Bungwe la World Council of Churches Livomerezana Kusagwirizanar
MKATI mwa August 3 mpaka 14, 1993, mzinda wa Santiago, Spain, unalandira gulu la apaulendo wachipembedzo. Mzindawo unali ndi Msonkhano wa Chikhulupiriro ndi Dongosolo wa Dziko Lonse, wochirikizidwa ndi World Council of Churches. Cholinga cha nthumwizo chinali chachikulu—kudzutsa ntchito yozilala ya kugwirizanitsa matchalitchi a Dziko Lachikristu.
Mkhalidwewo unatchedwa “mphwayi ya matchalitchi” yeniyeni ndi Desmond Tutu, akibishopu wa Angilikani wa ku South Africa. “Timanyika miyendo yathu m’madzi, koma timalephera kulimba mtima kuti tidziponyemo,” anadandaula motero.
Kudziponyamo kwa matchalitchi sikudzakhala kwapafupi. Magaŵano pakati pa nthumwizo anaonekera mkati mwa mwambo wotsegulira m’tchalitchi cha Katolika cha Santiago. “Nyimbo Yoimbira St. James,” imene inaimbidwa mkati mwa mwambowo, inasulizidwa kuti inali kutamanda nkhanza za zaka mazana ambiri za Akatolika Achisipanya kwa Ayuda, Asilamu, ndi Aprotesitanti, ngakhale kuti akibishopu Wachikatolika Rouco anali atalimbikitsa oimbawo ‘kuloŵa mumzimu wa apaulendo wachipembedzowo ndi kuyesa kuyanjanitsanso Akristu.’
Kodi pali makonzedwe aliwonse amene angathandize kuyanjanitsa Akatolika, Aorthodox, ndi Aprotesitanti? Gulu lina lofufuza linanena kuti matchalitchi osiyanasiyana amaona Nicene Creed “kukhala liwu lalikulu la chikhulupiriro cha utumwi.” Iwo amakhulupirira kuti chiphunzitso chimenechi chingakhale “njira yopezera mgwirizano wa chikhulupiriro,” ngakhale kuti pangakhale “kusiyanasiyana kwa malongosoledwe.”
“Kusiyanasiyana kwa malongosoledwe” kunaonekera mobwerezabwereza pamsonkhanowo. Nthumwi za Chiorthodox ndi za Chikatolika zinatsutsa chigamulo chaposachedwa cha Angilikani cha kudzoza akazi. Nkhani ina yodzutsa mkangano ndiyo udani waukulu pakati pa matchalitchi a Orthodox ndi Achikatolika m’maiko omwe kale anali Achikomyunizimu. Akibishopu Iakovos wa Tchalitchi cha Greek Orthodox ananena kuti kunali kulakwa kulankhula za “kulalikiranso anthu amene akhala Akristu kwa zaka mazana ambiri” koma amene anali ndi tsoka la kukhala pansi pa Chikomyunizimu chokana Mulungu kwa zaka mazana makumi ambiri. Kwenikweni, lipoti la msonkhanowo linatsutsa “kutembenuza anthu” kukhala chopinga pa chigwirizano, ngakhale kuti silinavomereze kufunika kwa ‘kuzindikira bwino mkhalidwe wa tchalitchi waumishonale.’
Samuel B. Joshua, bishopu wa ku Bombay, analongosola mwachisoni chigwirizano cha matchalitchi kukhala “loto la dziko la mtendere.” Atakumana ndi mavuto okhalapo poyesa kugwirizanitsa mipingo isanu ndi umodzi ya India, iye anati “mapindu ake akhala achiphamaso” pamene kuli kwakuti zothodwetsa zake “zakhala zosapiririka.” Iye amakhulupirira kuti mgwirizano wa Chikristu suyenera kufunidwa “m’ziphunzitso ndi dongosolo la tchalitchi.”
Koma kodi mgwirizano umene umanyalanyaza ziphunzitso ungakhaledi weniweni? Kodi zipembedzo zimene zikulepherabe ‘kumvetsetsa mkhalidwe wa tchalitchi waumishonale’ zingakhale zikutsatiradi Kristu? Paulo anati atsatiri a Kristu oona ayenera kupitiriza kukhala “amtima umodzi.” (2 Akorinto 13:11) Kungovomerezana kusagwirizana kumalephereratu kufika pamuyezo umenewo.