Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 11/12 tsamba 11
  • Timapiko ta Ntchentche

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Timapiko ta Ntchentche
  • Galamukani!—2012
  • Nkhani Yofanana
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2012
  • Kaulukidwe Kodabwitsa ka Ntchentche
    Kodi Zinangochitika Zokha?
  • Ntchentche ya Kambalame—Ndi Tsoka la Afirika Kodi?
    Galamukani!—1996
  • Ntchentche Zonyansazo—kodi Zili Ndi Ntchito Imene Simumaganizirapo?
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—2012
g 11/12 tsamba 11

Kodi Zinangochitika Zokha?

Timapiko ta Ntchentche

Kodi n’chiyani chimathandiza kuti ntchentche izitha kusintha mosavuta kumene ikulowera komanso kuti izitha kudzitembenuza kwinaku ikuuluka? Kodi imatha bwanji kuulukabe bwinobwino ngakhale itakumana ndi mphepo yamphamvu? Chomwe chimathandiza kuti ntchentche izitha kuchita zimenezi ndi timapiko tiwiri tooneka ngati kachibonga tomwe timakhala kunsi kwa mapiko enieni.a

Taganizirani izi: Ntchentche ikamauluka, timapiko timeneti timasuntha mogwirizana ndi mmene mapiko a ntchentcheyo akukupizira. Komabe timasiyana pang’ono ndi kayendedwe ka mapiko enieniwo chifukwa mapikowo akakwera, timapikoti timatsika. Asayansi atulukira kuti timapikoti timagwira ntchito ngati kachipangizo kenakake kothandiza kudziwa malo amene ndege kapena galimoto ili.b

Buku lina linanena kuti: “Kaphiko kalikonse kakamakupiza kamakwera m’mwamba kenako n’kubwerera ngati mmene umachitira muvi wa [sikelo].” (Encyclopedia of Adaptations in the Natural World) Bukuli linafotokozanso kuti ntchentche ikatembenuzika pouluka, mwina mwadala kapena chifukwa chokankhidwa ndi mphepo, “timapikoti timapindika. Kenako timinyewa ta timapikoti timatumiza uthenga ku ubongo, zomwe zimathandiza ntchentcheyo kudziwa kuti ikhoza kugwa kapena kuomba chinachake.” N’chifukwa chake ntchentche zimakhala zochenjera komanso zovuta kuzigwira.

Akatswiri a zopangapanga akuona kuti pali zinthu zambiri zimene angapange potengera mmene timapiko timeneti timagwirira ntchito. Zinthu zimenezi ndi monga makina ogwira ntchito ngati anthu komanso zombo zoyenda m’mlengalenga. Wasayansi wina, dzina lake Rafal Zbikowski, ananena kuti: “N’zodabwitsa kuti kachilombo konyozeka ngati kameneka kakutiphunzitsa zinthu zambiri chonchi.”

Kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika zokha kuti timapiko ta ntchentche timeneti tizichita zinthu zogometsa chonchi kapena alipo amene anatilenga?

a Tizilombo ta mapiko awiri monga ntchentche ndi udzudzu ndi tomwe timakhala ndi timapiko timeneti.

b Nthawi zambiri kachipangizoka kamakhala ndi kagudumu komwe kamazungulira mofulumira pakachitsulo kena. Kagudumuka sikasiya kuzungulira ngakhale mutamakasunthasuntha kapena kukazondotsa. N’chifukwa chake kachipangizo kameneka kamagwiritsidwanso ntchito kupangira makampasi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena