Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 1/8 tsamba 30-31
  • Ndani Amene Adzayeretse Dziko Lathuli?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndani Amene Adzayeretse Dziko Lathuli?
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Anthu Angathe Paokha?
  • Dziko Loyeretsedwa—Motani?
  • Kuipitsa Kuimitsidwa Kotheratu m’Malo Ake Oyamba!
    Galamukani!—1988
  • Kodi Ndi Ndani Amene Adzapulumutse Dzikoli?
    Nkhani Zina
  • Kuipitsa Kodi Ndani Akukuchititsa?
    Galamukani!—1990
  • Kututa Kwakupha kwa Kuipitsa
    Galamukani!—1988
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 1/8 tsamba 30-31

Ndani Amene Adzayeretse Dziko Lathuli?

“NDIKULINGALIRA kuti podzafika m’chaka cha 2025, malinga ndi mmene maindasitale alili, tidzaleka kugwiritsa ntchito mawu akuti ‘kuipitsa chilengedwe.’” Awa anali malingaliro a pulezidenti wa kampani yokonza makemikolo. Kodi mukulingalira kuti zimenezo zidzatheka? Ngati ndi choncho, kodi muganiza kuti zidzatheka bwanji?

Kukonda ndalama ndiko kumapangitsa kuti mankhwala osayenera azipezeka m’masitolo. Mwachitsanzo, malamulo okhudza za chinsinsi chopangira mankhwala ophera tizilombo kuti anthu ena asadziŵe mmene amapangidwira, amati ayenera kungolembapo kuti “inert,” mawu amene amatanthauza kuti “osaopsa.” “Koma mpamene mankhwala 394 otchedwa kuti osaopsawa akhala akugwiritsidwa ntchito monga ophera tizilombo,” inatero magazini yotchedwa kuti Chemical Week. Mwa zinthu zimene amagwiritsa ntchito kukonza mankhwala amenewa, 209 ndi n’zoopsa zoipitsa chilengedwe kwambiri, ndipo 21 anazilengeza kuti zikhoza kuyambitsa kansa, ndi 127 ndi zangozi kwa amene amagwira ntchito yozikonzawo!

N’zoona kuti njira zaboma zotetezera nthaŵi zonse zakhala zothandiza. Koma wolemba wina anati, boma limadera nkhaŵa kwambiri “za kupita patsogolo kwa chuma ndi maindasitale ndi mmene phindu likupezekera.” Choncho, amasowa chochita—popeza pali kuipa ndi ubwino womwe. Zotsatira zake zimakhala ‘kuloleza kuwononga chilengedwe mwakungoika malamulo chabe kuti zisanyanyire.’

Tsono ndani nanga angatithandize? Wa Mboni za Yehova wina anafunsa mwininyumba wina amene anali waubwenzi funso limenelo . Iye anayankha mosonyeza kudalira atsogoleri ndi asayansi kuti: “Tsiku lina adzathetsa vuto limeneli.”

Mboniyo inafunsa kuti, “koma nanga adzathetsewo ndani? Kodi iwo si anthu ngati inu ndi ine? Mwina akhoza kukhala ophunzira kwambiri, koma pali zina zimene amalephera, iwo ndi ofooka. Ndiponso amalakwa.” Ndiye wonjezeranipo kuchuluka kwa mavuto amene iwo amakumana nawo kuphatikizapo umbombo ndi katangale zimene zili padziko.

Kodi nanunso mukukhulupirira kuti adzathetsa mavutoŵa? Koma mbiri yaitali ya anthu ya kulephera singapangitse munthu kudalira kuti zidzatero. Magazini yakuti Outdoor Life inati “Asayansi ndi mabungwe awo amadziwa bwino kwambiri kupima mmene chilengedwe chikuwonongekera koma sadziŵa kwenikweni mmene angakonzere zinthu.” Kodi pali mfundo zanji zosonyeza kuti anthu angathe kuthetsa vuto lalikulu limeneli?

Kodi Anthu Angathe Paokha?

Kuchepetsa vuto la kuipitsa ndi makemikolo si vuto lokhudza atsogoleri a dziko limodzi. Ichi n’chifukwa chakuti makemikolo amene anthu amagwiritsa ntchito dziko limodzi amakhudza anthu a dziko lina, mwina ngakhale kukhudza anthu padziko lonse! Ndipo anthu alephera kugwirizana kuti athetse vuto la padziko lonse limeneli. Baibulo limasonyeza chifukwa chake pamene limati: “Wina apweteka mnzake pomlamulira.” (Mlaliki 8:9) Kodi ndi chifukwa chiyani anthu satha kudzilamulira bwino okha? Kachiŵirinso Baibulo limayankha kuti: “Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Kodi zimenezo zimatanthauza chiyani?

