Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 1/8 tsamba 20-22
  • Mmene Mungakhalire m’Nyengo ya Chidziŵitso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Mungakhalire m’Nyengo ya Chidziŵitso
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Olandira ndi Opereka Chidziŵitso
  • Kodi Timafuna Nkhani Wamba Zambiri Chonchi?
  • Kuchuluka kwa Chidziŵitso
    Galamukani!—1998
  • Kodi Nchiyani Chimachititsa Nkhaŵa Yofuna Kudziŵa Zambiri?
    Galamukani!—1998
  • Tiyenera Kugwiritsa Ntchito Intaneti Mwanzeru
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Uthenga Wabwino pa Internet
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 1/8 tsamba 20-22

Mmene Mungakhalire m’Nyengo ya Chidziŵitso

TIYENERA kudziŵa kuti pali mbali zambiri za nyengo ya chidziŵitso m’ma 1990 muno zimene zizitidetsabe nkhaŵa. Zina za izo tingazilamulire pang’ono kapena sitingathe nkomwe. Komabe, pali zinthu zina zimene tingachite kuti tichepetse kapena kuthetseratu nkhaŵa imeneyo. Choncho, tingatero kuti kukhala m’nyengo ya chidziŵitso nkovuta koma kopindulitsa.

Olandira ndi Opereka Chidziŵitso

Kaya tadziika tokha m’gulu limodzilo kapena linalo kapena iyayi, tonsefe mwanjira ina timalandira chidziŵitso ndi kuchipereka m’moyo wathu wonse. Komabe, ubongo wathu umalandira chidziŵitso nkuchitanthauzira mwa njira zosiyanasiyana. Njira ina ndiyo mmene ubongo umatanthauzira chidziŵitso modabwitsa kwambiri ifeyo tisakuzindikira chilichonse.

Njira ina mpamene ubongo umasamalira chidziŵitso, monga kukambitsirana. Kutanthauzira chidziŵitso kwa mtundu umenewu ife timakulamulira ndithu—pochipereka ndiponso pochilandira. Ponena za nkhani wamba, Baibulo limachenjeza za ena ‘osati aulesi okha, komatunso olankhula zopanda pake, nachita mwina ndi mwina, olankhula zosayenera.’ (1 Timoteo 5:13) Mwa mawu ena, samalani kuti musamawononge nthaŵi yochuluka mukumakamba nkhani wamba kapena ngakhale chidziŵitso chovulaza. Musakhale mtundu wa munthu amene amangofuna za miseche basi. Nthaŵi yofunika ndi nyonga zingangotayika, ndipo zimenezo zingapangitse ife ndi ena kudera nkhaŵa. Mungaphonye mipata yophunzira ndi kuchifalitsa chidziŵitso cholimbikitsa zedi ndi chofunikanso kuti mupirire m’dziko la mavutoli.

Chidziŵitso chimene timapeza mwa kuŵerenga, ubongo umachitanthauzira ifenso tikuzindikira. Panopa mpamene nkhaŵa yaikulu imayambika. Kudandaula kwa munthu wolemedwa ndi nkhaŵa, kwakuti, “Sinditha kumaliza zoŵerenga zanga iyayi!” si kwachilendo. Kodi mumamva kuti muli ndi zambiri zofuna kuŵerenga koma nkukhala ndi nthaŵi yochepa yoŵerengera? Chifukwa chakuti kuŵerenga kumadya nthaŵi, luso lake ndi kusangalatsa kwake kumatayika m’nyengo ino imene munthu angapeze chidziŵitso kamodzinkamodzi. Anthu ambiri amalola TV kuwadyera nthaŵi yawo yonse. Komabe, mawu olembedwa adakali njira yabwino koposa yosonkhezera maganizo ndi yoperekera chidziŵitso, malingaliro, ndi zikhulupiriro.

Kodi tingachite bwanji pamene mabuku ambiri akutiyembekezera kuti tiwaŵerenge pamene kwinaku TV, maseŵera a pakompyuta, ndi zosangulutsa zina zikufunanso kuti tiziyang’ane? Yankho ndilo kusankha. Kusankha kapena kuika pamalo oyamba zimene tikufuna kumva, kuona, kunena, kapena kuŵerenga kungathetse nkhaŵa ya chidziŵitso. Pali njira ziŵiri zimene mungasankhire bwino zochita.

Kodi Timafuna Nkhani Wamba Zambiri Chonchi?

Kaŵirikaŵiri timalephera kuzindikira zimene timafunadi chifukwa cha zimene anthu ena amaganiza kuti nzimene timafunikira kapena chifukwa cha zimene ofalitsa nkhani, posatsa malonda mwaluso, amatipangitsa kukhulupirira kuti nzimene timafunikiradi. Kuti mupewe msokonezo umene chidziŵitso chochulukitsitsacho chimabweretsa, sungani lamulo lakuti: Peputsani zinthu! Richard S. Wurman analongosola motere: “Chinsinsi cha kupeza chidziŵitso ndicho kupungula zimene mumaŵerenga nkungotsala ndi zokhazo zimene zimakhudzana ndi moyo wanu . . . Ndikuganiza kuti ndi bodza kuti ngati uli ndi ufulu wosankha zambiri, umathanso kuchita zambiri zoyenera ndipo umakhalanso ndi ufulu wochuluka. M’malo mwa zimenezo, kukhala ndi zambiri zosankha kumayambitsa nkhaŵa yaikulu.”

Choncho pamene mukufuna kuŵerenga kapena kuonerera TV, ndi bwino kupenda zizoloŵezi zanu. Dzifunseni kuti: ‘Kodi zimenezi nzofunika pantchito yanga kapena pamoyo wanga? Kodi ndifunikiradi kudziŵa nkhani zonse zopanda pake ndi manenanena okhudza anthu otchuka ndi omwe amatchedwa anthu okongola a padziko lapansi? Kodi moyo wanga udzasintha ndikaleka kuonerera programu ya TV imeneyi, kuŵerenga bukuli kapena magazini ija, kapena kuwononga nthaŵi yaitali kwambiri ndikuŵerenga nyuzipepala?’ Ena, akhoza kale kupenda mabuku omwe ankaŵerenga ndi nthaŵi imene ankapenyerera TV ndipo achotsa zimene zinali kungolemetsa maganizo awo ndi kuwathera malo panyumba. Mwachitsanzo, asankha kungokhala ndi sabusikripishoni ya nyuzipepala imodzi basi. Zilibe kanthube, chifukwa manyuzipepala ambiri amakhala ndi nkhani zofanana. Anthu enanso achita kupempha mwachindunji kuti asamalandire m’mabokosi awo a makalata manyuzipepala wamba ongosatsa malonda basi.

Munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako, Yesu Kristu, analimbikitsa za kukhala ndi moyo wopepuka, wopanda zambiri zopinga. (Mateyu 6:25-34) Anthu ambiri a ku Asia amauyamikira moyo wopepuka ndipo ngwofala kumeneko. Ngakhale anthu ambiri a Kumadzulo amaona kuti moyo umenewo ngwabwino koposa. Wolemba Duane Elgin anati: “Kukhala ndi moyo wopepuka kwenikweni ndiko kukhala moyo ndi cholinga ndipo wopanda zocheukitsa zambiri zosafunika.”

Tsopano, pokhala mutaika pamalo oyamba zimene mukufuna, mogwirizana ndi zosoŵa zanu, teroninso ndi zokusangalatsani, pakuti chidwi nchimene chimasonkhezera munthu kuphunzira. Komabe, panopa vuto ndilo kulekanitsa zimene zimakusangalatsanidi ndi zimene mungaganize kuti zingakusangalatseni kuti mukondweretse ena—mwina ogwira nawo ntchito. Koma ngati mungamalinganize nthaŵi yoŵerenga ndi yoonerera TV kapena yokhala pakompyuta monga mmene mumalinganizira china chilichonse, mudzapeza kuti mutamasankha zokhazo zokusangalatsani zidzapangitsa moyo wanu kukhala wabwino, wopanda nkhaŵa yopambanitsa.

Chotero, kodi mungachite nayo bwanji nkhaŵa ya chidziŵitso? Simungathe kuichotseratu yonse, koma mutatsatira malamulo ofeŵa oŵerengeka omwe tandandalikawa angakuthandizeni kwambiri. Dzipeputsireni zinthu, ndipo ikani chidziŵitso m’magulu mogwirizana ndi zosoŵa zanu ndi zimene mumakonda. Nthaŵi ikudza pamene moyo wonse wovuta, kuphatikizapo nkhaŵa ya chidziŵitso, zidzakhala zinthu zakale, koma pakali pano, zodabwitsa za makina amakono zikhale m’malo ake. Ingozionani ngati zogwiritsira ntchito. Musakhale kapolo wa izo kapena kuzilemekeza. Choncho, chidziŵitso chothandiza chidzakhala chomangirira, cholimbikitsa, chopindulitsa, chosakudetsani nkhaŵa.

[Bokosi patsamba 21]

Yesani Kulinganiza

“Lekani kulipirira maprogramu a cable TV, . . . ndi kugwiritsira ntchito [ndalama] zomwezo kugula buku limodzi kapena angapo abwino mwezi uliwonse. Mabuku amasiyana ndi wailesi yakanema: Mumawaŵerenga pang’onopang’ono, ngochititsa chidwi, amasonkhezera, amawonjezera luntha, ndipo amakupatsani luso la kuganiza.”

“Mungaganizenso zoti mudziikire malire kuti maola omwe mumawononga muli pa Internet azikhala oŵerengeka basi mlungu uliwonse, kapena kuti nthaŵi yomwe mumawononga muli pamakinawo izilingana ndi imene mumawononga mukuŵerenga.”—Data Smog—Surviving the information Glut.

[Bokosi patsamba 22]

Khalani Mbuye, Osati Kapolo

“Tsekani wailesi yakanema. Palibe njira ina yamwamsanga yoongolera moyo wanu, yobwezeretsera mtendere wapanyumba panu, yoongolera maganizo anu yoposa kungotseka chipangizo chimene chimalamulira moyo wa ambirife. Anthu mamiliyoni ambiri a ku America akhala akutulukira kuti kusinika batani la OFF kwawapatsa mtendere ndi nyonga, ndiponso kwawapatsa nthaŵi yambiri koti tsopano angayambe kuchitira zinthu zina zimene kale sanali kuzipezera nthaŵi.”—Data Smog—Surviving the Information Glut.

[Bokosi patsamba 22]

Chenjerani Nayo Internet

Anthu ena a khalidwe loipa amagwiritsira ntchito Internet kukhutiritsa zikhumbo zawo zakugonana kwauchinyama ndipo amayesa kulankhulana ndi anthu ena omwe angafune kutero kapena kuyesa kunyengerera anthu ena osadziŵa kanthu. Enanso amagwiritsira ntchito Internet kuchirikiza zolinga zawozawo. Ampatukonso nawo amakhala ndi Web yokolera anthu osasamala.

Nkofunikadi kusamala kwenikweni pamene mukugwiritsira ntchito Internet, ndipodi makolo ayenera kuyang’anira mwana wawo aliyense amene angakhale akuigwiritsira ntchito. Nzoona kuti mulinso zinthu zina zothandiza zimene mungapeze mmenemo, zonga malaibulale, masitolo a mabuku, ndi masiteshoni oulutsira nkhani. Mwachitsanzo, posachedwapa, Watch Tower Society inalengeza kuti nayonso ili ndi Web yakeyake (www.jw.org), yomwe ntchito yake njopereka maumboni oona onena za Mboni za Yehova. Komabe, munthu afunikira kuzindikira kuti kulinso zinthu zovulaza zedi, kuphatikizapo zithunzithunzi zaumaliseche ndi mpatuko.

Mkristu ayenera kumakumbukira uphungu wa Paulo wakuti: “Ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, m’chitsiru cha mtima wawo . . . Amenewo popeza sazindikiranso kanthu konse, anadzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite chidetso chonse mu umbombo. Koma inu simunaphunzira Kristu chotero.” (Aefeso 4:17-20) Ndiponso, “Dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima; kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko.” (Aefeso 5:3, 4) Tiyenera kuzindikira kuti ma Web ambiri apangidwa ndi anthu okhala ndi zolinga zoipa kapena za kusokeretsa ena. Ndipo ma Web ena omwe sangakhale oipa kapena omwe sangakhale achinyengo, monga kungolankhulana ndi magulu a anthu, zimangowononganso nthaŵi. Zonse zoterozo muzingozipeŵa basi!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena