Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 2/8 tsamba 23-24
  • Pamene Chakudya Chimakhala Mdani Wanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pamene Chakudya Chimakhala Mdani Wanu
  • Galamukani!—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Chimapangitsa Kudya Kukhala Vuto N’chiyani?
    Galamukani!—1999
  • Vuto la Kadyedwe N’chiyani Chingathandize?
    Galamukani!—1999
  • N’chifukwa Chiyani Ndimaopa Kunenepa?
    Galamukani!—1999
  • Kuthandiza Okhala ndi Vuto Lakadyedwe
    Galamukani!—1992
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 2/8 tsamba 23-24

Pamene Chakudya Chimakhala Mdani Wanu

Akaganiza zomwe zinkachitika pomwe anali mtsikana, Jean amakumbukira bwino kuti ankanyozedwa kwambiri. Chifukwa? Iye anali mtsikana wamtali ndiponso wamkulu thupi kwambiri m’kalasi mwawo. Koma vuto lake silinali lokhalo. “Choipa kwambiri kuposa kukhala wamkulu thupi, ndinali wamanyazi ndipo ndinkangoona ngati kuti ena akungolingalira za ine. Kaŵirikaŵiri ndimasowa wocheza naye, ndipo ndimafuna kugwirizana ndi anzanga, koma nthaŵi zonse ndimaona ngati sitikufanana,” anatero Jean.

Jean ankaona ngati kuti vuto kwa iye limabwera chifukwa chakuti ndi wamkulu thupi ndipo analingalira kuti kukhala ndi thupi lochepa kudzathetsa vutolo. Sikuti Jean anali wonenepa konyanya ayi. Mosiyana ndi zimenezo, pokhala wamtali 180 cm ndipo wolemera 66 kg, sanali wonenepa kuposa mlingo. Ngakhale n’choncho, Jean ankadziona monga wonenepa kwambiri, ndipo ali ndi zaka 23, analingalira zoyamba kutsatira njira zochepetserako thupi. Iye analingalira kuti, ‘Ngati nditakhala wochepa thupi ndiye kuti anthu azifuna kumakhala nane pafupi. Ndidzapeza kuti ndine wokondedwa ndiponso wapadera.’

“Malingaliro opanda pake amenewo anapangitsa kuti ndivutike kwa zaka khumi ndi ziŵiri ndi matenda a anorexia nervosa ndi bulimia,” anatero Jean. “Ndinachepadi thupi, kuonda kwambiri ndipo ndinali pafupi kufa, koma m’malo moti ndikhale wosangalala, ndinawononga thanzi langa ndikuyamba kudandaula ndi kukhumudwa kwambiri kwa zaka zoposa khumi.”

SI Jean yekha amene zotere zinam’chitikira. Malinga nkuyerekezera kwina, mmodzi mwa akazi 100 ku America amadwala anorexia nervosa adakali wachitsikana, ndipo mwina kuŵirikiza katatu chiŵerengerochi amadwala matenda a bulimia. Dr. Mary Pipher anati: “Ndakhala ndikugwira ntchito m’masukulu ndi m’makoleji kwa zaka zambiri ndipo ndimadzionera ndekha kuti vuto la kudya mopanda muyezo ndi lofala kuposa mmene linalili kale.”

Nthendayi imachitika mwanjira zosiyanasiyana. Kale linkalingaliridwa kuti ndi vuto la anthu olemera, koma tsopano likutengedwa kuti ndi vuto la anthu a mitundu yonse, azikhalidwe za mitundu yonse, ndipo silisiyana pakati pa achuma ndi osauka. Ngakhale chiŵerengero cha amuna amene akupezeka ndi nthendayi chikuchuluka mpaka kupangitsa magazini a Newsweek kutcha matenda a kudyawa kukhala “ogwira amuna ndi akazi mosasankha.”

Koma chikudetsa nkhaŵa kwambiri n’chakuti avareji ya zaka za anthu omwe akumalandira chithandizo chifukwa cha matenda a kudya ikumka nitsika. Margaret Beck amene ndi mkulu wa dipatimenti yoona za vuto la kudya ku Toronto anati, “Pali ana a zaka zosakwana khumi mwina ochepa mpaka zaka zisanu n’chimodzi amene amakhala akulandira mankhwala kuchipatala.” Iye anawonjezera kuti, “Chiŵerengerocho chidakali chochepa koma chikukulirakulira.”

Muta penyetsetsa, kuoneka kuti vuto la kudya limakhudza anthu mamiliyoni—makamaka achitsikana.a “Iwo salingalira za zakudya kapena kudya monga mmene anthu ambiri amachitira,” anatero Nancy Kolodny, wogwira ntchito zaumoyo. “Akakhala ndi njala, m’malo moti adye kuti akhale ndi thanzi labwino ndiponso kuti asangalale, kapena kudya n’cholinga choti ikhale nthaŵi yachisangalalo pamodzi ndi anzawo, iwo amayamba kuchita zosadziŵika, kumachita zinthu zomwe tingazione kuti si ‘zoyenera’—monga ngati kuchita timiyambo tosadziŵika asanayambe kudya, kapena kufuna atachotsa m’thupi mwawo chakudya chonse chimene adya.”

Tiyeni tsopano tionepo matenda a kudya a mitundu iŵiri yofala: anorexia nervosa ndi bulimia nervosa.

[Mawu a M’munsi]

a Popeza kuti vuto la kudya limagwira kwambiri akazi kuposa amuna, m’nkhani izi tizinena za wodwalayo monga mkazi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena