Kupsa ndi Ntchito—Kodi Ndinu Wotsatira?
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU JAPAN
“Maweta achikazi ku Sweden, aphunzitsi ku Japan, antchito ya mtengatenga ku America, oyendetsa mabasi ku Ulaya ndi antchito yopanga zinthu m’mafakitale kulikonse akusonyeza zizindikiro za kupsinjika ndi ntchito.”—MAINICHI DAILY NEWS.
NOBUAKI anatha mphamvu. Akumagwira ntchito usana ndi usiku, analemba antchito 130 m’miyezi inayi yokha. Iye anali manijala wa nthambi yatsopano ya gulu lalikulu la ma supermarket m’Japan, ndipo mwa kuyesayesa kwake pansi pa chitsenderezo, analemba ntchito anthu amene sanafike pa muyezo umene iye anafuna. Iwo anali kumenyana ndi kudandaula za ntchito yawo. Ndiponso, wantchito wachimuna anathaŵa ndi wantchito wachikazi. Nobuaki anali kudwala mutu tsiku lililonse. Posapita nthaŵi, analephera kupita ku ntchito, ndipo pamasiku amene anadzikakamiza kupita, ankabwera msanga kunyumba. Iye anapsa ndi ntchito, monga macheso amene atha kupsa.
Akazi apanyumba nawonso amapsa ndi ntchito. Atatha zaka ziŵiri akukhala ndi ana ake atatu panyumba, Sarah anakhala wamtima wapachala kwambiri kwa iwo. “Ndinamva ngati ndinali kungowagwirira ntchito kwamuyaya, ndipo ntchitoyo sinali kutha,” iye anatero. Pamene nakubala agwira ntchito yolembedwa ndi kulera ana, kupsa ndi ntchito kumakhala pafupi kwambiri. Betty, m’zaka zake za m’ma 40, anakhala mumkhalidwe wofuna kulera ana ndi kugwira ntchito panthaŵi imodzimodziyo, akumayesa kuchita ntchito ziŵirizo bwino lomwe. Anayesa kukondweretsa aliyense—mwamuna wake, ana ake, womlemba ntchito, ndi antchito anzake. BP yake inali kukwera, ndipo tinthu tating’ono tinamkwiyitsa. Anapsa ndi ntchito.
Kupsa ndi ntchito kumakantha ngakhale anthu amene samakuyembekezera. Shinzo, mtumiki Wachikristu wochita bwino, anali ndi changu ndi zonulirapo zabwino. Iye anapita kukathandiza kumalo kumene kunali kusoŵa kwakukulu kwa aphunzitsi Achikristu. Komabe, m’miyezi yoŵerengeka, iye anatha mphamvu, ndipo anadzitsekera m’chipinda chake chogona tsiku lonse. Anamva ngati anali m’dzenje lopanda kotulukira. Anali kuvutika kupanga zosankha, ngakhale ponena za chimene adzadya masana. Analibenso chikhumbo cha kuchita kalikonse. Anapsa kotheratu ndi ntchito.
Kodi Kupsa ndi Ntchito Nchiyani?
Pamenepa, kodi kupsa ndi ntchito nchiyani? Herbert Freudenberger ndi ofufuza ena anayamba kugwiritsira ntchito liwu limeneli chapakati pa ma 1970, ndipo linadzatanthauza “mkhalidwe wa kutha mphamvu chifukwa chochita ndi anthu m’mikhalidwe yovutitsa mtima kwambiri.” Ndiponso, ndiko “kutha mphamvu kapena nzeru, makamaka chifukwa cha kupsinjika kwanthaŵi yaitali kapena chifukwa cha mkhalidwe wa kusadziletsa.” (American Heritage Dictionary) Komabe, liwulo, malinga ndi wofufuza aliyense, limamasuliridwa mosiyanasiyana.
Ngakhale kuti kupsa ndi ntchito kulibe dzina lodziŵika m’zamankhwala, anthu amene ali ndi vutolo amadziŵika mwa zizindikiro zake zonga kutopa, kusakondwa, kusoŵa chochita, kuthedwa nzeru, ndi kusamva bwino m’thupi. Munthuyo amamva kutopa kwambiri ndipo amakwiya ndi tinthu tating’ono. Palibe chilichonse chimene chingamsonkhezere kukhala wachangu. Zonse zimaoneka kukhala zothetsa nzeru, ndipo motaya mtima angafune thandizo kwa aliyense amene akumana naye. Zoyesayesa zake zonse ku ntchito ndi panyumba zingaoneke kukhala zosathandiza. Amakhala ndi malingaliro a kuthedwa nzeru. Ngati muli ndi zizindikiro zimenezi limodzi ndi kusamva bwino m’thupi, kusakondwa ndi chilichonse, ndiye kuti mwina mukupsa ndi ntchito.
Kupsa ndi ntchito kungayambukire ntchito ndi moyo wa banja. Mufunikira kukupeŵa. Koma kodi mungatero motani? Kuti tipeze yankho, tiyeni choyamba tione amene amapsa ndi ntchito mosavuta ndi chifukwa chake.
[Bokosi patsamba 4]
Zizindikiro za Kupsa ndi Ntchito
“Kupsa ndi ntchito kumatanthauza mkhalidwe wa maganizo wofooketsa wochititsidwa ndi kupsinjika ndi ntchito kopitirizabe, umene umachititsa:
1. Kutha kwa nyonga
2. Kuchepa kwa mphamvu yolimbana ndi matenda
3. Kusakhutira kowonjezereka limodzi ndi kudandaula
4. Kulova ku ntchito kaŵirikaŵiri ndi kusagwira bwino ntchito.
“Mkhalidwe umenewu ndi wofooketsa chifukwa chakuti uli ndi mphamvu ya kulefula, ngakhale kuthetsa nzeru mwanjira zina anthu athanzi, anyonga, ndi ochita bwino. Chochititsa chake chachikulu ndicho kupsinjika kopitirizabe, kumene kumapitiriza tsiku ndi tsiku, mwezi ndi mwezi, chaka ndi chaka.”—The Work/Stress Connection: How to Cope With Job Burnout, lolembedwa ndi Robert L. Veninga ndi James P. Spradley.