Kupsa ndi Ntchito—Kodi Mungalimbane Nako Motani?
ATAPANIKIZIKA ndi kupsinjika chifukwa cha nkhaŵa ndi zovuta za tsiku ndi tsiku, ambiri amayesa kuiŵala mavuto awo mwa kumwa moŵa. Moŵa, umene umamwedwa mopambanitsa kwambiri lerolino, ambiri amaugwiritsira ntchito kuti aiŵale zovuta m’moyo. Ena adalira mankhwala otchuka kuti athetse nkhaŵa. Komabe ena amatembenukira ku mankhwala ogodomalitsa, onga chamba, methamphetamines, ndi cocaine. Ngakhale ana aang’ono akhala akugwiritsira ntchito anamgoneka kuti aiŵale zovuta za moyo. Kwanenedwa kuti 95 peresenti ya anyamata ndi atsikana Achimereka amakhala atagwiritsirapo ntchito kale mankhwala oletsedwa a mtundu umodzi kapena yambiri asanamalize maphunziro awo pasukulu yasekondale.
Ndiyeno pali awo amene amayesa kuiŵala kupsinjika kwa tsiku ndi tsiku mwa kusanguluka kosadziletsa ndi mabwenzi awo kapena kunamizira kuti ali okondwa pamene mumtima ali opsinjika. Kapena pazifukwa zolakwika, amafunafuna chikondi ndi chisamaliro cha osiyana nawo ziŵalo. Koma kugwiritsira ntchito njira zoiŵalira mavutowo polimbana ndi kupsinjika kumangowonjezera kulefuka. Pamene anthu ayesa kuchepetsa mphamvu ya kupsinjika mwa kumwa moŵa kapena kugwiritsira ntchito mankhwala ena ogodomalitsa, amafulumiza mchitidwe wa kupsa ndi ntchito m’malo mwa kudzutsanso nyonga yawo. Nanga kodi nchiyani chimene mungachite pamene muona kuti changu chanu chamoto chikutha pang’onopang’ono?
Mmene Mungachirire
Galamukani! siimapereka machiritso kapena mankhwala akutiakuti. Komabe, ikupereka malingaliro othandiza angapo ozikidwa pa miyezo ya Baibulo amene angakuthandizeni kudzutsanso nyonga yanu yomathayo. Dr. Yutaka Ono, mtsogoleri wa pa Keio University School of Medicine, akupereka “[zinthu] zitatu” zolimbanirana ndi kupsa ndi ntchito. Iye akufotokoza kuti: “‘[Zinthu] zitatuzo’ ndizo kulamulira, kulankhulana, ndi kuzindikira.”
Kuti mugonjetse malingaliro a kusoŵa chochita, muyenera kukhala wokhoza kumva kuti mukulamulira malingaliro anu ndi khalidwe. Pamene kulefuka kulamulira mtima wanu tsiku ndi tsiku ndi kuwononga mphamvu yanu ya kuthetsa mavuto, kumakhala kosavuta kuganiza kuti zinthu zafika posawongolereka. Komabe, musakhale chabe ndwii ndi kumangolingalira za zovutazo. Yesani kuthetsa vuto lanu pang’onopang’ono. (Onani bokosi, patsamba 8.) Musazengereze. Mwa kungochitapo kanthu, mudzayamba kupezapo bwino ndi kulamulira malingaliro anu.
Yesani kuchepetsa zokwiyitsa zimene zimayambitsa malingaliro a kungoumirira pa mavutowo. Mwachitsanzo, ena amakonda kukwiyakwiya pa tinthu tilitonse tating’ono m’moyo. Amaumirira pa njira yakutiyakuti yochitira zinthu ndipo amapsa mtima pamene ena saitsatira, kapena mwina amakhumudwa ndi kulephera kwawo. “Usapambanitse kukhala wolungama,” mwamuna wina wanzeru wakale anatero, “usakhale wanzeru koposa; bwanji ufuna kudziwononga wekha?” (Mlaliki 7:16) Kuumirira pa miyezo yapamwamba imene ili yosafikirika ndi kumaganiza nthaŵi zonse kuti simukuifikira ndiko kumachititsadi munthu kupsa ndi ntchito.
Uphungu wina wothandiza wa m’Baibulo ndiwo “kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.” (Mika 6:8) Kudzichepetsa kumatanthauza kuzindikira zimene munthuwe sukhoza kuchita kapena “kuona maluso a munthuwe kukhala ochepa.” Zimenezi zingatanthauze kukana zinthu zopanikiza pamalo antchito.
Awo amene adziŵa zimene sakhoza kuchita amafuna thandizo. Manijala wina wamkazi amene anapsapo ndi ntchito ananena kuti njira yaikulu yopeŵera zimenezo ndiyo kupempha thandizo. Chikhalirechobe, iye akuti, “anthu ambiri amawopa kupempha thandizo chifukwa amawopa kuti angasekedwe kuti ntchito yawo ikuwavuta.” Ikhale ntchito yapanyumba, yakusukulu, kapena kuntchito—iliyonse imene ingakutentheni—igaŵireni ngati mungakhoze. Mudzadabwa mmene zinthu zidzachitidwira popanda inu kuyang’anira zilizonse mwachindunji.—Yerekezerani ndi Eksodo 18:13-27.
Mwina mungafunikire kupumula. Kutengako tchuthi pantchito kungakhale kothandiza kwambiri kwa munthu amene ali pafupi kupsa ndi ntchito. Komabe, ngati mikhalidwe yanu silola zimenezo, “ngati mudziŵa mmene mungakhalire wokondwa, zimathandiza kwambiri,” akutero wofufuzayo Ann McGee-Cooper. Kupumira ntchito ina ndi kuyamba ina kungachititsedi ntchito yochuluka kuchitidwa, kukumasonkhezera maganizo anu kukhala ndi luntha la kuchita zosiyanasiyana. Uphungu umene Mfumu Solomo anapereka zaka zambiri zapitazo udakagwirabe ntchito wakuti: “Dzanja limodzi lodzala pali mtendere liposa manja aŵiri oti tho pali vuto ndi kungosautsa mtima.”—Mlaliki 4:6.
Olankhulana Nawo Ochirikiza
Chinthu chachiŵiri chimene Dr. Ono anatchula ndicho kulankhulana. Nkosangalatsa kuti kaŵirikaŵiri ozima moto samapsa ndi ntchito yawo. Zimenezi zingakhale chifukwa chakuti, kuwonjezera pa kuonedwa kwawo monga ngwazi, iwo ali ogwirizana ndi chomangira cholimba cha ubwenzi. Pokhala ndi anthu ochirikiza omwe amawadalira, munthu angapeze thandizo kwa iwo. Kodi nkuti kumene mungapeze chichirikizo chotonthoza lerolino? Polongosola njira za madokotala zochitira ndi kupsa ndi ntchito, buku lakuti Moetsukishokogun (Zizindikiro za Kupsa ndi Ntchito) likuti: “Kwa madokotala, mabanja awo, makamaka wa muukwati mnzawo, ali wolimbitsa mtima wachipambano ndi woona.” Aliyense amafuna wina wolankhula naye zakukhosi. Pankhani imeneyi ya kulankhulana, Baibulo limapereka uphungu wogwira ntchito. Limalimbikitsa okwatirana kukhala okondana kwambiri ndipo limauza onse kukhala ndi mabwenzi amene angawapatse malingaliro othandiza ndi ogwira ntchito.—Miyambo 5:18, 19; 11:14.
“Tiyenera kukhala ndi njira yathuyathu yopezera chichirikizo kwa mabwenzi athu apamtima ndi banja lathu,” ikutero USA Today. Ndiyeno ikuwonjezera kuti: “Tiyeneranso kukhala aufulu kugwiritsira ntchito njira zochirikizira zimene zipembedzo zathu ndi zipatala zosamalira zamaganizo zimapereka.” Ponena za mmene tingagwiritsirire ntchito njira zachipembedzo zochirikizira, Yakobo, mbale wa Yesu wa bambo wina, analemba kuti: “Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu a mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m’dzina la Ambuye.” (Yakobo 5:14) Akristu amene ali ndi mavuto angapeze mpumulo mwa kulankhula ndi akulu a mipingo ya Mboni za Yehova. Ngakhale kuti akulu sali akatswiri osamalira vuto la kupsa ndi ntchito, chichirikizo chauzimu chimene amapereka nchofunika koposa.
Pamene kuli kwakuti njira yaumunthu ya chichirikizo ingatipatsenso nyonga yogwiritsira ntchito tsiku lina, singakhale yokwanira nthaŵi zina. M’mawu oyamba a buku lake lakuti, Helplessness, Martin E. P. Seligman anatchula mzimu wa kudzidalira kwambiri wopezeka Kumadzulo kukhala chochititsa kupsinjika maganizo kowonjezereka lerolino, ndipo anatchula kufunika kwa kupeza moyo watanthauzo. Ndiyeno anasonyeza kuti “chinthu chimodzi chofunika kuti mupeze moyo watanthauzo ndicho kudzipereka pa chinthu china chachikulu kuposa inuyo.” Ngakhale kuti anthu ambiri lerolino samauona mwamphamvu unansi wawo ndi Mulungu, kulankhulana ndi Mlengi—amene alidi ‘wamkulu kuposa inuyo’—kungakuthandizeni kulimbana ndi malingaliro osoŵa chochita.
Mfumu Davide, amene anayang’anizana ndi masoka ambiri, analimbikitsa nzika zake kuti: “Khulupirani pa [Mulungu] nyengo zonse, anthu inu: tsanulirani mitima yanu pamaso pake: Mulungu ndiye pothaŵirapo ife.” (Salmo 62:8) Mulungu ndi wokonzekera kutitchera khutu, ngakhale kumva “zobuula [zathu] zosatheka kuneneka.” (Aroma 8:26) Kumchonderera mwakhama kumadzetsa mtendere umene ‘ungasunge mitima yanu ndi maganizo anu’ kuti musapse ndi ntchito.—Afilipi 4:6, 7.
Kusintha Kaonedwe Kanu ka Zinthu
Chomalizira, mungafunikire kusintha mmene mumaonera mkhalidwe wanu. Kuzindikira, kapena kumvetsetsa, ndiko chinthu chomalizira chimene Dr. Ono akuchitchula kukhala njira yolimbanira ndi kupsa ndi ntchito. Pamene tipsinjika mtima kwambiri, timakonda kuona chilichonse moipa ndi kugwera mumsampha wa kumangolingalira za vutolo. Komabe, tifunikira kuona zinthu monga momwe zilili. Tapendani mkhalidwe wanu kuona ngati palidi chifukwa chenicheni cholingalirira zosautsa mtimazo. Kodi zotsatirapo zake zidzakhala zoipa kwambiri malinga ndi zimene mukuwopa? Yesayesani kukhala ndi kaonedwe kosiyana ka zinthu.
“Mungayambe kutero mwa kuganiza kuti ngati mwapsa ndi ntchito, mwinamwake chili chifukwa chakuti ndinu ‘wabwino,’ osati ‘woipa,’” akutero magazini a Parents. Kumbukirani: Anthu amene amakonda kupsa ndi ntchito ali ndi miyezo yapamwamba ndipo amasamala anthu ena. Zimene zimathandiza kwambiri munthu wakupsa ndi ntchito ndiwo mawu achiyamikiro. Zinthu zikhoza kukhalapo bwino kwambiri kwa nakubala ngati mwamuna wake ndi ana ake amamyamikira kaamba ka ntchito yonse yosamalira banja. Ngati manijala wamng’ono amapsa ndi ntchito, mawu oyamikira ndi kumpapasa papheŵa kungawongolere kwambiri kaonedwe kake ka zinthu.
Baibulo limasonyeza mmene mkazi wochita bwino amayenererera kuyamikiridwa: “Anake adzanyamuka, nadzamutcha wodala; mwamuna wake namtama, nati, Ana akazi ambiri anachita mwangwiro, koma iwe uposa onsewo.” (Miyambo 31:10, 28, 29) Ndithudi, “mawu okoma ndiwo chisa cha uchi, otsekemera m’moyo ndi olamitsa mafupa.”—Miyambo 16:24.
Shinzo, mkulu Wachikristu wotchulidwa m’nkhani yoyamba, anachira mokulirapo pa vuto lake la kupsa ndi ntchito. Ngakhale kuti analandira thandizo la akatswiri, chimene chinathandiza Shinzo koposa chinali mapemphero ake kwa Yehova. Pambuyo pa mapemphero ake amtima wonse opempha thandizo, iye anakumana ndi mkulu amene anali ataphunzira naye Mawu a Mulungu kwanthaŵi yoyamba. Mkulu ameneyo, ndi akulu anzake ena, anamchirikiza mwa kumvetsera nkhaŵa zake. M’kope lapapitapo la magazini amene mukuŵerenga tsopano, mkazi wake anamuŵerengera nkhani zonena za kulaka kupsinjika mtima. (October 8, 1992) M’kupita kwa nthaŵi iye anazindikira kuti anali kuyesa kuchita zonse yekha. Kaonedwe kake ka zinthu zimene zinali kumchitikira kanayamba kusintha. Ngakhale kuti poyamba anamva ngati anali m’dzenje lalitali la kutaya mtima, anayamba kuona kuti panali zifukwa zokhalira ndi chiyembekezo kufikira pomalizira pake anatuluka m’dzenjelo.
Mofanana ndi Shinzo, inunso mukhoza kulimbana ndi kupsa ndi ntchito ndi kuchitanso nawo moyo.
[Bokosi patsamba 8]
Njira Khumi ndi Ziŵiri Zoletsa Kupsa ndi Ntchito
ZOTSATIRAZI zazikidwa pa malingaliro oŵerengeka chabe operekedwa ndi katswiri wa m’kiliniki wodziŵa kusamalira nthenda zamaganizo.
1. Lamulirani maganizo anu, mtima, ndi khalidwe lanu—pemphero limathandiza kwambiri.
2. Mutayamba kuda nkhaŵa, sinthani dala kalingaliridwe kanu ndi kulingalira zinthu zothandiza ndi zotsimikizirika.
3. Mutakalipa, foyani ndipo mwadala khazikani mtima pansi.
4. Yesani kuona mikhalidweyo malinga ndi mmene munthu wina angaionere kuti mumvetsetse mmene kupsinjikako kwayambira.
5. Sumikani maganizo pa mikhalidwe yabwino imene mumaona mwa ena ndipo ayamikireni. Ayamikireni pa zenizeni m’malo mokometsa pakamwa.
6. Zindikirani ndipo letsani kalingaliridwe koipa ndi kowononga.
7. Dziŵani kukana ngati nyonga yanu yachepa ndipo ngati ndandanda yanu siilola.
8. Chitani maseŵera olimbitsa thupi masiku onse—kuyenda mofulumira kowongola miyendo nkwabwino.
9. Chitirani ena mwaulemu, mukumayesayesa kuwasonkhezera kuchita zabwino koposa.
10. Khalani wanthabwala ndi wokondwa.
11. Siyani kuntchito mavuto anu akuntchito.
12. Chitani lero lomwe zimene ziyenera kuchitidwa—musazengereze.
(Zotengedwa mu “Dealing With Feelings, Beating Burnout,” lolembedwa ndi Ruth Dailey Grainger, American Journal of Nursing, January 1992.)
[Chithunzi patsamba 9]
Kupsa ndi ntchito kaŵirikaŵiri kumachitikira munthu wokangaza, wotsimikiza mtima