Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 7/8 tsamba 3-4
  • Mudzi wa Dziko Lonse Koma Wogaŵanikabe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mudzi wa Dziko Lonse Koma Wogaŵanikabe
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mitundu Ikumana
  • Chimene Anthu Amakhalirabe Ogaŵanikana
  • Kodi Kudana ndi Anthu Amitundu ina N’koyenera?
    Galamukani!—2003
  • Kodi Tsankho Lingathe Bwanji?
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kugwetsa Makoma ndi Kumanga Maulalo
    Galamukani!—1996
  • Kodi Dziko Lingagwirizanitsidwe?
    Galamukani!—1994
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 7/8 tsamba 3-4

Mudzi wa Dziko Lonse Koma Wogaŵanikabe

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU  NIGERIA

KODI munamvapo nthano za fuko la anthu amene analibe kamwa ndipo chotero sanali kudya ndi kumwa? Anthu ankanena kuti iwo anali kukhala ndi moyo mwa kununkhiza, makamaka maapulo. Fungo loipa linali kuwapha.

Panalinso nkhani zonena za anthu a ku West Africa amene anali ndi golidi wogulitsa. Kazembe wa bwato la apwitikizi wa panthaŵiyo anati: ‘Pamtunda wa ma league mazana aŵiri kudutsa ufumu wa [Mali], munthu amapezako dziko limene anthu ake ali ndi mitu ndi mano a galu ndi michira ngati agalu. Ameneŵa ndiwo Anthu Akuda amene amakana kukambitsirana chifukwa safuna kuonana ndi anthu ena.’ Amenewo anali ena a malingaliro achilendo amene anthu anali nawo zaka zambiri zapitazo, nyengo ya maulendo ndi kutumba malo isanayambe.

Mitundu Ikumana

Anthu anakhulupirira nkhani zimenezo zaka mazana ambiri. Koma pamene oyendera malo anazonda pulanetili, sanapeze anthu opanda kamwa onunkhiza maapulo kapena anthu amitu ya agalu. Lerolino palibe chinsinsi ponena za amene amakhala kumaiko ena. Dziko lakhala mudzi umodzi. Wailesi yakanema imabweretsa maiko akutali ndi anthu ake m’chipinda chathu chochezera. Maulendo apandege amatheketsa kuchezera maikowo m’maola ochepa; anthu mamiliyoni amatero chaka chilichonse. Ena ali paulendo pazifukwa za chuma kapena ndale. Lipoti la United Nations Population Fund linati: “Pamlingo waukulu koposa m’mbiri—umenetu udzawonjezeka—anthu padziko lonse akuchoka ndi kusamuka pofunafuna moyo wabwino.” Pafupifupi anthu 100 miliyoni akukhala kunja kwa maiko omwe anabadwirako.

Pali kudalirana komawonjezereka pa zachuma pakati pa mitundu. Njira yolankhulirana padziko lonse, monga minyewa ya ubongo ndi fupa la msana, imalunzanitsa mtundu uliwonse padziko lapansi. Pamene asinthana malingaliro, chidziŵitso ndi tekinoloji, miyambo imagwirizana ndi kulolerana. Padziko lonse anthu amavala zofanana kuposa ndi kale lonse. Mizinda ya dziko njofanana kwambiri—ili ndi apolisi, mahotela ambambande, misewu, masitolo, mabanki, kuipitsa. Chifukwa chake, pamene mitundu ya dziko lonse ikumana, timaona chimene ena atcha mwambo wa dziko lonse umene ukupangika.

Chimene Anthu Amakhalirabe Ogaŵanikana

Koma pamene mitundu ndi miyambo imaloŵerana, mwachionekere si onse amene amaonana ngati abale. “Aliyense amafulumira kuimba mlandu mlendo,” analemba motero wolemba maseŵero wachigiriki zaka zoposa 2,000 zapitazo. Mwachisoni, zinthu ndi mmenenso zilili lerolino. Umboni sumavuta kuona m’nkhani za nyuzipepala zokhudza liuma, kuda alendo, “kuyeretsa fuko,” kulimbana kwa mafuko, zipolowe zachipembedzo, kupulula anthu wamba, mabwalo opherako anthu, misasa yogwirira chigololo, kuzunza, kapena kupululutsa fuko.

Ndithudi, ife ambiri tingachite zochepa ngati tingathe nkomwe kusintha kulimbana kwa mafuko. Mwina sitingakhudzidwe nako nkomwe mwachindunji. Komabe, ambiri a ife timapezana ndi mavuto chifukwa cha kulephera kulankhulana ndi alendo amene timakumana nawo—achinansi, anzathu a kuntchito, kapena anzathu a kusukulu.

Kodi sizimaoneka zachilendo kuti anthu a mafuko osiyana nthaŵi zambiri kumawavuta kukhulupirirana ndi kuyamikirana? Ndi iko komwe, pulaneti lathu lili ndi zinthu zamitundumitundu zosatha. Ochuluka a ife tiyamikira kuchuluka kwa zakudya zamitundumitundu, nyimbo, ndi maonekedwe ndiponso mitundu yambiri ya zomera, mbalame, ndi nyama. Komatu kuyamikira kwathu zinthu zamitundumitundu sikumaphatikizapo anthu nthaŵi zonse amene amaganiza ndi kuchita zinthu mosiyana ndi ife.

M’malo moyang’ana pa mbali zabwino za kusiyanasiyana kwa anthu, ambiri amakonda kusumika maganizo pa kusiyanako ndi kukupanga kukhala nkhani ya mkangano. Nchifukwa ninji zili choncho? Kodi kuli ndi phindu lanji kuyesetsa kulankhulana ndi anthu amene miyambo yawo imasiyana ndi yathu? Kodi tingagwetse motani makoma opinga kulankhulana ndi kumangapo maulalo? Nkhani zotsatira zidzapereka mayankho a mafunso amenewo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena