Kusintha Maganizo Kubutsa Nkhani Zatsopano
“KUSINTHA MAGANIZO PA ZAKUGONANA,” “kutengeka mtima ndi zakugonana,” “kusintha maganizo pa makhalidwe.” Mawu ngati ameneŵa anasonyeza kusintha maganizo pa zakugonana, makamaka chapakati pa ma 1960 ndi zaka zotsatirapo. Ambiri anayamba kugwiritsira ntchito mawu akuti “kugonana kwaufulu,” amene anasonyeza moyo wa anthu omwe anakana ukwati ndi unamwali.
Chikalata chosonyeza maganizo a mlembi Ernest Hemingway chakuti, “Chabwino ndi chimene chimakusangalatsa ukachichita, ndipo choipa ndi chimene chimakunyansa ukachichita,” chikufotokoza bwino mwachidule maganizo a aja amene anakopeka ndi chiyembekezo chopeza ufulu pa zakugonana ndi kukhutira nazo. Kulandira mzimu umenewu kunalola kumagonana ndi anthu ambirimbiri pazitsamwali zosakhalitsa, zimene zinachititsa anthu, amuna ndi akazi, kuyesa kuona pamene angafike ndi chilakolako chawo cha kugonana. Sanali “kukhutira” ndi kugonana. Mankhwala oletsa kutenga mimba, omwe anakhalako panthaŵi imodzimodziyo, analimbikitsa kwambiri kugonana kosadziletsa ndi aliyense.
Komabe, chifukwa cha moyo wachiwerewere umenewu, panatsatira AIDS ndi matenda ena opatsana mwa kugonana. Maganizo a mbadwo wachiwerewere umenewo pa zakugonana anakhwetemuka. Zaka zingapo zapitazo, magazini ya Time inali ndi mutu wakuti “Kugonana m’ma ’80—Abwezanso Maganizo.” Chilengezo chimenechi chinakhalapo makamaka chifukwa cha kuwanda kwa matenda opatsana mwa kugonana omwe Aamereka ambiri anatenga. Lero, chiwonkhetso cha odwala AIDS padziko lonse chafika pachiŵerengero choopsa pafupifupi 30 miliyoni!
Kuopa matenda opatsana mwa kugonana kunasinthitsanso ambiri maganizo awo pa kugonana kwa zitsamwali zosakhalitsa. Mu 1992 kope la US, magazini ya zosangulutsa, inati posimba za kufufuza kochitidwa ndi boma: “Akazi osakwatiwa okwanira ngati 6.8 miliyoni asintha khalidwe lawo pa kugonana chifukwa cha AIDS ndi matenda ena opatsana mwa kugonana.” Malinga ndi nkhaniyo, uthenga ngwomveka wakuti: “Kugonana si maseŵera. Nkwangozi.”
Kodi zaka zovuta zimenezi zakhudza motani maganizo a anthu pa kugonana? Kodi aphunzirapo zilizonse pa kusadziletsa kwaukandifere kosonyezedwa ndi kugonana kwaufulu pazaka zapitazi ndiponso pa matenda opatsana mwa kugonana omwe abuka m’ma ’80? Kodi maphunziro a zakugonana omwe ayambika m’masukulu athandiza anyamata ndi atsikana kukhala odzisunga? Kodi njira yabwino ndi iti yolimbanirana ndi vuto la kusintha maganizo kwa lero pa kugonana?