Kupanda Chitetezo—Vuto la Dziko Lonse
KODI inu nthaŵi zina mumaona kuti moyo ndi chuma chanu zili pangozi ndipo nzosadalirika kuti zikhalapo kwa nthaŵi yaitali motani? Inu simuli nokha. Anthu mamiliyoni ambiri amamvanso choncho. Kupanda chitetezo kumafala mofulumira monga matenda, mosasamala kanthu za malire adziko, chipembedzo, kapena chikhalidwe cha anthu, ndipo kumavutitsa anthu kuchokera ku Moscow mpaka ku Manhattan.
Malinga nkunena kwa dikishonale ina, pamene moyo wathu uli wosatetezereka, “timagwidwa ndi mantha ndiponso nkhaŵa.” Nkhaŵa ndi vuto la maganizo limene limapangitsa kupanikizika maganizo ndipo ikhoza kuwononga thanzi lathu. Koma nanga nchifukwa ninji timakhala odera nkhaŵa ndi opanda chitetezo?
Nkhaŵa ku Ulaya
M’maiko a m’bungwe la European Union (EU), munthu mmodzi mwa anthu asanu ndi mmodzi ali mu umphaŵi wadzaoneni, 18 miliyoni ali paulova, ndipo ena osaŵerengeka amadera nkhaŵa kuti adzachotsedwa ntchito. M’maiko ambiri a m’bungwe la EU, makolo ndi a nkhaŵa kuopa kuti ana awo adzagwiriridwa ndi ogona ana. M’dziko lina la m’bungwe la EU, anthu aŵiri mwa atatu ali ndi nkhaŵa chifukwa cha upandu. Ena a anthu a m’maiko a EU nthaŵi zonse amakhala ndi nkhaŵa zomakulirakulirabe chifukwa choopa anthu owononga katundu wa anzawo, uchifwamba, ndi kuipitsa zinthu zachilengedwe.
Moyo ndiponso njira yopezera zofunika pamoyo zili pangozi osati chabe chifukwa cha makhalidwe oipa a anthu komanso chifukwa cha masoka achilengedwe. Mwachitsanzo, mu 1997 ndi 1998, mvula yambiri, matope ndi chimphepo zinawononga malo osiyanasiyana ku United States. Mu 1997, madzi osefukira anawononga ku Central Europe pamene mitsinje ya Oder ndi Neisse inasefukira. Malinga nkulemba kwa nyuzipepala ya sabata ndi sabata ya ku Poland ya Polityka, madzi anasefukira m’minda yambiri ndiponso m’mizinda ndi m’matauni 86 ndi m’midzi 900. Anthu pafupifupi 50,000 mbewu zawo zinawonongeka, ndipo ena pafupifupi 50 anafa. Kumayambiriro kwa 1998 matope oyenderera anapha anthu makumi ambiri kummwera kwa Italy.
Chitetezo cha Munthu Aliyense
Koma kodi sititsimikizira kuti moyo uli wotetezereka tsopano kuposa mmene unalili zaka khumi zapitazo? Kodi kutha kwa Nkhondo ya Mawu sikunapangitse chiŵerengero cha asilikali kutsika? Ndithudi, dziko liyenera kukhala litatetezereka kwambiri. Komabe, chitetezo cha munthu aliyense chimakhudzidwa ndi zimene zimachitika panyumba ndi mumsewu. Ngati ntchito itithera kapena tikulingalira kuti munthu wakuba kaya wogona ana ali pafupi, zilibe kanthu kuti ndi zida zingati zimene aphwasula, timakhalabe ndi nkhaŵa ndi kudzimva osatetezereka.
Kodi anthu ena amakhala bwanji pali kusadalirika kwa moyo? Ndipo chofunika koposa, kodi pali njira yopangitsira moyo wamunthu aliyense—kuphatikizapo wanu—kukhala wotetezereka kwa nthaŵi zonse? Mfundo zimenezi tizikambitsirana m’nkhani ziŵiri zotsatira.
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
UN PHOTO 186705/J. Isaac
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
FAO photo/B. Imevbore