Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 9/8 tsamba 18-19
  • Chimene Analankhulira Mopanda Mantha

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chimene Analankhulira Mopanda Mantha
  • Galamukani!—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Kuvumbula Zoipa za Nazi
    Galamukani!—1995
  • Kodi Inuyo Mumamvera Ndani—Mulungu Kapena Anthu?
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Chimene Matchalitchi Anakhalira Chete
    Galamukani!—1995
  • Sitinachirikize Nkhondo ya Hitler
    Galamukani!—1994
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 9/8 tsamba 18-19

Chimene Analankhulira Mopanda Mantha

POLINGALIRA zakumbuyo, tinganene kuti kulimbana kwa pakati pa Mboni za Yehova ndi Chinazi, kapena chipani cha National Socialism kunali kosapeŵeka. Chifukwa ninji? Chifukwa cha malamulo osasinthika a Anazi amene anawombana ndi zitatu za zikhulupiriro zazikulu za Mboni zozikidwa pa Baibulo. Izo ndi izi: (1) Yehova Mulungu ndiye Mfumu Yaikulu. (2) Akristu oona satenga mbali m’ndale. (3) Mulungu adzaukitsa amene akhala okhulupirika kwa iye kufikira imfa.

Zikhulupiriro zozikidwa pa Baibulo zimenezi ndizo zinachititsa Mboni za Yehova kuchirimika motsutsana ndi malamulo opanda umulungu a Anazi. Motero, izo zinalankhula molimba mtima ndi kuvumbula zoipa za Chinazi.

Mboni za Yehova zinakana kutamanda Hitler. Zinakana chifukwa chakuti chipulumutso chawo chili kwa Mulungu ndipo zapatulira miyoyo yawo kwa iye yekha. Baibulo limati ponena za Yehova: “Inu nokha, . . . ndinu Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.”—Salmo 83:18.

Kwenikweni, kunena kuti “Tamandani Hitler” kunatanthauza kuti chipulumutso chinali kwa Hitler. Chotero Mboni sizikanakhala zokhulupirika kwa Mulungu ndipo panthaŵi imodzimodzi ndi kutamanda munthu aliyense. Miyoyo yawo limodzinso ndi kukhulupirika kwawo ndi kumvera kwawo zinali kwa Mulungu.

Mboni za Yehova zinali ndi zitsanzo zabwino zakale zimene zinakanirapo kumvera zofuna zolakwika za Hitler. Mwachitsanzo, pamene atumwi a Yesu a m’zaka za zana loyamba analamulidwa kuleka kulengeza uthenga wabwino wonena za Kristu, anakana. Iwo anati: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.” Baibulo limanena kuti chifukwa cha kaimidwe kawo kosagwedera, olamulirawo “anawakwapula nawalamulira asalankhule kutchula dzina la Yesu.” Komabe, atumwiwo anakana kumvera lamulo lonyoza Mulungu limenelo. “Sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira.”—Machitidwe 5:29, 40-42.

Akristu oyambirira ambiri anafa chifukwa cha kumvera Mulungu m’malo mwa anthu. Ochuluka anafa m’mabwalo amaseŵera a Roma chifukwa chakuti anakana kutamanda Kaisara mwa kukana kumlambira. Koma kwa anthu otero unali ulemerero ndi chilakiko kwa iwo kusonyeza kukhulupirika kwawo kwa Mulungu kufikira imfa, mofanana ndi msilikali wopanda mantha wokonzekera kufera dziko lake.

Chifukwa chakuti Mboni za Yehova zimachirikiza boma limodzi lokha, Ufumu wa Mulungu, ena aziona kukhala zoukira boma. Komatu sizingachitire mwina. Potsatira chitsanzo cha atumwi a Yesu, izo ‘sizili za dziko lapansi.’ (Yohane 17:16) Sizimaloŵa m’ndale. Chifukwa cha kukhulupirika kwawo kwa Mulungu, zimamvera malamulo a maboma a anthu amene zikukhalamo. Ndithudi, zimapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa ‘kumvera maulamuliro aakulu.’ (Aroma 13:1) Sizinachirikizepo kuukira boma la anthu lililonse!

Komabe, pali malire amene sangalumphidwe zivute zitani. Ndiwo malire pakati pa thayo la Mboni za Yehova kwa munthu ndi thayo lawo kwa Mulungu. Izo zimapereka kwa Kaisara, kapena olamulira a boma, za Kaisara, koma kwa Mulungu zake za Iye mwini. (Mateyu 22:21) Ngati aliyense ayesa kuzilanda chimene chili cha Mulungu, adzalephera.

Bwanji ngati Mboni yauzidwa kuti idzaphedwa? Chabwino, Mboni za Yehova zili ndi chidaliro chosagwedezeka pa mphamvu ya Mulungu ya kuzibwezeretsa ku moyo. (Machitidwe 24:15) Motero, Mboni zili ndi maganizo amodzimodzi amene anali ndi Ahebri atatu m’Babulo wakale. Pamene anawopsezedwa kuti adzaphedwa m’ng’anjo ya moto, anauza Mfumu Nebukadinezara kuti: “Mulungu wathu amene timtumikira akhoza kutilanditsa . . . Koma akapanda kutero, dziŵani, mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu, kapena kulambira fano lagolidi mudaliimikalo.”—Danieli 3:17, 18.

Chotero, monga momwe taonera kale, pamene Hitler anayamba kudzikweza monga mulungu wodziika yekha, nkhondo ya zikhulupiriro inali yosapeŵeka. Lupanga la Ulamuliro wa Nazi linayang’anizana ndi kagulu kakang’ono ka Mboni za Yehova zimene zinalumbira kukhala zokhulupirika kwa Mulungu woona, Mulungu Wamphamvuyonse, Yehova. Komabe, ngakhale nkhondoyo isanayambe, chotulukapo chake chinali chodziŵikiratu.

[Bokosi patsamba 19]

Kukhulupirika mpaka Imfa

WOLFGANG KUSSEROW anali mmodzi wa ophedwa chifukwa chakuti anakhalabe wokhulupirika kwa Mulungu ndipo anakana kuchirikiza Chinazi. Asanadulidwe mutu pa March 28, 1942, analembera makolo ake ndi abale ake kuti: “Monga mwana wanu wachitatu ndi mbale wanu, ndikukusiyani maŵa mmaŵa. Musachite chisoni, pakuti nthaŵi idzafika pamene tidzakhalanso pamodzi. . . . Tidzasangalala chotani nanga panthaŵiyo, pamene tidzakhalanso pamodzi! . . . Tsopano talekanitsidwa, ndipo aliyense wa ife ayenera kuchirimika pachiyeso; tikatero tidzafupidwa.”

Atakhala pafupi kunyongedwa pa January 8, 1941, Johannes Harms analemba m’kalata yake yomaliza kwa atate wake kuti: “Chiweruzo changa cha kunyongedwa chalengezedwa kale ndipo ndakhala womangidwa maunyolo usana ndi usiku—zisindikizo (papepala) nza unyolo wa m’manja . . . Wokondedwa atate, ndikukuchondererani mwa mzimu kuti mukhalebe wokhulupirika, monga ndayesera kukhala wokhulupirika, ndiyeno tidzaonananso. Ndidzakhala ndikulingalira za inu mpaka imfa.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena