Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 6/8 tsamba 11-13
  • Ntchentche ya Kambalame—Ndi Tsoka la Afirika Kodi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ntchentche ya Kambalame—Ndi Tsoka la Afirika Kodi?
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zimadya Mwazi
  • Imapha Nyama
  • Imapha Anthu
  • Mawu Oitetezera
  • Kaulukidwe Kodabwitsa ka Ntchentche
    Kodi Zinangochitika Zokha?
  • Matenda Ofalitsidwa Ndi Tizilombo Akuvutitsa Kwambiri
    Galamukani!—2003
  • Khungu la mu Mtsinje Kugonjetsa Mliri Wowopsawo
    Galamukani!—1995
  • Timapiko ta Ntchentche
    Galamukani!—2012
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 6/8 tsamba 11-13

Ntchentche ya Kambalame—Ndi Tsoka la Afirika Kodi?

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU NIGERIA

TINALI titangosamukira kumene ku dera lina lakumidzi ku West Africa. Tinazingidwa ndi nkhalango yakumalo otentha. Masana ena mkazi wanga anapita ku wadirobu nafuula kuti: “Maine chimphanga kuno!”

Ntchentcheyo inathaŵa mu wadirobumo ndi kuloŵa m’chipinda chosambira. Ndinatenga chitini cha mankhwala ophera tizilombo ndi kuilondola, ndikumatseka chitseko kumbuyo kwanga. Ntchentcheyo inasoŵa. Mwadzidzidzi inaulukira kumaso kwanga. Ikundiluma! Poikupa, ndinalephera kuigwetsera pansi. Inaulukira pazenera. Inatsekerezedwa ndi sikirini. Ntchentcheyo inatera pamenepo.

Ndinainenekera ndi kuipopera ndi mankhwalawo. Kaŵirikaŵiri kupopera mankhwala kwachindunji konga kumeneko kumapha pafupifupi kachilombo kalikonse. Komatu osati ntchentcheyi. Inauluka nipitiriza kulira m’chipinda chosambiramo.

Ha, imeneyi njolimbadi! Ndinali ndi chikhulupiriro chakuti mankhwalawo adzagwira ntchito ndipo ntchentcheyo idzagwera pansi msanga. Komatu sinagwe. Itateranso, ndinaipoperanso mankhwala. Inaulukanso.

Kodi imeneyi ndi ntchentche ya mtundu wanji? Ndinawonjezeranso kupopera kaŵiri ndipo potsirizira pake ndinaipha.

Ndinavala magalasi ndi kuipenda mosamalitsa. Inali yaikulu kuposa ntchentche wamba ya m’nyumba, ngakhale kuti sinali yaikulu monga chimphanga. Mapiko ake anali opingasana kumsana, ikumaoneka kukhala yosiyana kwambiri ndi ntchentche wamba. Chaso chake chachitali chonga singano chinachokera chapakamwa pake.

Ndinauza mkazi wanga mofuula kuti: “Chimenechi si chimphanga. Ndi kambalame.”

Chochitikacho chinandichititsa kumvetsetsa vuto la kuyesa kuthetsa ntchentchezo m’malo ake a mu Afirika a makilomita 11.7 miliyoni monsemonse, dera lalikulu kuposa lija la United States. Kodi nchifukwa ninji anthu amafuna kuzithetsa? Amaziimba milandu itatu. Mlandu woyamba:

Zimadya Mwazi

Pali mitundu 22 yosiyanasiyana ya ntchentche za kambalame. Yonseyo imakhala ku dera la kumunsi kwa Sahara mu Afirika. Zonse zimene, zazimuna ndi zazikazi, zimayamwa mwazi wa zolengedwa zokhala ndi fupa la msana, zikumatsopa mwazi wochuluka kuŵirikiza katatu kulemera kwawo pamene ziluma kamodzi nkamodzi.

Zimaluma nyama zosiyanasiyana zodya udzu—za mu Afirika ndi zimene sizili za mu Afirika zomwe. Zimalumanso anthu. Kulumako kumakhala kwakukulu, kubaya kotsopa magazi, kolasa ndi kopweteka. Kumanyerenyetsa ndi kupweteka panthaŵi imodzimodziyo. Kumatulutsa nsungu.

Ntchentche za kambalame nzaluso pa ntchito yake. Sizimataya nthaŵi ndi kulira mozungulira mutu wanu. Zitha kuulukira pa wina monga ngati chipolopolo ndi kuima mwanjira ina ndi kutera kumaso bwinobwino kwakuti munthu sangamve. Zingathe kukhala ngati mbala; nthaŵi zina inu simungadziŵe kuti zaba magazi anu ena kufikira zitapita—pamene chotsalira kwa inu ndicho kuona chivulazo chake.

Kaŵirikaŵiri zimakonda thupi losaphimbidwa. (Zichita ngati kuti zimakonda kuseri kwa khosi langa!) Komabe, nthaŵi zina, zimasankha kuloŵa m’mwendo wa buluku kapena mumkono wa shati zisanayambe kutsopa mumtsempha wa mwazi. Kapena ngati zasankha, zingathe kuluma kupyola pa chovala—si vuto kwa kachilombo kamene kangaboole ngakhale chikumba cholimba cha chipembere.

Anthu samangoimba mlandu ntchentche ya kambalame wa kukhala yanzeru chabe komanso yamachenjera. Tsiku lina pamene ndinayesa kupha ina ndi mankhwala, inaloŵa m’wadirobu yanga ndi kubisala m’zovala zanga zosambira. Patapita masiku aŵiri pamene ndinavala zovala zangazo, inandiluma kaŵiri! Panthaŵi ina ntchentche ya kambalame inabisala m’chikwama cha ndalama cha mkazi wanga. Anapita ndi chikwamacho ku ofesi, ndipo pamene anapisamo dzanja, ntchentcheyo inaluma dzanja lake. Ndiyeno inaulukauluka m’chipindamo, ikumasokoneza ogwira ntchito mu ofesimo. Aliyense anasiya ntchito akumayesa kuipha.

Chotero mlandu woyamba pa ntchentche ya kambalame ngwakuti ili yotsopa magazi mwa kuluma momvetsa ululu. Mlandu wachiŵiri:

Imapha Nyama

Mitundu ina ya ntchentche za kambalame imapereka nthenda yochititsidwa ndi tizilombo totchedwa kuti ma trypanosome. Pamene ntchentche ya kambalame itsopa magazi a nyama imene ili ndi nthendayo, imameza mwazi wokhala ndi tizilomboto. Timeneti timakula ndi kuswana mkati mwa ntchentcheyo. Pamene ntchentcheyo iluma nyama ina, tizilombo timaperekedwa ndi ntchentcheyo kuloŵa m’mwazi wa nyamayo.

Nthendayo ndiyo trypanosomiasis. Mtundu umene umakhala m’nyama umatchedwa kuti nagana. Tizilombo ta nagana ntambiri m’mwazi wa nyama zambiri za mu Afirika, makamaka nswala, njati, nguluwe, agwape, mphoyo, ndi akaphulika. Tizilomboto sitimapha nyama zimenezi.

Koma tizilomboto timasakaza zifuyo zimene sizili za mu Afirika—ngamila, agalu, abulu, mbuzi, akavalo, nyulu, ng’ombe, nkhumba, ndi nkhosa. Malinga ndi magazini a National Geographic, nagana imapha ng’ombe mamiliyoni atatu chaka chilichonse.

Oŵeta ng’ombe, monga ngati Amasai a ku East Africa, aphunzira mmene angapeŵere madera amene kuli ntchentche za kambalame zambiri, komano chirala ndi kusoŵa kwa malo odyera ng’ombe nthaŵi zina zimapangitsa zimenezi kukhala zosatheka. Mkati mwa chirala chaposachedwapa, mabanja anayi amene anali kuŵeta ng’ombe zawo 600 pamodzi anali kutayikiridwa ng’ombe imodzi pa tsiku chifukwa cha ntchentcheyo. Lesalon, mkulu wina m’banja pakati pawo, anati: “Amasaife ndife anthu olimba mtima. Timalasa mkango ndi nthungo ndi kulimbana ndi njati. Timapha njoka ya mamba ndi kulimbana ndi njovu yaukali. Koma bwanji ponena za orkimbai [ntchentche ya kambalame]? Timasoŵa chochita.”

Pali mankhwala ochiritsira nagana, koma maboma ena amangolola kuwagwiritsira ntchito moyang’aniridwa ndi wavetenale chabe. Pali chifukwa chabwino chochitira zimenezo, popeza kuti milingo yosakwanira singangopha chifuyocho chabe komanso kuyambitsa tizilombo tosamva mankhwala. Kungakhale kovuta kwa woŵeta ng’ombe wakumidzi kupeza wavetenale panthaŵi yake kuti adzachiritse zifuyo zake zodwala kwambiri.

Milandu iŵiri yoyamba pa ntchentche ya kambalame yasonyezedwa popanda mtsutso—imadya magazi ndi kuwanditsa nthenda imene imapha zifuyo. Koma pali zina. Mlandu wachitatu:

Imapha Anthu

Anthu samadwala nagana trypanosome. Koma ntchentche ya kambalame imatenga mwa munthu ndi kupereka kwa munthu wina mtundu wina wa trypanosome. Mtundu umenewu wa trypanosomiasis umatchedwa kuti nthenda ya kaodzera. Musaganize kuti munthu wodwala nthenda ya kaodzera amangogona kwambiri. Nthendayo sili yogonetsa munthu tulo mwachisangalalo. Imayamba mwa kufoola munthu, kumtopetsa, ndi malungo pang’ono. Pambuyo pake pamadza kuodzera kosatha msanga, malungo aakulu, kuphwanya mumfundo, kutupa minyewa, ndi kukula chiŵindi ndi kapamba. Itafika poipa, pamene tizilomboto tikuloŵerera mu ubongo ndi m’fupa la msana, wodwalayo amasokonezeka maganizo, amadwala kowopsa, kukomoka, ndi kufa.

Kumayambiriro kwa zaka za zana lino, mliri wa nthenda ya kaodzera unawononga kontinenti ya Afirika. Pakati pa 1902 ndi 1905, nthendayo inapha anthu pafupifupi 30,000 pafupi ndi Lake Victoria. M’zaka makumi ambiri zimene zinatsatira, nthendayo inafalikira kuloŵa mu Cameroon, Ghana, ndi Nigeria. M’midzi yambiri munthu mmodzi mwa atatu anagwidwa nayo, zikumachititsa kusamuka kwa anthu ochuluka kuchoka m’mbali mwa mitsinje yambiri. Magulu oyenda opereka thandizo anachiritsa anthu mazana zikwi zambiri. Ndi kufikira kumapeto kwa ma 1930 pamene mliriwo unazimiririka ndi kutha.

Lerolino nthendayo imasautsa anthu pafupifupi 25,000 chaka chilichonse. Malinga ndi kunena kwa World Health Organization, anthu oposa 50 miliyoni m’maiko 36 a kumunsi kwa Sahara ali pangozi ya kugwidwa ndi nthendayo. Ngakhale kuti nthenda ya kaodzera njakupha ngati siichiritsidwa, mankhwala oichiritsira alipo. Posachedwapa mankhwala otchedwa kuti eflornithine anapangidwa kuchiritsira nthendayo—mankhwala oyamba otero m’zaka 40.

Anthu amenya nkhondo kwa nthaŵi yaitali molimbana ndi ntchentche ya kambalame ndi nthenda imene imanyamula. Mu 1907, Winston Churchill analemba za mkupiti wa kuthetsa ntchentche ya kambalame kuti: “Akuilukira ukonde wabwino kwambiri mosalekeza, kuti isafalikire.” Pokumbukira zimenezo, kuli kwachionekere kuti “ukonde wabwino kwambiri” wa Churchill unali ndi ziboo zazikulu. Buku lakuti Foundations of Parasitology likunena kuti: “Kufikira pano, zaka 80 za kuthetsa ntchentche za kambalame sizinathandize kwenikweni kuletsa kuswana kwa kambalame.”

Mawu Oitetezera

Wolemba ndakatulo wa ku America Ogden Nash analemba kuti: “Mulungu mu nzeru Yake anapanga ntchentcheyo, naiŵala kutiuza chifukwa chake.” Pamene kuli kwakuti nzoona kuti Yehova Mulungu ndiye Mlengi wa zinthu zonse, ndithudi si zoona kunena kuti amaiŵala. Amalola kuti tidzitumbire tokha zinthu zambiri. Bwanji nanga za ntchentche ya kambalame? Kodi tinganene kanthu kena kotetezera mpandu wachionekere ameneyu?

Mwinamwake chitetezero chake champhamvu koposa nchakuti kuwononga kwake ng’ombe kwatetezera nyama zakuthengo za mu Afirika. Madera aakulu a Afirika ngofanana ndi madambo akumadzulo kwa United States—okhoza kudyetsa zifuyo. Koma chifukwa ntchentche za kambalame, zifuyo zimaphedwa ndi trypanosomes imene simapha nyama zakuthengo zodya udzu za mu Afirika.

Ambiri amakhulupirira kuti kukanapanda ntchentche za kambalame, nyama zakuthengo zochuluka za mu Afirika zikanakhala zitalandidwa malo kalekale ndi magulu a ng’ombe. “Ndimachirikiza kambalame,” anatero Willie van Neikerk, woonetsa nyama m’malo a nyama zakuthengo ku Botswana. “Thetsani kambalame ndipo ng’ombe zidzalanda malo, ndipo ng’ombezo zili owononga mu Afirika, zikumasakaza kontinentiyi kukhala yoguga.” Anawonjezera kuti: “Ntchentchezo ziyenera kukhalapo.”

Zoonadi, si onse amene akuvomerezana ndi zimenezo. Chifukwacho sichimasangalatsa munthu amene akuona ana ake kapena ng’ombe zikudwala trypanosomiasis. Ndiponso sichimasangalatsa aja amene amanena kuti Afirika afunikira kukhala ndi ng’ombe kuti adzidyetse.

Komabe, mosakayikira pakali zambiri zoti tiphunzire ponena za ntchito imene ntchentche ya kambalame imachita m’chilengedwe. Ngakhale kuti milandu yake ikuoneka kukhala yaikulu, mwinamwake kuweruziratu nkufulumira.

Ponena za ntchentchezo, imodzi yangoulukira kumene m’chipinda muno. Ndiloleni ndionetsetse ngati isali kambalame.

[Mawu a Chithunzi patsamba 11]

Kambalame: ©Martin Dohrn, The National Audubon Society Collection/PR

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena