Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Nchifukwa Ninji Mbale Wanga Amamuikako Nzeru Kwambiri?
“Chimandivuta nchakuti pamene abale ndi alongo anga alakwa, amawaikako nzeru kwambiri—achite zabwino kaya zoipa. Koma poti ndimamvera nthaŵi zonse, sasamala za ine.”—Kay wazaka 18.a
“Abale anga ndi alongo anga amawaikako nzeru ndipo amawakomera mtima. Akati andiikeko nzeru ineyo, nkundipatsa uphungu basi. Ndikadakondwa ndikadadziŵa kuti nawonso amapatsidwa uphungu.—Ruth wazaka 15.
“Ine ndimaona kuti akulu anga ndi alongo anga amawachitira zambiri ndipo amawaikako nzeru kwambiri.”—Bill wazaka 13.
KUCHOKERA tsiku lomwe tinabadwa, tonsefe timafuna chisamaliro cha makolo. Ndiye ngati muona kuti sakusamala za inu, nzomveka kuti mukhoza kukhumudwa ndiponso kupsa mtima. Makamaka ngati kuoneka kuti mbale wanu—wamkulu pa onse, wamng’ono pa onse, wakhalidwe labwino kwambiri, mwina ngakhale wopulupudza kwambiri—ndiye amamlingalira kwambiri nthaŵi zonse. Mpaka mwina mungamve monga Davide pamene analemba kuti: “Ndaiwalika m’mtima monga wakufa: ndikhala monga chotengera chosweka.”—Salmo 31:12.
Kuona mbale wanu akumuikako nzeru kwambiri, chimenenso inu mungafune, kungakhale koŵaŵa. Koma kodi izi zimatanthauza kuti sakukondani? Si choncho ayi. Nthaŵi zina achinyamata ena amawaikako nzeru chifukwa chakuti ali ndi maluso kwambiri kapena kuti ngaubwenzi. Kenneth wazaka 11 akuti: “Ngakhale kuti mng’ono wanga, Arthur, ali m’giredi lachitatu, amaimba nawo m’bandi la m’giredi lachisanu. Komanso ndi katswiri pa maseŵero ndi masamu. Kunena zoona, amangopeza ma A m’kalasi lililonse pasukulu. Nthaŵi zina ndimaganiza kuti anthu amamkonda kuposa ine, koma sindimchitira nsanje. Ee, mwinamwake pang’ono chabe.”
Ndiye pali achinyamata ena amene makolo amatayirapo nthaŵi yaikulu kwambiri chabe chifukwa chakuti ndiwo aakulu pa onse—kapena aang’ono pa onse. Baibulo limati ponena za wachinyamatayo Yosefe: “Israyeli anamkonda Yosefe koposa ana ake onse, pakuti anali mwana wa ukalamba wake.” (Genesis 37:3, 4) Kumbali ina, Todd wazaka 18 anaganiza kuti makolo amakonda mkulu wake chifukwa chakuti ndiye wamkulu pa onse. Iye akukumbukira kuti: “Nthaŵi ina aliyense anauzidwa kukabweretsa chithunzi chake chapaukhanda chomwe amakonda kwambiri kuti tikachitire pulojekiti ina kusukulu. Ndinangopeza zithunzi zanga zochepa chabe koma ndinaona zithunzi zambiri zedi zamkulu wanga. Sindinamvetse chifukwa chake zinali choncho.”
Komabe, makolo kaŵirikaŵiri amaika nzeru kwambiri mbale wanuyo chifukwa chakuti iyeyo ali ndi vuto—mwina vuto limene inu simukulidziŵa. “Pamene ndinali ndi zaka ngati 16, mkulu wanga anali ndi mavuto ena,” akulongosola motero Cassandra, yemwe tsopano ali ndi zaka 22. “Iye anali kudzikayikira ngati akufunadi kutumikira Yehova, motero makolo anga anaika pafupifupi nzeru zawo zonse kwa iye. Panthaŵiyo, sindinamvetsetse chifukwa chake zinthu zinali choncho. Ndinalingalira kuti sasamala nkomwe za ine. Ndinamva chisoni ndipo ndinaganiza kuti anditaya—nditero kuti ndinapsa mtimatu.”
Chifukwa Chake Amakondera
Komabe, nthaŵi zina makolo amakhaladi okondera. Mayi wina anavomereza kuti: “Ndimazindikira kuti mwana wanga, Paulo, momvetsa chisoni amadziŵa momwe timanyadirira mwana wathu wamkazi. Watiuza pamaso pathu kuti, ‘Inu ndi Atate nthaŵi zonse mumayang’anizana Liz akanena kanthu.’ Poyamba sitinazindikire zimene anali kutanthauza. Kenaka tinazindikira kuti timayang’anizana kaŵirikaŵiri nkumati ‘akunena zanzeru eti?’ Popeza watiuza, tayesetsa kuti tisazichitenso.”
Koma kodi nchifukwa ninji makolo amakondera? Chochititsa chingakhale mmene iwo eni analeredwera. Mwachitsanzo, ngati amayi anu pakukula kwawo ndiwo anali mwana wamng’ono pa onse, angamakonde kwambiri mwana wawo wamng’ono pa onse. Mosazindikira konse, kaŵirikaŵiri adzamkhalira kumbuyo. Nthaŵi zina kholo lingamakomere mtima mwana amene limafanana naye makhalidwe kapena amene amakonda zomwe limakonda. Lingalirani zimene Baibulo limanena za Isake ndi Rebeka pa za ana awo amapasa, Yakobo ndi Esau: “Anakula anyamatawo; ndipo Esau anali munthu wakudziŵa zakusaka nyama, munthu wa m’thengo; ndipo Yakobo anali munthu wofatsa, wakukhala m’mahema. Ndipo Isake anakonda Esau, chifukwa anadya nyama yake ya m’thengo; koma Rebeka anakonda Yakobo.”—Genesis 25:27, 28.
Kodi nchiyani chimene muyenera kuchita ngati makolo anu aoneka kuti akukondera mmodzi wa abale anu?b Yesani kulankhula nawo za nkhaniyo mofatsa, mosaŵaimba mlandu. (Miyambo 15:22) Mwa kuwamvetsera mwaulemu, mukhoza kuzindikira mmene iwo amaganizira. Izi zikhoza kuthandiza kuchepetsa kukhumudwa kwanu. (Miyambo 19:11) Mtsikana wina akuti: “Zinandiŵaŵa mtima kwambiri kuona kuti Amayi anga anali kukonda mlongo wanga kuposa ine. Nditawafunsa, ananena kuti nchifukwa chakuti iye amaoneka kwambiri ngati Atate, ndiye chifukwa chake amamkonda. Ndipo poti ine ndimaoneka kwambiri ngati iwo, Atate amakonda ine kwambiri. Mofananamo, poti iwo ndi ine timafanana kwambiri, timakwiyitsana. Ndipo poti mlongo wanga ndi atate amafanana kwambiri, amapsetsana mtima. Pamene anangonena zimenezo—ngakhale kuti sizinandikondweretse—ndinavomereza.”
Kuwasiyanitsa—Kodi Nkupanda Chilungamo?
Komabe, nchifukwa ninji makolo samangochitira mwana aliyense mofanana ndendende ndi mnzake? Beth, yemwe tsopano ali ndi zaka 18, akuti: “Pamene ndinali ndi zaka pafupifupi 13, ndinaganiza kuti ineyo ndi mlongo wanga ayenera kutichitira chimodzimodzi—ndendende osasiyanitsa. Koma iwo anali kukalipira ine nthaŵi zonse, pamene iye anali kungomuleka. Ndipo anali kuthera nthaŵi yochuluka ndi Atate kukonza galimoto. Sizinaoneke bwino.”
Koma sikuti nchisalungamo kuwasiyanitsa anthu. Lingalirani mmene Yesu Kristu anali kuchitira ndi atumwi ake. Palibe kukayikira kulikonse kuti anali kuwakonda onse 12, komabe anaitana atatu okha mwa iwo kuti akaonerere zochitika zapadera, kuphatikizapo chiukiriro cha mwana wamkazi wa Yairo ndiponso kusandulika. (Mateyu 17:1; Marko 5:37) Ndiponso, Yesu anali ndi ubwenzi wapadera ndi mtumwi Yohane. (Yohane 13:23; 19:26; 20:2; 21:7, 20) Kodi uku kunali kuwasiyanitsa? Inde. Kodi zinali zoipa? Ayi ndithu. Chifukwa ngakhale kuti Yesu anali kukonda enawo, sananyalanyaze zofunika za atumwi ake ena.—Marko 6:31-34.
Mofananamo, kungakhale kuti wina mwa abale anu amamuikako nzeru kwambiri chifukwa cha maluso ake, umunthu wake, kapena zofunikira zina. Mwachibadwa, kuona zotere kungakhale koŵaŵa. Koma funso nlakuti, Kodi zofunika zanu zikunyalanyazidwa? Pamene mufuna uphungu kwa makolo anu, chithandizo kapena chilimbikitso kodi amakupatsani? Ngati zili choncho, kodi ndithudi munganene kuti sakukuchitirani chilungamo? Baibulo limatilimbikitsa ife ‘kupatsa [ena] zosoŵa zawo.’ (Aroma 12:13) Popeza inu ndi abale anu ndinu anthu okhala ndi zosoŵa zosiyana, nzosatheka kuti makolo anu akuchitireni mofanana nthaŵi zonse.
Beth, wonenedwa poyamba paja, anafika pozindikira kuti kuchitidwa mofanana sikumakhala koyenera nthaŵi zonse ndi kuti kuchitidwa moyenera sikukhala kofanana nthaŵi zonse. Iye akuti: “Ndinazindikira kuti ine ndi mlongo wanga ndife anthu osiyana motero tifunika kuchitidwa mosiyana. Ndikayang’ana mmbuyo, sinditha kumvetsetsa kuti sindinali kuzindikira zimenezo ndili wamng’ono. Ndikuganiza kuti zili chabe mmene umaonera zinthu uli pausinkhu umenewo.”
Kuphunzira Kukhala Wozindikira
Inde, “mmene umaonera zinthu” kumakhudza kwambiri mmene umachitira pakakhala zotero. Monga mandala aja omwe amapangitsa zinthu kuoneka za mtundu wina, malingaliro anu akhoza kupangitsa zinthu kuoneka za mtundu wina kwa inu. Ndipotu malingaliro anu akuti makolo anu azisamala za inu ndi kukondwa nanu ngamphamvu kwambiri. Ofufuza ena, Stephen Bank ndi Michael Kahn ananena kuti: “Ngakhale ngati makolo akanatha kuchita chinthu chosathekachi chochitira ana awo osiyanasiyana mofanana ndendende, mwana aliyense akanaona ngati kuti makolowo akukondera wina wa anawo.”
Mwachitsanzo, lingaliraninso zomwe zinanenedwa ndi achinyamata atatu omwe tawagwira mawu pamwambapo. Mkhalidwe wawo ungaoneke kukhala wosatheka kuwongokera koma mfundo njakuti: Onsewo mpachibale! Ndithudi, aliyense mwa iwowa amaganiza kuti enawo akuwaikako nzeru kwambiri ndi kuti iye ndiye amene akunyalanyazidwa! Motero, kaŵirikaŵiri sitiona zinthu monga mmenedi zilili. “Wofatsa mtima [“wozindikira,” NW] ali wanzeru,” imatero Miyambo 17:27. Kukhala wozindikira ndiko kuona zinthu mongadi mmene zilili ndiponso cholinga chake, osati mokhudzika mtima ayi. Kuzindikira kukhoza kukuthandizani kudziŵa kuti ngakhale makolo anu angakhale asakukuchitirani zinthu zofanana nonse, amakonda kukuchitirani zabwino nonse! Kuzindikira zimenezi kukhoza kukuthandizani kupeŵa kupsa mtima ndi kudandaula.
Komabe, bwanji ngati zikuonekadi kuti inuyo sakuikaniko nzeru nkomwe? Kodi mungatani? Izi tidzaziona mu nkhani zamtsogolo za Galamukani!
[Mawu a M’munsi]
a Maina ena asinthidwa.
b Nkhani yamtsogolo idzakamba mwatsatanetsatane mmene mungachitire pakakhala kukondera.
[Chithunzi patsamba 18]
Kuwasiyanitsa sikungaoneke bwino