Zimatanthauza kuti anthu sanalengedwe kuti azidzilamulira okha popanda kutsogozedwa ndi Mulungu. N’zoona kuti anthu achita zinthu zambiri—amanga nyumba zabwino, kupanga zipangizo mwaluso, ngakhale kupita ku mwezi—komabe sangathe kudzilamulira popanda kutsogozedwa ndi Mulungu. Izi ndizo zimene Baibulo limaphunzitsa, ndipo mbiri yakale imasonyeza kuti Baibulo limanena zoona.

Dziko Loyeretsedwa—Motani?

Mlengi wathu, Yehova Mulungu, nthaŵi zonse wakhala wodera nkhaŵa ndi mtundu wa anthu ndi dziko, limene anakonzera anthu. Atalenga anthu, iye anati ayenera kusamalira dziko ndi zamoyo zimene zili pamenepo. (Genesis 1:27, 28; 2:15) Pambuyo pake, pamene banja loyambirira linanyalanyaza malangizo ake, iye anapereka malangizo kwa mtundu wakale wa Israyeli okhudza kusamalira nthaka, kuphatikizapo lakuti azileka osalima kwa chaka chonse pakapita zaka zisanu n’ziŵiri zilizonse. Izi zinkathandiza kuti nthaka ibwereremo. (Eksodo 23:11; Levitiko 25:4-6) Koma anthu anakhala aumbombo ndipo sanamvere Mulungu. Iwo anavutika ndi nthakanso inawonongeka.

N’zoona kuti panthaŵiyo sizinali zotheka kuti nthaka n’kuwonongeka ndi makemikolo. Komabe nthaka inaonongeka chifukwa chakuti Aisrayeli analephera kuileka kuti ipume mogwirizana ndi mmene Mulungu anafunira, ndipo anthu osalakwa anavutika. Choncho Mulungu analola a Babulo kugonjetsa Aisrayeli ndi kuwatengera ku ukapolo ku Babulo kwa zaka 70. Chilango chimenechi chinathandiza kuti nthaka ipumule ndipo ibwereremo.—Levitiko 26:27, 28, 34, 35, 43; 2 Mbiri 36:20, 21.

Mbiri imatiphunzitsa kuti Mulungu amaŵerengera anthu mlandu pazimene akuchitira dziko. (Aroma 15:4) Ndipo Mulungu amalonjeza kuti ‘adzawononga iwo akuwononga dziko.’ (Chivumbulutso 11:18) Baibulo limalongosola momvekera bwino za anthu amene “akuwononga” dziko. Khalidwe lawo ndi lomwe linasonyezedwa m’Baibulo pa 2 Timoteo 3:1-5, limene limaphatikizapo kukonda ndalama ndi kudzikonda mpaka kufika posasamala za Mulungu ndiponso chilengedwe chake, kuphatikizapo ndi anthu omwe.

Choncho malemba aŵiri a m’Baibulo amenewa—2 Timoteo 3:1-5 ndi Chivumbulutso 11:18—amasonyeza zinthu ziŵiri. Choyamba, malingaliro olakwika amapangitsa kuwononga dziko. Chachiŵiri, Mulungu adzaloŵererapo kuti apulumutse dzikoli ndi anthu oopa Mulungu, pamene mitundu yonse iŵiri yakuwononga idzafika poipitsitsa. Kodi Mulungu adzaloŵererapo motani?

Kupyolera mwa mneneri wake Danieli, Mulungu ananeneratu kuti: “Ndipo masiku a mafumu aja [umboni umasonyeza kuti ndi maboma a masiku ano] Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu . . . [umene] udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. nudzakhala chikhalire.” (Danieli 2:44) Ufumu umenewo ndi boma lenileni la dziko lonse. Yesu Kristu anaphunzitsa ophunzira ake kuti azipempherera boma limenelo pamene ananena kuti: “Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, . . . Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.”—Mateyu 6:9, 10.

Moyang’aniridwa mwachikondi ndi Ufumu wa Mulungu, anthu okhala padziko adzasangalala ndi mwayi wabwino kwambiri wopanga dziko lonseli kukhala paradaiso. Mpweya udzakhala wabwino, mitsinje idzakhala ndi madzi abwino, ndipo nthaka idzakhala yachonde. (Salmo 72:16; Yesaya 35:1-10; Luka 23:43) Pambuyo pake Baibulo limalonjeza kuti: “Ndipo zinthu zakale [matenda aliko masiku ano, kuvutika, kuipitsa malo, ndi mavuto ena ambiri] sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.”—Yesaya 65:17.

[Chithunzi patsamba 30]

Dziko loyeretsedwa kukhala la ukhondo—kodi mudzakhalapo kuti mudzalione?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena