Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 12/8 tsamba 11-14
  • Anthu Onse Padziko Lapansi Adzakhala ndi Ufulu Wachibadwidwe!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anthu Onse Padziko Lapansi Adzakhala ndi Ufulu Wachibadwidwe!
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zifukwa Ziŵiri Zosinthira
  • Maphunziro Aphindu
  • Boma Ladziko Lonse—‘Maloto’?
  • Omwe Kale Anali Odana Atumikira Yehova Mogwirizana
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kuionera Pansanjika ya 29
    Galamukani!—1998
  • “Ntchito Yanthaŵi Yaitali Yatha”
    Galamukani!—1998
  • Ufulu Wachibadwidwe ndi Zimene Anthu Amalakwitsa Lerolino
    Galamukani!—1998
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 12/8 tsamba 11-14

Anthu Onse Padziko Lapansi Adzakhala ndi Ufulu Wachibadwidwe!

LOYA wina yemwe wasamala nkhani za ufulu wachibadwidwe kwa zaka zambiri anafunsidwapo kuti: “Kodi kwenikweni chimachititsa anthu kulanda anzawo ufulu wachibadwidwe nchiyani?” Loyayo anayankha kuti: “Dyera. Dyera pankhani zandale ndi kufuna kutchuka pazachuma.” Ndiye popeza kuti dyera limayambira m’maganizo a munthu, anthu amene amalanda anzawo ufulu wachibadwidwe amangosonyeza mmene maganizo awo alili. Chifukwa china ndicho kukonda dziko lako. Maganizo akuti dziko langa lipambane ndiwo amasonkhezera anthu kulanda anzawo ufulu wachibadwidwe. Polofesa wina wa ku Holland, wodziŵa zamalamulo ndi zachuma, Jan Berkouwer, ananena kuti ufulu wachibadwidwe ungatheke pokhapokha ‘ngati pangakhale boma ladziko lonse limene lidzaika malamulo omwe adzasungidwadi.’

Mwa mawu ena, kuti ufulu wachibadwidwe utheke padziko lonse, pafunikira kuchitika zinthu ziŵiri: kusintha maganizo ndi kusinthanso boma. Kodi tingayembekezere kuti zimenezi zingachitikedi?

Zifukwa Ziŵiri Zosinthira

Pamene kuli kwakuti pologalamu ya UN yotchedwa Zaka Khumi za Maphunziro a Ufulu Wachibadwidwe yatsala pang’ono kuloŵa m’chaka chachisanu, pali pologalamu yapadziko lonse yamaphunziro osachirikizidwa ndi boma, yomwe kwa zaka makumi ambiri yakhala yokhoza kusintha maganizo a anthu mamiliyoni ambirimbiri. Chifukwa cha maphunziro amenewo, anthuwa tsopano amalemekeza anthu anzawo. Mboni za Yehova ndizo zikuchititsa maphunziro ameneŵa m’maiko oposa 230. Kodi nchifukwa chiyani ikuthandiza?

Chifukwa china nchakuti pologalamu yophunzitsa anthu Baibulo padziko lonse imawatsegula anthu mitu nkuyamba kuzindikira chiyambi cha ufulu wachibadwidwe. Chikalata cha mfundo za ufulu wachibadwidwe cha Universal Declaration of Human Rights chimati munthu ali ndi ufulu chifukwa amaganiza ndiponso amazindikira chabwino ndi choipa.

Wina wake woposa munthu ndiye anapatsa munthu mphamvu yake yakuganiza limodzi ndi chikumbumtima. (Onani bokosi lakuti “Gwero la Ufulu Wachibadwidwe,” patsamba 13.) Mukamazindikira kuti Mulungu ndiye gwero la ufulu wachibadwidwe, mudzakhala ndi chifukwa chabwino kwambiri cholemekezera munthu mnzanu. Ndiyeno mudzalemekeza anzanu osati chifukwa chokha chakuti chikumbumtima chanu chikukuuzani kutero, koma makamaka kuti kulemekeza kwanu Mlengi ndi kumkonda kudzakusonkhezerani kulemekezanso zimene analenga. Mbali ziŵiri zimenezi zikuchokera pa mawu a Yesu Kristu akuti: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse” ndipo, “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini.” (Mateyu 22:37-39) Munthu amene amalemekeza kwambiri Mlengi sadzayesa kumlanda mnzake ufulu wake wachibadwidwe chifukwa ufuluwo ncholowa chomwe mnzakeyo anachilandira kwa Mulungu. Munthu wolanda anzake ufulu wawo wachibadwidwe amalanda anzake cholowa chawo.

Maphunziro Aphindu

Kodi pologalamu ya maphunziro a Baibulo imeneyi yomwe Mboni za Yehova zikuchititsa, ikuthandiza bwanji anthu kuleka kulanda anzawo ufulu wachibadwidwe? Njira yabwino yoyankhira funso limeneli ndiyo kuyang’ana zimene anthu ophunzitsidwawo akuchita, popeza kuti Yesu anati, “nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake.”—Mateyu 11:19.

Mawu otchuka olembedwa pakhoma la Nyumba ya United Nations mu New York City amati: “Adzasula malupanga awo akhale zolimira. Ndi nthungo zawo zikhale anangwape: Mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina. Ndipo sadzaphunziranso nkhondo.” Mwa mawu amenewo ochokera m’Baibulo, m’buku la Yesaya chaputala 2, vesi 4, King James Version, UN ikutchula mfundo yaikulu yoletsera anthu kulanda anzawo ufulu wachibadwidwe—kuthetsa nkhondo. Ndiponso, malinga ndi kunena kwa chofalitsa china cha UN, ‘nkhondo ndiyo yosemphaniratu ndi ufulu wachibadwidwe.’

Pologalamu ya maphunziro ya Mboni za Yehova imapitiriza lingaliro lolemba mawu a Yesaya pakhoma la mwala. ‘Imalemba’ mawu a Yesaya m’mitima ya anthu. (Yerekezerani ndi Ahebri 8:10.) Motani? Maphunzirowo amafafaniza malire aufuko ndi autundu ndi kuthetsa maganizo okonda dziko lako mwa kuphunzitsa anthu zimene Baibulo limanena pankhani yamafuko: Kuti pali fuko limodzi basi—fuko la anthu. (Machitidwe 17:26) Amene amaphunzitsidwawo amayamba kukhumba kwambiri ‘kutsanza Mulungu,’ yemwe Baibulo limati: “Alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.”—Aefeso 5:1; Machitidwe 10:34, 35.

Chifukwa cha maphunziro a Baibulo amenewa, anthu mamiliyoni ambiri lerolino ‘sakuphunziranso nkhondo.’ Anthu asinthadi maganizo ndi mtima. Ndipo anthu amasinthiratu. (Onani bokosi lakuti “Maphunziro Obweretsa Mtendere,” patsamba 14.) Pakali pano, tsiku lililonse, anthu oposa 1,000 pa avareji, amatsiriza kuphunzira mfundo zoyambirira zamaphunziro amene amaphunzitsidwa ndi Mboni za Yehova ndiye amagwirizana ndi gulu lapadziko lonse limeneli lochirikiza mtendere.

Kodi anthu ameneŵa amatsimikiza mpaka pati kusintha maganizo awo ndi kukana kulanda anzawo ufulu wachibadwidwe mwa kukana kupita kunkhondo? Amatsimikizadi. Nachi chitsanzo: Mboni zinaoneka kuti nzotsimikizadi kukana kulanda anzawo ufulu wachibadwidwe pamene zinayesedwa mothetsa khama pa Nkhondo Yadziko II, makamaka poyesedwa ndi a Nazi ku Germany. Wolemba mbiri wina, Brian Dunn, anati: “Mboni za Yehova sizinali kugwirizana ndi zofuna za a Nazi. Mboni za Yehova zinali zachete pankhani zandale, ndiye zimenezo nzimene a Nazi anali kudana nazo kwambiri. Zimenezo zinatanthauza kuti panalibe wokhulupirira aliyense amene akananyamula zida.” (The Churches’ Response to the Holocaust) Paul Johnson, m’buku lakuti A History of Christianity, anati: “Ambiri ankaweruzidwa kuti aphedwe chifukwa chokana kupita kunkhondo . . . , kapena ankatumizidwa ku Dachau kapena kumalo osungirako anthu amisala.” Koma sanafookebe. Katswiri wa zachikhalidwe cha anthu, Anna Pawelcynska ananena za Mbonizo kuti zinali ngati “kachilumba kochepetsetsa kosamva chitsutso kokhala m’chifuwa mwa mtundu wovutitsidwa.”

Tangoyerekezerani mmene kulanda ena ufulu wawo wachibadwidwe kukanachepera ngati anthu onse padziko anali ndi maganizo amenewa ndiponso ngati ‘akanaleka kuphunzira nkhondo!’

Boma Ladziko Lonse—‘Maloto’?

Wantchito wina wa UN anati, ‘kusintha maganizo a anthu nkovuta, ndipo kukonza boma ladziko lonse ndi maloto chabe.’ Ndithudi, chifukwa chokha chakuti maiko akhala akukana kupereka mphamvu yawo ku UN kapena ku gulu lina lililonse chimatsimikizira zimenezi. Komabe, Polofesa Berkouwer anati, anthu amene amati boma ladziko lonse nlosatheka, “angatchule njira zina zothetsera mavuto a dzikoli. Ndiye njira zina zothetsera mavutozo nzimene palibe.” Ndiko kuti njira za anthu. Koma yemwe angathetse mavutowa alipo wosakhala wathupi lanyama. Ameneyo ndiye ndani?

Monga momwe Baibulo limatiuzira kuti Mlengi ndiye anapatsa anthu mphamvu yamaganizo yozindikira kuti anthufe tili ndi ufulu wachibadwidwe, limatiuzanso kuti yemweyonso ndiye adzabweretsa boma ladziko limene lidzatheketsa ufulu umenewo. Boma lakumwamba limeneli nlosaoneka koma lilikodi. Kunena zoona, anthu mamiliyoni ambiri, mwina mosadziŵa, amalipempherera boma ladziko lonse limeneli pamene amapemphera pemphero lotchedwa Pemphero la Ambuye, kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Munthu yemwe Mulungu wamuika kuti atsogolere boma la Ufumu limenelo ndiye Kalonga wa Mtendere, Yesu Kristu.—Yesaya 9:6.

Boma ladziko lonse limeneli, mwa kuthetseratu nkhondo ndi kuthetsanso zinthu zina, lidzapambana pakugwirizanitsa anthu padziko lonse omwe adzakhala opatsana ufulu wachibadwidwe kosatha. Baibulo linalosera kuti: “[Mlengi] aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magareta ndi moto.”—Salmo 46:9.

Kodi kuti zimenezo zitheke padziko lonse zingachitike mwamsangadi? Maphunziro a Baibulo amene Mboni za Yehova zimachititsa amayankha funso limeneli mokhutiritsa. Tikukulimbikitsani kuphunzira nawo maphunziro amenewa.a Ngati mumafunadi ufulu wachibadwidwe, simudzakhumudwa nawo maphunzirowo.

[Mawu a M’munsi]

a Ngati mukufuna kudziŵa zambiri za maphunziro a Baibulo amenewa, lemberani ofalitsa a magazini ino kapena onanani ndi Mboni za Yehova za m’dera lanu. Maphunziro amenewa ngaulere.

[Bokosi patsamba 13]

Yemwe Anayambitsa Ufulu Wachibadwidwe

Mfundo 1 ya Universal Declaration of Human Rights (Chikalata cha mfundo za ufulu wa anthu onse wachibadwidwe), imati “Anthu onse amabadwa mfulu ndipo ngolingana ndipo ali ndi ulemu ndi ufulu wachibadwidwe wolingana.” Choncho, ufulu wachibadwidwe uli ufulu wobadwa nawo womwe umachokera kwa makolo kumka kwa ana, monga momwedi mtsinje umanyamula madzi kumka nawo kwa anthu okhala m’gombe lamtsinjewo. Kodi mtsinje umenewu wa ufulu wachibadwidwe unayambira kuti?

Malinga ndi chikalata cha Universal Declaration, anthu ali ndi ufulu chifukwa “anapatsidwa nzeru ndi chikumbumtima.” Chofalitsa china cha UN chinafotokoza motere: “Chifukwa chakuti munthu amaganiza ndi kuzindikira chabwino ndi choipa, ngwosiyana ndi zolengedwa zina padziko lapansi choncho ayenera kukhala ndi ufulu umene zolengedwa zinazo zilibe.” (Tapendeketsa mawu ndife.) Choncho, akuti kuganiza limodzi ndi chikumbumtima ndicho chifukwa chokhaliranso ndi ufulu wachibadwidwe. Poti zili choncho, yemwe anapatsa anthu nzeru ndi chikumbumtima ali yemweyonso amene anawapatsa ufulu wawo wachibadwidwe.

Zoti ufulu wachibadwidwe ngwogwirizana ndi maganizo a munthu limodzi ndi chikumbumtima chake, zimawagometsa aja okhulupirira kuti munthu anachokera kunyama. Buku lakuti Life Ascending, lochirikiza zoti anthu anachokera kunyama, linavomereza kuti: “Tikati tifufuze za mmene zinachitikira [kusinthika kuchokera kunyama nkukhala munthu] . . . kuti munthuyo akhale wokonda zinthu zokongola ndi wokonda choonadi, akhale munthu wachifundo, wokonda ufulu, ndipo makamaka kuti munthuyo afikire pakuganiza mwakuya, sitimamvetsa.” Ndipo mposamvekadi. Chifukwa kunena kuti kuganiza kwa munthu limodzi ndi chikumbumtima chake zinachokera kunyama zosaganiza ndi zopanda chikumbumtima kuli ngati kunena kuti mtsinje umachokera m’chitsime chopanda madzi.

Popeza kuti mphamvu yakuganiza ya munthu limodzi ndi chikumbumtima chake sizingachokere kunyama, ndiye kuti nzeru imeneyo iyenera kuchokera kwa munthu wina wosakhala wathupi ngati lathuli. Anthu okha ndiwo ali ndi mikhalidwe yokhudzana ndi ufulu wachibadwidwe—nzeru ndi chikumbumtima—chifukwa Baibulo limafotokoza kuti anthu ngosiyana ndi nyama, iwo analengedwa “m’chifanizo” cha Mulungu. (Genesis 1:27) Choncho, buku lakuti Human Rights—Essays on Justification and Applications limati, yankho lomveka la funso lakuti nchifukwa chiyani anthu ali oyenera ufulu, nlakuti chifukwa “anthuwo amabadwa olemekezeka kapena kuti aulemu kapena kuti ali . . . ana a Mulungu.”

[Bokosi patsamba 14]

Maphunziro Obweretsa Mtendere

Zaka zingapo zapitazo, pamene nkhondo inali kusakaza maiko a Balkans, Branko anali mlonda wokhala ndi mfuti pachipatala china ku Croatia, mbali ya Bosnia.b Dokotala wina pachipatalacho ankaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndiye tsiku lina anamuuza Brankoyo zimene ankaphunzira. Branko atamva zimenezo anatula zida zake. Panthaŵi inanso, atasamukira m’dziko lina la ku Ulaya, Branko anakhala nawo pamsonkhano wa Mboni za Yehova, ndiye kumenekoko anakumana ndi Slobodan.

Slobodan nayenso anali wa ku Bosnia. Anali atamenyapo nkhondo imodzimodziyo imenenso Branko anamenya—chabe kuti anali m’magulu osiyana. Slobodan anali kumbali ya a Serb akumamenyana ndi a Croatia. Panthaŵi imene aŵiriwa anakumana, nkuti Slobodan atakhala kale wa Mboni za Yehova, ndiye anampempha Branko, yemwe anali mdani wake wakale, kuti aziphunzira naye Baibulo. Adakali mkati mophunzira choncho, Branko anayamba kukonda kwambiri Mlengi, Yehova. Pasanapite nthaŵi, anaganiza zokhala wa Mboni za Yehova.c

Slobodan nayenso anali atakhala wa Mboni mothandizidwa ndi mdani wake wakale. Motani? Slobodaniyo atasiya zankhondo ku Bosnia, analandira mlendo wotchedwa Mujo, yemwenso anali wa ku Bosnia koma wokulira m’chipembedzo chosiyana kwambiri ndi cha Slobodan. Tsopano Mujoyo anali wa Mboni za Yehova. Ngakhale kuti anali adani, Slobodan anavomera pamene Mujo anampempha kuphunzira naye Baibulo ndipo patapita kanthaŵi nayenso anadzakhala wa Mboni za Yehova.

Kodi nchiyani chinachititsa anthu amenewa kuthetsa chidani chafuko naleka kukhala adani nkukhala mabwenzi? Anayamba kukonda Yehova chifukwa chophunzira Baibulo. Kenako analola ‘kuphunzitsidwa ndi Mulungu kukondana wina ndi mnzake.’ (1 Atesalonika 4:9) Malinga ndi mmene polofesa Wojciech Modzelewski ananenerapo za Mboni zonse za Yehova, “chimene chimawapangitsa kukhala ndi maganizo a mtendere nchakuti ngakhale tsopano lino amafuna kumvera malamulo a Baibulo.”

[Mawu a M’munsi]

b Maina onse amene tawatchula m’bokosi lino ngobwereka.

c Patapita nthaŵi, Branko anakondwa kumva kuti dokotala amene anali atamlankhulapo anali atakhala wa Mboni za Yehova nayenso.

[Zithunzi patsamba 11]

Kusintha maganizo a anthu ndi kusinthanso boma—kodi zingadzatheke?

[Mawu a Chithunzi]

U.S. National Archives photo

[Zithunzi pamasamba 12, 13]

Maphunziro a Baibulo akuchititsa anthu kusintha nkukhala a maganizo abwino

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena