidwa mwa kuyesayesa kuchita zonse zothekera ndi kunyalanyazidwa.”

Malingaliro akusoŵa chochita mwa anthu amakula m’nthaka ya mkhalidwe wosayamika ndi kubala chipatso cha kupsa ndi ntchito. Akazi amapsa ndi ntchito pamene amuna awo samayamikira kuchuluka kwa ntchito ya kukonza panyumba ndi kusamalira ana. Amanijala aang’ono amapsa ndi ntchito pamene mkulu wantchito anyalanyaza ntchito yabwino imene iwo amachita ndi kumawafunira zifukwa pa zophophonya zawo zazing’ono. “Choonadi nchakuti tonsefe timafuna kuti kuyesayesa kwathu kuyamikiridwe ndi kuzindikiridwa,” akutero magazini a Parents, “ndipo ngati tigwira ntchito pamalo amene zoyesayesa zathu sizifupidwa—panyumba pathu kapena kuntchito kwathu—ndiye kuti tikhoza kupsa msanga ndi ntchitoyo.”

Mokondweretsa, pamene kuli kwakuti manesi ambiri amapsa ndi ntchito, othandiza anakubala kubereka amene amapsa ndi ntchito ali oŵerengeka kwenikweni. Kaŵirikaŵiri, ntchito ya wothandiza anakubala kubereka imaphatikizapo kuthandiza miyoyo yatsopano kufika m’dziko. Anakubala ndi abambo amawayamikira kaamba ka ntchito yawo. Pamene anthu ayamikiridwa, amamva kuti ali othandiza ndipo amalimbikitsidwa.

Wina atangodziŵa munthu amene amakonda kupsa ndi ntchito ndi chifukwa chake amatero, kumakhala kosavuta kulimbana ndi vutolo. Nkhani yotsatira ingathandize anthu opsa ndi ntchito kukhala ndi kaonedwe kabwino ka moyo.

[Mawu Otsindika patsamba 6]

Kupsa ndi ntchito kumachititsidwa ndi kungogwira ntchito popanda kupumula

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena