Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 2/8 tsamba 29-32
  • Vuto la Kadyedwe N’chiyani Chingathandize?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Vuto la Kadyedwe N’chiyani Chingathandize?
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Malingaliro a Chikatikati Ponena za Kaonekedwe ka Thupi
  • Kupeza “Bwenzi Lokonda”
  • Ngati Kukufunikira Kuti Mukagonekedwe M’chipatala
  • Kukhala Popanda Vuto la Kadyedwe
  • Kuthandiza Okhala ndi Vuto Lakadyedwe
    Galamukani!—1992
  • Chimapangitsa Kudya Kukhala Vuto N’chiyani?
    Galamukani!—1999
  • Kodi Ndili Ndi Matenda Ovutika Kudya?
    Galamukani!—2006
  • Pamene Chakudya Chimakhala Mdani Wanu
    Galamukani!—1999
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 2/8 tsamba 29-32

Vuto la Kadyedwe N’chiyani Chingathandize?

NGATI mwana wanu wamkazi ali ndi vuto la kadyedwe, afunikira chithandizo. Musangolekerera mukumalingalira kuti vutolo litha lokha. Matenda akadyedwe n’ngovuta, amakhudza thupi ndiponso malingaliro.

Ndipo, akatswiri amanena za njira zochiritsira zosiyanasiyana zoti mutha kusokonezeka nazo. Ena amati koma mankhwala. Ena amati koma kukambirana naye. Ambiri amati kuphatikiza zonsezo mpamene amathandizika mwamsanga. Ndiye pali uphungu wochokera kwa makolo, umene ena amati ndiwo wothandiza kwambiri ngati munthuyo akukhala panyumba.a

Ngakhale kuti akatswiri amasiyana pa nkhaniyi, komabe ambiri amagwirizana pa mfundo imodzi: Matenda akudya sakhudza za chakudya chokha. Tiyeni tione mfundo zina zoyenera kulingaliridwa pofuna kuthandiza munthu kuti achire kumatenda a anorexia kapena bulimia.

Malingaliro a Chikatikati Ponena za Kaonekedwe ka Thupi

Mayi wina anati, “Ndinaleka kugula magazini a mafashoni pamene ndinali ndi zaka 24. Podziyerekezera ndi anthu ogwiritsidwa ntchito ndi osatsa malonda ndinkaona kuti zinkandisokoneza.” Monga mmene tanenera kale, osatsa malonda akhoza kusokoneza mtsikana pa nkhani ya kukongola. Mayi wina amene ali ndi mwana mtsikana wokhala ndi matenda a kudya anati “nkhani za osatsa malonda zosatha m’manyuzipepala ndi m’magazini ndi pa wailesi ya kanema n’zakuti munthu akhale woonda, woonda, woonda.” Iye anati: “Ine pamodzi ndi mwana wanga timafuna kukhala ochepa thupi kwambiri, tinapeza kuti kulakalaka kukhala ochepa matupi kunakhala chinthu chofunika kwambiri m’moyo kuposa china chilichonse.” Kuti munthu achire kumatenda a kudya kumafunika kuti munthu asinthe maganizo ake onena za chimene kukongola kwenikweni kuli.

Baibulo lingathandize pankhani imeneyi. Mtumwi wachikristu Petro analemba kuti: “Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kuvala za golidi, kapena kuvala chovala; koma kukhale munthu wobisika wamtima, m’chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.”—1 Petro 3:3,4.

Petro akuti tiyenera kudera nkhaŵa kwambiri za umunthu wamkati kuposa maonekedwe a kunja. Baibulo limatitsimikizira kuti: “Pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang’ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.” (1 Samuel 16:7) Izi n’zotonthoza kwambiri, chifukwa sitingathe kusintha mbali zina za kaonekedwe kathu, koma nthaŵi zonse tingathe kusintha mtundu wa munthu amene tili.—Aefeso 4:22-24.

Popeza matenda a kadyedwe amakula pamene munthu akudziona monga wopanda pake, muyenera kulingalirapo bwino nkuyamba kumadziona monga wofunika. Baibulo limati sitiyenera kulingalira kwambiri za ife eni kuposa pamlingo woyenera. (Aroma 12:3) Koma limatiuzanso kuti mpheta imodzi ndi yamtengo wapatali m’maso mwa Mulungu, ndipo linawonjezera kuti: “Muposa mtengo wake wa mpheta zambiri.” (Luka 12:6,7) Choncho Baibulo likhoza kukuthandizani kuti muyambe kumadzilemekeza. Kondani thupi lanu, ndipo mudzayamba kumalisamalira.—Yerekezerani ndi Aefeso 5:29.

Koma bwanji ngati kulidi koyenera kuti muyenera kuchepetsako thupi? Mwinamwake chakudya choyenera ndiponso maseŵero olimbitsa thupi ndi zofunika. Baibulo limati “chizolowezi cha thupi chipindula,” ngakhale kuti ndi pang’ono chabe. (1 Timoteo 4:8) Koma simuyenera kudera nkhaŵa kwambiri za thupi. Ofufuza za kaonekedwe ka thupi anati, “Mwinamwake chinthu chofunika koposa ndicho kuchita masewero olimbitsa thupi—ndi kungovomereza kuti mmene mulilimo ndimomwemo basi mmalo momayesa kuchita zinthu zomwe ndi anthu ochepa okha angazithe.” Mayi wina wazaka 33 wa ku United States anapeza kuti zimenezi ndi zothandiza. Iye anati, “Ndili ndi lamulo langa losavuta, ndimalimbikira kusintha chinthu chokhacho chomwe ndingathe kusintha, osataya nthaŵi ndi zina.”

Ngati mutamalingalira zinthu moyenera kuphatikizapo chakudya chopatsa thanzi ndiponso maseŵera olimbitsa thupi oyenera ndiye kuti thupi lanu lidzachepako moyenera.

Kupeza “Bwenzi Lokonda”

Polofesa James Pennebaker atafufuza za anthu odwala bulimia, iye anati vuto lawo lakuti azidya ndiye kenaka n’kuchotsa zomwe adyazo m’thupi lawo limawapangitsa kuti azikhala abodza. Iye anati, “Pafupifupi aliyense anazindikira payekha kuti zimafuna nthaŵi yambiri ndi khama kuti azibisira anzake ndi banja lake za khalidwe lake. Onseŵa ankanama ndipo ankadana nazo kwambiri.”

Choncho njira imodzi yothandiza kuti muchire ndiyo kulankhula. Odwala bulimia ndi odwala anorexia ayenera kulankhula za vutolo. Koma nanga alankhule ndi ndani? Mwambi wa m’Baibulo umati: “Bwenzi limakonda nthaŵi zonse; ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.” (Miyambo 17:17) “Bwenzi lokonda” limeneli lingathe kukhala kholo kapena munthu wina wachikulire. Ena aona kuti n’zothandiza kuuza munthu wodziwa kuchiritsa matenda a kadyedwe.

Mboni za Yehova zili ndi gulu linanso—akulu mumpingo. Anthu amenewa akhoza kukhala monga “pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m’malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.” (Yesaya 32:2) Komabe, sikuti akulu ndi madokotala ayi, choncho kuwonjezera pa uphungu wawo wothandiza, mufunikirabe chithandizo cha mankhwala. Komabe, anthu ofikapo mwauzimu amenewa akhoza kukhala othandiza kwambiri pamene mukuchira.b—Yakobo 5:14, 15.

Komabe munthu amene mungamuze zambiri ndi Mlengi wanu. Wamasalmo analemba kuti: “Umsenze Yehova nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza: Nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” (Salmo 55:22) Inde, Yehova Mulungu amakonda ana ake a padziko lapansi. Choncho musazengereze kupemphera kwa iye kunena za nkhaŵa zanu za pansi pa mtima. Petro amalangiza kuti: ‘mutaye pa Iye nkhaŵa yanu yonse pakuti Iye asamalira inu.’—1 Petro 5:7.

Ngati Kukufunikira Kuti Mukagonekedwe M’chipatala

Kukagonekedwe m’chipatala mwa iko kokha sikungakuchiritseni. Komabe, ngati mtsikana wakhala wopanda zakudya zokwana m’thupi chifukwa cha anorexia, kungakhale koyenera kuti iye alandire chithandizo ku chipatala. N’zomveka kuti si chapafupi kwa makolo kuchita zimenezi. Lingalirani zimene Emily, amene mwana wake wamkazi anafunikira kukagonekedwa ku chipatala pamene, malinga ndi kunena kwa Emily, moyo “unafika povuta kwa iye ndi ife tomwe.” Iye anawonjezera kuti: “Kupita naye kuchipatala akulira ndicho chinthu chovuta kwambiri chimene ine ndakumana nacho, tsiku loipa kwambiri kwa ine m’moyo wanga.” Zinalinso choncho ndi Elaine, amenenso anafunikira kuti mwana wake akamugoneke m’chipatala. Iye anati, “Ndikhulupirira kuti nthaŵi imene inandiipira kwambiri yomwe ndikukumbukira ndi pamene anali m’chipatala ndipo ankakana kudya choncho ankam’dyetsera m’mitsempha. Ndinkaona ngati kuti anam’kakamiza kuchita zomwe iye samafuna.”

Kukhala kuchipatala mwina sikungasangalatse, koma nthaŵi zina kungakhale koyenera. Kumathandiza kwambiri kuti anthu ambiri omwe ali ndi vuto la kadyedwe achire. Emily ponena za mwana wake anati: “Iye anafunikiradi kuchipatala. Anayamba kupeza bwino chifukwa chakuti anakagona m’chipatala.”

Kukhala Popanda Vuto la Kadyedwe

Mbali ina yachithandizo kwa odwala anorexia kapena bulimia amafunikira kuti aphunzire kukhala popanda vuto la kadyedwe. Izi zingakhale zovuta. Mwachitsanzo, Kim amayerekezera kuti panthaŵi imene ankadwala anorexia, sikelo yake inatsika ndi makilogalamu 18 m’miyezi khumi. Koma kuti thupi libwereremo kuonjezera makilogalamu 16 zinam’tengera zaka zisanu ndi zinayi! Kim anati, “Ndinavutika kwambiri kuti ndiyambirenso kumadya bwino monga kale, popanda kuŵerengetsera za ma calorie, kuyesa chakudya changa, kudya chakudya choyenera chokha, kudera nkhaŵa ndikadya zakudya zomwe sindikuzidziŵa bwino, ndipo osamadanso nkhaŵa ngati ndadya ku resitilanti.”

Koma kuchira kwa Kim kunam’thandiza kuzindikira kanthu kena. Iye anati, “Ndinazindikira kuti ndiyenera kumalankhula zimene ndikulingalira kuposa kumangochita zina zake kapena kuyamba kumangolimbana ndi zakudya. Kuzindikira njira zatsopano zothetsera mikangano ndi ena kunapangitsa kuti pakhale ubwenzi ndi anzanga ndiponso abale anga.”

N’zomveka kuti munthu achire matenda okhudza kadyedwe n’kovuta, koma potsiriza kumapezeka kuti n’kofunika. Izi ndizo zimene Jean, amene tinamugwira mawu mu nkhani yoyambirira ija, amakhulupirira. Iye anati, “Kuyambiranso kwa vuto la kadyedwe kukhoza kukhala ngati kubwereranso kuchipatala pamene unachira kwa kanthaŵi.”

Ngati mungafune kudziŵa zambiri kapena kuti wina aziphunzira nanu Baibulo panyumba panu kwaulere, lemberani ku Watch Tower, Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku adiresi yoyenera pa maadiresi osonyezedwa patsamba 2.

[Mawu a M’munsi]

a Galamukani! sichirikiza machiritso a mtundu ulionse. Akristu ayenera kulingalirapo bwino okha, kusamala kuti machiritso alionse amene asankha sakuombana ndi mapulinsipulo a Baibulo. Ena sayenera kutsutsa kopena kuweruza pa zimenezo.

b Kuti mumve zambiri zonena za mmene mungathandizire odwala anorexia ndi bulimia, onani nkhani zakuti “Kuthandiza Okhala ndi Vuto Lakadyedwe,” mu in Galamukani! ya March 8 1992, ndi nkhani zakuti “Eating Disorders—What Can Be Done?,” mu Galamukani! yachingelezi ya December 22, 1990.

[Bokosi patsamba 31]

Zofunika Kuchita kuti Munthuyo Achire

KODI n’chiyani chimene mungachite ngati mukuona kuti mwana wanu ali ndi vuto la kudya? N’zodziŵikiratu kuti simungalinyalanyaze vutolo. Koma nanga mungayambe bwanji kukambirana za nkhaniyo? Michael Riera anati, “Kumufunsa mwachindunji nthaŵi zina kumathandiza, koma malinga ndi mmene zakhala zikuchitikira nthaŵi zambiri, sanena.

Pachifukwa chimenechi, kungakhale kothandiza kwambiri kumufikira momunyengerera. Riera anati, “Pamene mukulankhula ndi mwana wanu, iyeyo sayenera kuona kuti mukumuimba mlandu kuti walakwa chinachake. Ngati mungathe kum’pangitsa kulingalira choncho, nthaŵi zambiri ana ambiri amatha kunena zoona, mwinanso adzaona ngati kuti mwam’masula ku vuto lake. Makolo ena zinawapindulira mwanjira ya kulembera ana awo achinyamatawo makalata kulongosola za nkhaŵa zawo ndi chithandizo chimene angapereke. Choncho, panthaŵi imene adzayamba kukambirana, kumakhala kuti anayala kale maziko.”

[Bokosi patsamba 32]

Ntchito Yovuta ya Makolo

MAKOLO amavutika kwambiri ngati mwana wawo ali ndi vuto la kadyedwe. Bambo wina anati, “Uyenera kulimba kwambiri kuti umthandize mwanayo. Umakhala ukuona mwana wako akuwonongeka.”

Ngati muli ndi mwana amene ali ndi vuto la kadyedwe, simuyenera kukayikira kuti nthaŵi zina mwanayo adzakukhumudwitsani chifukwa chosamva zimene mukunena. Koma musataye mtima. Musasiye kumusonyeza chikondi. Emily amene mwana wake ankadwala anorexia, anavomereza kuti siinali ntchito yapafupi. Komabe iye ananena kuti: “Nthaŵi zonse ndinkamugwira; ndinkayesera kumukumbatira; kumupsopsona. . . . Ndinkaona kuti ngati ndisiya kumusonyeza chikondi, sitidzagwirizananso.”

Njira ina yothandizira kuti mwana wanu athetse vuto lake la kadyedwe ndiyo kukambirana naye. Pochita zimenezo, muyenera kumamvetsera kwambiri osati kulankhula kwambiri. Chonde pewani kumamdula mawu mwakunena mawu monga akuti, “Zimenezo si zoona” kapena kuti, “Suyenera kumalingalira choncho.” Chonde, ‘osatseka makutu anu polira waumphawi.’ (Miyambo 21:13) Pakakhala kukambirana kwabwino, ndiye kuti mwana adzapeza koti azinena zinthu zikamuvuta motero sangamathetse mavuto ake mwakudya chakudya mosayenera.

[Zithunzi patsamba 30]

Pamafunikira kudekha, kumvetsa zinthu, ndiponso chikondi chachikulu kuti muthandize amene ali ndi vuto la kadyedwe

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena