Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 3/1 tsamba 28
  • Omwe Kale Anali Odana Atumikira Yehova Mogwirizana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Omwe Kale Anali Odana Atumikira Yehova Mogwirizana
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Anthu Onse Padziko Lapansi Adzakhala ndi Ufulu Wachibadwidwe!
    Galamukani!—1998
  • Kodi Dziko Lingagwirizanitsidwe?
    Galamukani!—1994
  • Kuchiritsa Mabala a Nkhondo
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Anapeza Mtendere M’dziko Lachipwirikiti
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 3/1 tsamba 28

Olengeza Ufumu Akusimba

Omwe Kale Anali Odana Atumikira Yehova Mogwirizana

“NDINAMVA koyamba za Mboni za Yehova pamene ndinali msilikali wolonda ku Bosnia,” akutero Branko.a

Branko anali paulonda pa chipatala chimene ovulala anali kusamaliridwapo. Mmodzi wa madokotala ake anali kuphunzira Baibulo ndi Mboni, ndipo pachipani china cha usiku, anafotokozera Branko zambiri zimene anaphunzira ponena za Baibulo.

Zimene Branko anamva usikuwo zinamsonkhezera maganizo kwambiri kwakuti anatula zida zake. Anafikira Mboni, akumafuna kuphunzira zambiri. Patapita nthaŵi, atasamukira ku dziko lina la ku Ulaya, Branko anafunafuna Nyumba ya Ufumu ndi kufika pamsonkhano wa mpingo wa Mboni za Yehova wachiyugosolaviya. Kumeneko nkumene Branko anakumana ndi Slobodan.

Nayenso Slobodan anachokera ku Bosnia ndipo anali atamenyapo nkhondo imodzimodziyo monga wodzifunira ngati Branko​—komano kumbali ya adani. Slobodan anamenya nkhondo mochirikiza Asebu polimbana ndi Akroati. Koma panthaŵi imene aŵiriwo anakumana, Slobodan anali Mboni ya Yehova yobatizidwa. Anapempha kuphunzira Baibulo ndi Branko, mdani wake wakale. Pamene phunzirolo linali kupita patsogolo, Branko anadziŵa zambiri ponena za Yehova, ndipo chikondi chake pa Mulungu chinakula. Zimenezi zinasonkhezera Branko kupatulira moyo wake kwa Mlengi. Mu October 1993 anasonyeza kudzipatulira kwake ndi ubatizo wa m’madzi.

Kodi ndi motani mmene Slobodan anakhalira mmodzi wa Mboni za Yehova? Anayambirira kuchoka kudera la nkhondo ku Bosnia. Anali ataŵerenga zofalitsidwa zina za Mboni, komano chidwi chake pa Mawu a Mulungu chinakula pamene Mboni zina ziŵiri zinamfikira panyumba kuchiyambiyambi kwa 1992. Kodi ndani amene anafikira Slobodan, akumampempha kuphunzira naye Baibulo? Anali Mujo, amenenso anachokera ku Bosnia komano yemwe analeredwa monga Msilamu. Pamene phunziro la Baibulo linapita patsogolo, Mujo ndi Slobodan, amene kale anali odana, anathera nthaŵi ali pamodzi akumalimbitsana chikhulupiriro masiku onse.

Nkhondo ya amene kale anali Yugoslavia yapha anthu zikwi mazana ambiri. Koma Branko, Slobodan, ndi Mujo tsopano akutumikira monga alaliki anthaŵi yonse a uthenga wabwino mumpingo umodzimodziwo wa Mboni za Yehova. Athetsa udani wamtundu ndi wafuko, ndipo tsopano akufuna mtendere pamene akugonjera Mlengiyo, Yehova.

Koma kodi nchiyani chimene chinapangitsa kusinthaku? Chinali chikondi chawo pa Yehova, kulemekeza kwawo Baibulo, ndi kufunitsitsa kwawo kugwiritsira ntchito choonadi cha Baibulo m’moyo wawo. Zili monga momwe Malemba Opatulika amanenera kuti, “mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, . . . nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.”​—Ahebri 4:12.

[Mawu a M’munsi]

a Tagwiritsira ntchito maina opeka.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena