Kuphana m’Dzina la Mulungu
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU FRANCE
“Timaphana m’Dzina la Mulungu, Ndipo Tidzaphanabe”
PAMUTU wa nkhani umenewu, nyuzipepala ya International Herald Tribune inati: “Zaka za zana lino, zomwe oyembekeza zabwino okhalako apa ndi apo amakonda kuona ngati zomasuka paumbuli, zakhala ndi mzimu woopsa wakuti anthu nkumaphana okhaokha m’dzina la Mulungu mofanana ndi zaka za mazana apitawo.”
Mlembi wake anatchula zitsanzo za kupululana kwa anthu a zipembedzo. Ndiyeno, atasonyeza kupululana kumene kwachitika m’zaka za zana la 20 zino, anati: “Zomwe tikuzionazi zangokhala kupitiriza kwa nkhalwe yoopsa yosalolerana ya m’nyengo zapita. Chiwawa m’ndale ndi kulimbirana malire zikuchitika chifukwa cha chipembedzo.”
Ena amayesa kunena kuti nkhondo zalero za zipembedzo zili bwino popeza ngakhale Mulungu analola Aisrayeli akale kupha Akanani. Koma sikuti zimenezo zimalungamitsa nkhondo zomenyedwa ndi odzitcha Akristu lerolino. Chifukwa ninji? Chifukwa Aisrayeli Mulungu anawauza mwachindunji kupereka chiweruzo chake cholungama pa anthu amenewo olambira ziŵanda, amene kulambira kwawo kunaphatikizapo chisembwere chonyansa ndi kupereka ana nsembe.—Deuteronomo 7:1-5; 2 Mbiri 28:3.
Umboni wakuti nkhondo za Israyeli wakale sizinali nkhondo wamba ayi ndiwo zilakiko zozizwitsa zimene Mulungu anapatsa mtunduwo. Mwachitsanzo, nthaŵi ina Aisrayeli akale anauzidwa kugwiritsira ntchito malipenga, mitsuko, ndi miyuni—zimene sizili zida za nkhondo nkomwe! Nthaŵi inanso anaika oimba kutsogolo kwa gulu la nkhondo la Aisrayeli amene anayang’anizana ndi makamu ochuluka a magulu a nkhondo a mitundu ingapo.—Oweruza 7:17-22; 2 Mbiri 20:10-26.
Ndiponso, pamene Aisrayeli nthaŵi ndi nthaŵi anamenya nkhondo zosalamulidwa ndi Mulungu, iye sanawadalitse ndipo anagonjetsedwa. (Deuteronomo 28:15, 25; Oweruza 2:11-14; 1 Samueli 4:1-3, 10, 11) Chifukwa chake, nkhondo za Israyeli sizingagwiritsiridwe ntchito kulungamitsa nkhondo zomenyedwa m’Dziko Lachikristu.
M’dzina la chipembedzo, Ahindu athirana nkhondo ndi Asilamu ndi Asiki; Asilamu achishiaiti athirana nkhondo ndi achisuni; ndipo ku Sri Lanka, Abuda ndi Ahindu aphana.
Nkhondo zomwe zinachitika ku France m’zaka za zana la 16 zili chitsanzo chabwino cha anthu ophana m’dzina la Mulungu. M’nkhondo zina zimenezi munali kukhetsa mwazi koopsa kumene sikunachitikepo m’mbiri ya chipembedzo cha Roma Katolika ndi Chiprotesitanti ku Ulaya. Tiyeni tipende nkhondo zimenezi, ndi kuona zimene tingaphunzirepo.
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
U.S. Army Photo