Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndiyenera Kupita ku Makonsati a Rock?
Gulu loimba lodziŵika kwambiri likubwera ku tauni yakwanu. Matikiti akutha, motero muyenera kupanga chosankha tsopano. Kodi mudzapezekako?
NYIMBO zabwino mumkhalidwe woyenera zingakhale chinthu chosangalatsa. Ndi iko komwe, Yehova Mulungu anatilenga ndi kukhoza kwa kusangalala ndi nyimbo, ndipo nyimbo za mitundu yosiyanasiyana nzovomerezeka kwa iye.
Pakati pa achichepere ambiri lerolino, kaŵirikaŵiri nyimbo zokondeka kwambiri ndizo za rock m’mipangidwe yake iliyonse yambiri. Ambiri amasangalala nazo kwambiri pamene ziimbidwa namaona eni akewo. Komabe, pakati pa zinthu zina, malipoti a chiwawa ndi khalidwe losalamulirika pa makonsati a rock amadzutsa mafunso aakulu kwambiri kwa achichepere owopa Mulungu. Kodi chimachitika kwenikweni nchiyani pa makonsati a rock? Kodi kungakhale bwino kukapezeka pa imodzi ya makonsatiwo?
Kuyesa Nyimbozo
Choyamba, tiyeni tikambitsirane za nyimbo zenizenizo. Nyimbo zingafotokoze—ndi kusonkhezera—malingaliro ambiri osiyanasiyana. M’nthaŵi za Baibulo, anthu a Mulungu kaŵirikaŵiri anagwiritsira ntchito nyimbo kusonyeza chikondi chawo pa Mulungu. (Salmo 149:3; 150:4) Nyimbo zinagwiritsidwanso ntchito kusonyeza chisangalalo, chikondwerero, ndi chisoni. (Genesis 31:27; Oweruza 11:34; 1 Samuel 18:6, 7; Mateyu 9:23, 24) Komabe, nzachisoni kuti nyimbo sizinali zabwino nthaŵi zonse ngakhale m’nthaŵi za Baibulo. Nyimbo zonyansa, zodzutsa chilakolako cha kugonana ziyenera kukhala zinali ndi mbali pa kusonkhezera Aisrayeli kuchimwa pamene mtunduwo unapanga chigono munsi mwa phiri la Sinai.—Eksodo 32:1-6, 17, 18, 25.
Kunena zoona, nazonso nyimbo za rock zambiri zimasonkhezera zinthu zoipa—chisembwere, anamgoneka, chipanduko, kulambira mizimu. Zimenezi sizimatanthauza kwenikweni kuti muyenera kulekeratu kumvetsera nyimbo, koma Baibulo limauza Akristu “kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani.” (Aefeso 5:10) Motero muyenera kukhala wosankha ndi waluntha ponena za nyimbo.a
Kodi nyimbo zimene mumakonda zimakuyambukirani motani? Kodi zimakupangitsani kukhala wachimwemwe, wabata, kapena wamtendere? Kapena kodi zimakupangitsani kukhala wokwiya, wopandukira, kapena wochita tondovi? Mwamuna wina wachikristu ku Denmark akukumbukira masikuwo pamene anali wokonda nyimbo za heavy metal, mpangidwe wina wa nyimbo za rock. Iye akuti: “Ndinali kuzimvetsera pogwira ntchito. Ndipo ngati ndinalakwitsa kenakake, ndinali kukwiya kwambiri moti ndinkaswa chinthu chimene ndinali kugwirirapo ntchitocho ndi kuchitaya mwaukali!” Wachichepere wina anavomereza kuti: “Ndinkamvetsera kwambiri nyimbo za rap ndi heavy metal zimene zinalemekeza kugonana ndi moyo wakudziko. Nyimbo zimenezi zinaloŵa m’maganizo mwanga, ndipo chotulukapo chake chinali kukhumba zinthu zimene anali kuimba.” Tsopano ngati nyimbo zongojambulidwa zingakhale ndi zotulukapo zotero, talingalirani za chisonkhezero cha kuonerera oimbawo akumaimba!
Talingaliraninso: Kodi nyimbozo zidzakhala ndi phokoso lotani? Inde, anthu ali ndi zosankha zosiyanasiyana pankhaniyi. Ndipo Baibulo silimaletsa nyimbo za mawu aakulu moyenerera. Eya, pa kupatulira kwa kachisi wa Solomo, owomba malipenga okha anali 120! (2 Mbiri 5:12) Zimenezo ziyenera kukhala kuti zinalidi za mawu aakulu omveka bwino! Komabe, pali kusiyana kwakukulu pakati pa kufuula kwakukulu kwa chitamando kwa Mulungu ndi nyimbo za rock zogonthetsa m’kutu. M’zotchulidwa pomalizazo, kukwera kwa mawu kaŵirikaŵiri kumagwiritsiridwa ntchito kusonkhezera khamulo kuloŵa mumzimu wa kunyanyuka. Koma Baibulo limatsutsa “mapwando aphokoso,” (NW) kapena “mapwando osalamulirika” (Agalatiya 5:21; Byington) Ndipo kulemekeza thupi lanu sikungafune kumvetsera nyimbo za mawu aakulu kwambiri moti nkuwononga makutu anu.—Aroma 12:1.
Mfundo ina yofunika kuganizira yanenedwa pa Yobu 12:11. Pamenepo Baibulo limafunsa kuti: “M’kutumu simuyesa mawu, monga m’kamŵa mulaŵa chakudya chake?” Mogwirizana ndi zimenezi, muyenera ‘kuyesa’ mawu anyimbo! Mkristu wina wachichepere akuvomereza kuti: “Ndinayamba kumvetsera mawu a nyimbo zina zimene ndinali kukonda, koma ndinadabwa kuti sizinali zabwino kwa Mkristu kumazimvetsera. Ndinakuona kukhala kwanzeru kutaya nyimbozo.” (1 Akorinto 14:20; Aefeso 5:3, 4) Dziŵaninso, pasadakhale kuti oimba ambiri amagwiritsira ntchito makonsati kudziŵikitsira nyimbo zawo zatsopano—nyimbo zimene zingakhale zosiyana kwambiri ndi nyimbo zawo zakale, mwinamwake zimene zinali zabwinopo.
Ndiponso, muyenera kutsimikizira kuti nyimbozo zilibe malingaliro auchiŵanda—chinthu chodziŵika bwino kwambiri mu nyimbo za heavy metal. Oimba nyimbo za heavy metal ngodziŵika chifukwa cha kukometsera zovala zawo ndi ma alabamu awo ndi zizindikiro zauchiŵanda ndi zinthu zina zosiyanasiyana zausatana. (Yakobo 3:15) Kupita ku konsati ya gulu lotero sikungakondweretse Mulungu, amene amatilamula ‘kukaniza Mdyerekezi’!—Yakobo 4:7.
Kusalamulirika
Kodi chingachitike nchiyani pa konsatipo? Mtsikana wina wotchedwa Stacey anapita ndi anzake kukaonerera gulu loimba limene analingalira kuti linali kuimba nyimbo zabwino. Koma pakati pa konsatiyo, wotsogolera gululo anafanizira msonkhano wolankhula ndi mizimu napempha onse opezekapo kugwirizana naye m’kuyesa kulankhula ndi mizimu! Nthabwala chabe? Mwinamwake. Koma popeza kuti Baibulo limatsutsa kulambira mizimu m’njira ina iliyonse, Stacey ndi anzake anakakamizika kutulukamo.—Levitiko 19:31; Deuteronomo 18:10-13; Chivumbulutso 22:15.
Achichepere ena achikristu akumanapo ndi zochitika zoipa zofananazo, popeza pamene kuli kwakuti kulambira mizimu koonekeratu sikungapezekepezeke pa makonsati a rock, kusalamulirika kwa anthu nkofala. Pa konsati ina gulu loimba linathandizira kusonkhezera chipolowe chimene chinavulaza anthu 60 ndi kuwononga zinthu za mtengo woposa pa $200,000! Pa konsati inanso, achichepere atatu anaphedwa. Zoona, makonsati ambiri a rock samathera m’zipolowe, kuvulazidwa kwa anthu, kapena imfa. Koma pali kufunika kosakayikirika kwa chenjezo. Miyambo 22:3 imati: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.”
Motero ngati mungaganize zopita ku konsati, dziŵani zoonadi. Kodi gululo lili ndi mbiri ya kusonkhezera anthu kuloŵa m’mkhalidwe wakusalamulirika? Kodi ndi anthu a mtundu wotani amene amakonda gululo? (1 Akorinto 15:33) Kodi zakumwa zoledzeretsa ndi anamgoneka zimagwiritsiridwa ntchito kufikira pati? Ndiponso bwanji ponena za holo ya konsatiyo? Kodi yakhalapo ndi mavuto a kupanda chisungiko kumbuyoku? Kodi makhalidwe m’mipando adzakhala otani? Ngati anthu adzangokhala chikhalekhale, ngozi yakuti wina angapwetekedwe imakhala yaikulu kwambiri.
Anamgoneka ndi zakumwa zoledzeretsa nzofala pa makonsati a rock. “Anthu samadzera nyimbo,” anatero mwamuna wina wachikristu wogwiritsidwa mwala amene anapita ku konsati ya gulu loimba classic rock. “Amadza kudzaledzera.” Anasankha konsati ya rock imeneyo kukhala yomaliza kufikapo. Mtsikana wina wachikristu mofananamo akunena kuti: “Ndikukumbukira ndikupita ku konsati imene gulu ‘loimba zochitika zamakono’ linali kuyimba. Zinali zochititsa mantha! Anthu anali kusuta chamba. Malankhulidwe anali oipa, ndipo ambiri kumeneko anali kuoneka ngati olambira Satana chifukwa cha mavalidwe awo.” Ngakhale kumene anamgoneka ndi zakumwa zoledzeretsa zili zoletsedwa mwamphamvu, si kwachilendo kuona ambiri mwa oonerera akufika ataledzera kale. Kodi kupita kuchochitika chonga chimenecho kungakhale kogwirizana ndi lamulo la Baibulo la ‘kukana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, ndi kukhala ndi moyo m’dziko lino odziletsa’?—Tito 2:12.
Chiyambukiro cha Mkhalidwe Wokuzingani
Komabe, mungalingalire kuti palibe chifukwa chodera nkhaŵa ponena za zimene awo okuzingani akuchita malinga ngati simuchita nawo chiwawacho. Komabe, mkhalidwe wokuzingani umakuyambukirani. Pa Aefeso 2:2, Baibulo limanena za “ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera.” Onani kuti dzikoli lili ndi “mzimu,” kapena njira yofala ya kalingaliridwe. Uli ponseponse, wopezeka paliponse monga mpweya weniweniwo. Koma onaninso kuti mzimu umenewu, kapena kalingaliridwe, uli ndi “ulamuliro”—mphamvu yosintha maganizo anu, malingaliro anu, ndi khalidwe—ngati mudziloŵetsa mu uwo! Simungangopuma mpweya wamphamvu umenewu ndi kusayambukiridwa.
M’zochitika zambiri, pa makonsati a rock m’pamene pamakhala mzimu wa dziko wochuluka kwambiri. Munthu akhoza kuloŵa mosavuta mumkhalidwe wachiwawa umene umakhalapo—kapena m’kufuula ndi kutukulira manja m’mwamba kumene sikungasiyanitsidwe kwenikweni ndi ulemu wa kulambira oimbawo. Ulemu wopyola malire wotero umatsutsana ndi ulemu umene moyenerera uyenera kukhala wa Mulungu. Zimakhala kulambira mafano, chinthu chotsutsidwa momvekera bwino m’Malemba. (1 Akorinto 10:14; 1 Yohane 5:21) Kodi mukufuna kudziika pa ngozi ya kuloŵa m’zimenezi?
Kunena kuti makonsati ambiri a rock amaloŵetsamo ngozi zazikulu kuposa mapindu aliwonse amene munthu angapeze mwa kupitako nkosatsutsika. Zoonadi, makolo anu ndiwo angapange chosankha chomaliza chakuti kaya mungapite ku konsati yakutiyakuti kapena ayi. Koma ngati inu mwini muli ndi ufulu wa kudzipangira chosankha, sankhani mwanzeru. Pali njira zambiri zimene mungasangalale nazo zimene zili zabwino ndipo zilibe ngozi za kupita ku makonsati a rock.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani za “Achichepere Akufunsa Kuti . . .” zonena za nyimbo zopezeka m’magazini a Galamukani! a February 8, March 8, ndi April 8, 1993.
[Chithunzi patsamba 16]
Moŵa, anamgoneka, ndi kakhalidwe kosalamulirika nzofala pa makonsati a rock