Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwyp nkhani 74
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndisamapanikizike Kwambiri?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingatani Kuti Ndisamapanikizike Kwambiri?
  • Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene zimachititsa
  • Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji?
  • Zimene mungachite
  • Kupsa ndi Ntchito—Kodi Mungalimbane Nako Motani?
    Galamukani!—1995
  • Kupsa ndi Ntchito—Kodi Ndani Ali Pangozi Ndipo Nchifukwa Ninji?
    Galamukani!—1995
  • Kodi Mungatani Ngati Mukupanikizika Chifukwa cha Ntchito?
    Galamukani!—2014
  • Kupsa ndi Ntchito—Kodi Ndinu Wotsatira?
    Galamukani!—1995
Onani Zambiri
Zimene Achinyamata Amafunsa
ijwyp nkhani 74
Wachinyamata wapanikizika ndi zochita zambiri. Akufuna kulemba za kusukulu, kuchita masewero olimbitsa thupi komanso zinthu zina

ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA

Kodi Ndingatani Kuti Ndisamapanikizike Kwambiri?

Kodi mukuvutika chifukwa chopanikizika ndi zinazake? Ngati ndi choncho ndiye kuti nkhaniyi ingakuthandizeni.

  • Zimene zimachititsa

  • Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji?

  • Zimene mungachite

  • Zimene achinyamata anzanu amanena

Zimene zimachititsa

  • Kukhala ndi zochita zambiri. Mtsikana wina dzina lake Julie ananena kuti: “Pa zilizonse zomwe timachita, timauzidwa kuti tiziyesetsa kuzichita bwino kwambiri komanso kukhoza bwino. Zimenezi zimachititsa kuti tizipanikizika kwambiri.”

  • Zipangizo zamakono. Chifukwa cha zipangizo ngati mafoni, matabuleti komanso zipangizo zina zomwe tikugwiritsa ntchito panopo, anthu ena akhoza kukuimbira kapena kukutumizira meseji nthawi ina iliyonse. Zimenezi zimatopetsa ndipo kenako umayamba kupanikizika.

  • Kusagona mokwanira. Mtsikana wina dzina lake Miranda ananena kuti: “Achinyamata ambiri amadzuka m’mawa kwambiri komanso kugona mochedwa. Amakhala ndi zochita zambiri monga kupita kusukulu, kugwira ntchito komanso kuchita zosangalatsa.” Zimenezi zimachititsa kuti munthu azipanikizika.

Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji?

Baibulo limatilimbikitsa kugwira ntchito mwakhama. (Miyambo 6:​6-8; Aroma 12:11) Koma sikuti limati tizigwira ntchito kwambiri mpaka kufika poika moyo wathu pangozi kapena kulephera kuchita zinthu zinanso zofunika.

Mtsikana wina dzina lake Ashley ananena kuti: “Nthawi ina ndinakhala tsiku lonse osadya kanthu pofuna kuwonetsetsa kuti ndakwanitsa kuchita zonse zomwe ndimafuna kuchita tsiku limenelo. Ndaphunzira kuti ndizitha kukanako zinthu zina chifukwa sibwino kumangovomera ntchito iliyonse yomwe ungapatsidwe mpaka kufika poika moyo wako pangozi.”

Ndipo ndi pomveka kuti Baibulo limanena kuti: “Galu wamoyo ali bwino kuposa mkango wakufa.” (Mlaliki 9:4) Mogwirizana ndi lembali, kudzikakamiza kugwira ntchito zina kungakupangitsenidi kudzimva kuti muli ndi mphamvu ngati mkango. Koma ngati nthawi zonse mumangokhalira kupanikizika chifukwa cha zochita zambiri, mutha kuika moyo wanu pangozi.

Zimene mungachite

  • Muzitha kukana zinthu zina. Baibulo limanena kuti: “Nzeru zimakhala ndi anthu odzichepetsa.” (Miyambo 11:2) Munthu wodzichepetsa amadziwa zomwe sangakwanitse kuchita ndipo savomera kugwira ntchito zambirimbiri.

    Jordan ananena kuti: “Munthu amene amavomera kugwira ntchito iliyonse yomwe wapemphedwa, ndi amene amapanikizika kwambiri. Kumeneko sikudzichepetsa ndipo pakapita nthawi yochepa, amayamba kumva kuti akupanikizika.”

  • Muzipuma mokwanira. Baibulo limanena kuti: “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.” (Mlaliki 4:6) Ambiri amanena kuti tulo ndi mankhwala. Koma achinyamata ambiri sagona maola okwanira. Akatswiri amanena kuti munthu amafunika kugona maola 8 kapena 10 pa tsiku.

    Mnyamata wina dzina lake Brooklyn ananena kuti: “Ndinkalolera kugona kwa maola ochepa ndikakhala ndi zochita zambiri. Koma nthawi zambiri sindinkaganizirako kuti nthawi yotsalayo ndi imene inali yofunikanso kuti ndichite zinthu zolongosoka kukacha.”

  • Muzikhala ndi pulogalamu. Baibulo limati: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira.” (Miyambo 21:5) Mukazolowera kugawa bwino nthawi komanso kudziwa ntchito zomwe mungayambirire kuzigwira, zidzakuthandizani kwa moyo wanu wonse.

    Vanessa ananena kuti: “Munthu amene amakhala ndi pulogalamu sapanikizika kwambiri. Ukamachita zinthu motsatira pulogalamu yomwe wakonza, umadziwa zinthu zimene ungafunike kusintha kuti pamapeto pake usapanikizike kwambiri.”

Zimene achinyamata anzanu amanena

Gianna

Gianna ananena kuti: “Anthu ena amapanikizika ndi zochita zambiri chifukwa chofuna kupanga ndalama. Koma pa 1 Timoteyo 6:8, pamasonyeza kuti tizikhala okhutira ndi zinthu zokhazo zomwe ndi zofunika pa moyo. Mfundoyi ndi yomveka ndipo ndi yothandiza kuti tisamadzichulukitsire zochita komanso kutanganidwa kwambiri ndi zinthu zosafunika.”

Waylon

Waylon ananena kuti: “Ndimaona kuti kukonza pulogalamu ya zomwe ndichite wiki imeneyo kumandithandiza kwambiri. Ndikapanda kutero ndimangovomera ntchito iliyonse imene ndingapatsidwe ndipo zochita zimandichulukira kwambiri. Pamapeto pake ndimapanikizika koopsa ndipo sindipeza mpata wokwanira woti n’kugwira ntchito zina.”

Kara

Kara ananena kuti: “Nthawi zina ukhoza kuona kuti ndi bwino kuvomera kugwira ntchito iliyonse yomwe wauzidwa, n’kumaganiza kuti ukapanda kuvomera siziyenda. Koma ndaphunzira kuti zimenezi si zoona. Munthu amakhala wosangalala komanso wopanda nkhawa akamapeza nthawi yopuma.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena