Ngakhale Ndili Wakhungu Ndili Wofunika ndi Wachimwemwe
Yosimbidwa ndi Polytimi Venetsianos
Ndinkaseŵera ndi achimwene anga aŵiri, mkulu wanga ndi msuweni wanga. Kenaka kanthu kena kanaloŵera pawindo. Inali grenade, ndiye pamene inaphulika, abale anga atatu onsewo anaphedwa, koma ine ndinachitiratu khungu.
DETI lake linali July 16, 1942, pamenepo n’kuti ndili kamtsikana kazaka zisanu zokha. Kwa masiku angapo ndinkangokomokakomoka. Ndikatsitsimuka, ndinkafunafuna achimwene anga ndi mkulu wanga. Nditamva kuti afa, inenso ndinakhumbira kufa.
Pamene ndinabadwa, n’kuti makolo anga akukhala pa chilumba chotchedwa Salamis, ku Greece, pafupi ndi Piraievs, doko la Athens. Ngakhale kuti tinali osauka, moyo wathu unali wamtendere. Zonsezo zinatha nthaŵi imodzi pamene Nkhondo Yadziko II inayamba, mu 1939. Bambo wanga anali m’malinyero panyanja ya Mediterranean. Nthaŵi zambiri ankafunikira kuzemba sitima zapanyanja zotchedwa submarines, frigates, kuzemba mabomba a torpedoe, ndiponso kuzemba mabomba a asilikali a mbali yathu ndi mabomba a asilikali a adani. Greece anali kulamulidwa ndi Italy ndiponso Germany.
Ndinaphunzitsidwa Kuda Mulungu
Mwana wachinayi wa amayi anamwalira chifukwa cha mikhalidwe yovuta panthaŵi yankhondo. Mayi anavutika maganizo koopsa, anadwalanso chifuwa cha TB, ndiyeno atabala mwana wachisanu ndi chimodzi, iwowo anamwalira mu August 1945. Anansi athu achipembedzo anayamba kunena kuti Mulungu anali kutilanga. Ansembe ena a tchalitchi cha Greek Orthodox ankayesa kuti akutilimbikitsa pomwe ankangowononga zinthu potiuza kuti Mulungu anali atatenga achimwene anga ndi akulu anga kuti akakhale tiangelo kumwamba.
Bambo anapsa mtima. Kodi Mulunguyo angatenge bwanji tiana tinayi m’banja losauka pomwe iye ali ndi angelo ambirimbiri kuli iyeko? Zikhulupiriro zimenezi za Tchalitchi cha Orthodox zinawapangitsa bambo kudana naye Mulungu mpaka kudananso ndi chipembedzo. Kenaka, sankafunanso kupita kutchalitchi. Anandiphunzitsa kuda Mulungu, akumati Mulungu ndiye anali kutizunza.
Ngati Chilombo mu Mpanda
Mayi wanga atangomwalira kumene mu 1945, Bambonso nawo anadwala chifuwa cha TB, ndiye anagonekedwa m’chipatala cha anthu odwala matenda ovuta. Mng’ono wanga, anakam’lembetsa sukulu yamkaka. Kenaka, pamene Bambo anatuluka m’chipatala, n’kupita kusukulu yamkaka kuti akam’tengeko, anamva kuti anamwalira. Ineyo anakandilembetsa kusukulu ya anthu akhungu, kumene ndinakhalako zaka zina zisanu ndi zitatu za moyo wanga. Poyamba ndinali wachisoni. Zinthu zinali kundiipira kwambiri pamasiku omwe makolo amabwera kudzaona ana. Anzanga ambiri akhungu pasukulupo ankalandira munthu wina wowachezera, koma ine panalibe aliyense wodzandichezera.
Ndinkangokhala ngati chilombo mumpanda. Ndinkatchedwa munthu wovutitsa pasukulupo. Ndiye ankandimenya n’kundikhazika ‘pampando wa ana opulupudza.’ Nthaŵi zambiri ndinkaganiza zodzipha. Komabe, pakupita kwa nthaŵi, ndinaphunzira kuti ndinayenera kuphunzira kudzidalira. Ndinayamba kukondwa ndikamathandiza ana anzanga akhungu, nthaŵi zambiri kuwathandiza kuvala kapena kuyala mabedi awo.
Ansembe ankatiuza kuti Mulungu anatichititsa khungu chifukwa chakuti makolo athu anali atachita machimo ena aakulu kwambiri. Zimenezo zinangondipangitsa kuda Mulungu kwambiri, chifukwa ankaoneka kuti anali woipa ndiponso wankhanza. Mfundo ina yachipembedzo yomwe inkandiopsa ndi kundiputira msunamo inali yakuti mizimu ya anthu akufa imayendayenda nimavutitsa anthu amoyo. Choncho, ngakhale kuti ndinkakonda ana anzanga m’banja mwathu limodzi ndi mayi, koma ndinkaopa “mizimu” yawo.
Bambo Ndiwo Anandithandiza
Patapita nthaŵi, Bambo anakumana ndi Mboni za Yehova. Anadabwa atamva m’Baibulo kuti Satana ndiye woyambitsa mavuto ndi imfa, osati Yehova. (Salmo 100:3; Yakobo 1:13, 17; Chivumbulutso 12:9, 12) Posakhalitsa, bambo wanga ataphunzira bwino, anayamba kupita nawo kumisonkhano ya Mboni za Yehova, anapita patsogolo mwauzimu, ndiyeno anabatizidwa mu 1947. Miyezi ingapo zimenezo zisanachitike, n’kuti atakwatiranso, moti pamenepo n’kuti ali ndi mwana mmodzi. Posakhalitsanso, mkazi wawo watsopanoyo nayenso anayamba kulambira Yehova.
Nditafika zaka 16, ndinasiya sukulu ya ana akhungu. Ndinatonthozekatu zedi kubwerera kubanja lachikristu! Ankakambirana nkhani ina yomwe ankaitcha kuti phunziro la Baibulo la banja, ndiye ankandipempha kuti ndizikhalapo. Inenso ndinkangokhalirapo kuti ndiwapatse ulemu ndi kutinso ndisaoneke ngati wonyoza, komabe sindinkamvetsera kwenikweni. Mulungu ndinali ndidakanyansidwa naye, chipembedzonso ndinkachida.
M’banja lathu ankaphunzira kabuku kakuti God’s Way Is Love. Poyamba, ndinalibe nazo ntchito, komano ndinadzamva Bambo akunena za mmene anthu akufa alili. Nditamva zimenezo ndinakhala tsonga. Anaŵerenga m’Baibulo pa Mlaliki 9:5, 10, kuti: “Pakuti amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bi . . . Mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziŵa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.”
Ndinayamba kuzindikira kuti ndinkaopa zinthu zosayenera kuopa. Mayi wanga wakufa, achimwene anga, ndi akulu anga sanali oti angandivulaze. Ndiyeno nkhaniyo inayamba kukhudza za chiukiriro. Mpamene ndinayambano kumvetsera kwambiri. Mtima wanga unakondwa nditamva lonjezo la Baibulo kuti mu ulamuliro wa Kristu, anthu akufa adzakhalanso moyo! (Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 20:12, 13) Tsopano phunzirolo linayamba kundisangalatsa. Moti ndinkaona ngati kuti tsiku loti banja lidzakhalenso pansi n’kuphunzira likuchedwa kwambiri, ndipo ngakhale ndili wakhungu, koma ndinkakonzekera bwino.
Ndinayamba Kuona Mwauzimu
Pamene ndinayamba kudziŵa zambiri za m’Malemba, ndinaiŵaliratu zoti Mulungu n’ngwachabe ndi ntchito zake zomwe. Ndinadziŵa kuti si Mulungu yemwe anandichititsa khungu kapena kuchititsa khungu wina aliyense, koma kuti Mdani wa Mulungu, Satana Mdyerekezi, ndiye muzu wa zoipa zonse. Ndinamva chisoni kwambiri kuti chifukwa cha kusadziŵa kwanga, ndinkamuimba mlandu Mulungu! Ndinapitirizabe mwakhama kudziŵa Baibulo molongosoka. Ngakhale kuti tinkakhala kutali kwambiri ndi Nyumba ya Ufumu, komabe ndinkafika pamisonkhano yonse yachikristu ndiponso kutengamo mbali. Ndinkagwira nawonso ntchito yolalikira, sindinkalephera chifukwa choti ndinali wakhungu.
Ndinakondwatu zedi pamene ndinabatizidwa pa July 27, 1958, patapita zaka zoposa 16 chichitikire ngozi ija imene inandichititsa khungu! Zinali ngati kungoyamba kumene moyo watsopano ndipo ndinali ndi chiyembekezo chakuti moyo wam’tsogolo udzakhala wokondweretsa. Tsopano moyo wanga unali ndi cholinga—kutumikira Atate wanga wachikondi wakumwamba. Nditangom’dziŵa, ndinamasuka kuziphunzitso zonyenga ndipo ndinalimba mtima, moti ndinatsimikiza kulimbana ndi mavuto akukhala wakhungu, ndipo ndinalibe chisoni. Polalikira ena uthenga wabwino waulemerero, nthaŵi zambiri pamwezi ndinkakwanitsa maola 75 kapena kuposapo.
Kutha kwa Ukwati
Mu 1966, ndinakwatiwa ndi mwamuna yemwenso anali ndi zolinga ngati zanga m’moyo. Tinaganiza kuti tidzakhala ndi banja lachimwemwe popeza tonse tinkalimbikira kuchita zambiri pantchito yathu yolalikira. Kwa miyezi yambiri tinkagwira ntchito kwa maola ambirimbiri pantchito yopulumutsa moyoyi. Tinasamukira kudera lakutali kufupi ndi Livadia, chigawo chapakati cha Greece, ndiye tili kumeneko tinathandiza anthu angapo kuphunzira choonadi cha m’Baibulo n’kukhala Akristu obatizidwa. Tinakondwanso kuthandiza kampingo kena ka Mboni za Yehova m’dera lomwelo.
Komabe, patapita nthaŵi, mwamuna wanga anayamba kunyalanyaza kuphunzira Baibulo, osapezekanso pamisonkhano yachikristu, ndipo potsirizira anangolekeratu ziphunzitso za Baibulo. Zimenezo zinapangitsa ukwati wathu kuvuta kwambiri, moti mu 1977 tinalekana. Ndinakhumudwa kwambiri.
Moyo Wosangalatsa, Wopindulitsa
Panthaŵi yomvetsa chisoni kwambiri m’moyo wanga ngati imeneyi, Yehova ndi gulu lake anandithandizanso. Mbale wina wachikristu, wachikondi, anandifotokozera kuti, ndikamamva chisoni chifukwa cha zimene mwamuna wanga wakale anandichitira, ndiye kuti ndidzakhala kapolo wake. Zidzakhala ngati kuti iyeyo ndiye chimwemwe changa. Patangopita kanthaŵi, mlongo wina wachikulire mumpingo wachikristu anapempha kuti athandizidwe kulalikira. Posachedwa ndinayamba kutanganidwa ndi zimene zinkandisangalatsa kwambiri—kugwira ntchito yolalikira!
Kenaka Mkristu wina anandiuza kuti: “Ungamathandizebe kwina ndi kwina kumene ukufunika kwambiri. Yehova Mulungu angamakugwiritse ntchito monga chotsogoza anthu.” Linali ganizo losangalatsa zedi! Yehova “kugwiritsa ntchito munthu wakhungu monga chotsogoza”! (Afilipi 2:15) Sindinachedwe ayi, ndinasamuka mu Athens n’kupita kukakhala m’mudzi wina wa Amarinthos, cha kummwera kwa Evvoia, dera lokhala ndi anthu ophunzitsa Baibulo oŵerengeka kwambiri. Mabwenzi kumeneko anathandizana kundimangira nyumba ndi kundithandiza kupeza zofunika zokwanira.
Choncho, kwa zaka zoposa 20 tsopano, chaka chilichonse ndakhala ndikupatula miyezi ingapo yowonjezera ntchito yanga yolalikira. Yehova amandipatsa mphamvu, moti ndimagwira nawo ntchito yolalikira mwa njira zonse, kuphatikizapo kufikira anthu panyumba zawo, kuphunzitsa Baibulo anthu okondwerera, ndi kulankhula ndi anthu pamisewu. Pakali pano, ndimachita maphunziro a Baibulo anayi ndi anthu ofuna kudziŵa za Mlengi wathu. Ndinakondwa kwambiri kuona mipingo itatu ikukhazikitsidwa m’dera lino limene munali abale oŵerengeka zaka 20 zapitazo!
Ndimayenda makilomita oposa 30 kupita ndi kubwera, kaŵiri pamlungu, kuti ndikapezeke pamisonkhano yachikristu, ndimatsimikiza kuti ndisaphonye ngakhale umodzi. Ngati ndaona kuti maganizo anga akuganiza zina—chifukwa chakuti sindimuona wokamba nkhaniyo—ndimagwiritsa ntchito kabuku kanga ka Braille kulembamo notsi zachidule. Ndikamatero ndiye kuti ndimaumiriza makutu anga ndi maganizo anga kukhala tcheru. Ndiponso, ndili ndi mwayi wakuti msonkhano wina wampingo timauchitira m’nyumba mwanga. Anthu amachokera kumidzi yapafupi kudzakhala pa msonkhano umene timatcha Phunziro la Buku la Mpingo. M’malo moyembekezera kuti anthu azidzandichezera kunyumba kwanga nthaŵi zonse, inenso ndimakawachezera, ndipo chimenecho n’chinthu chimene chimatilimbikitsa tonse.—Aroma 1:12.
Pamene ndinkakhala ndi bambo wanga ndili wamng’ono, sankachita nane ngati mwana wakhungu. Moleza mtima ndi mobwerezabwereza, ankatha nthaŵi yaitali akumandiphunzitsa kuchita zinthu ndi manja anga. Chifukwa chakuti anandiphunzitsa zonse, ndimadziŵa kusamalira dimba langa ndi ziŵeto zanga zoŵerengeka. Ndimagwira ntchito kwambiri panyumba, kukonza m’nyumba ndi kuphika zakudya. Ndaphunzira kuti zinthu zochepa pamoyo, zimene tili nazozo, n’zimene zimatisangalatsa ndi kutipatsa chimwemwe. Ndakhoza kuchita zinthu zambiri mogwiritsa ntchito zinthu zinayi—kumva, kununkhiza, kulaŵa zinthu, ndi kukhudza zinthu—zimenezi zimandipatsa chimwemwe chosaneneka. Ndipo zakhalanso umboni wabwino kwa anthu akunja.
Mulungu Akundichirikiza
Ambiri amadabwa kuti ngakhale ndili wakhungu ndimadzichitira zinthu ndipo sindidandaula. Izozo si kanthu, koma woyenera kutamandidwa ndiye Yehova, “Mulungu wa chitonthozo chonse.” (2 Akorinto 1:3) Pamene ndinangochita khungu, nthaŵi zonse ndinkaganiza zodzipha. Choncho, sindikukhulupirira kuti ndikanakhala wamoyo lero ndikanapanda kudziŵa Yehova ndi choonadi cha m’Baibulo. Ndafikira pakuzindikira kuti Mlengi wathu anatipatsa mphatso zambiri—osati maso chabe—moti kuzigwiritsa ntchito zimenezo, tingapeze chimwemwe. Tsiku lina pamene Mboni zina zinkalalikira m’mudzi wathu, mkazi wina anawauza kuti: “Mulungu yemwe mayi amene uja amalambira ndiye amam’thandiza kuchita zinthu zonsezi!”
Ziyeso zanga zonse zandipangitsa kuyanjana ndi Mulungu. Zalimbitsa chikhulupiriro changa kwambiri. Ndimakumbukira kuti mtumwi Paulo nayenso anavutika ndi vuto limene anatcha kuti “munga m’thupi,” mwinadi anali maso omwe ankam’vuta. (2 Akorinto 12:7; Agalatiya 4:13) Zimenezo sizinam’lepheretse ‘kupsinjidwa,’ [“kutanganidwa,” NW], ndi uthenga wabwino. Inenso ndinganene monga ananenera iyeyo, kuti: “Makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m’mafooko anga . . . Pakuti pamene ndifooka, pamenepo ndili wamphamvu.”—Machitidwe 18:5; 2 Akorinto 12:9, 10.
Kuposa zonse, chiyembekezo changa chomwe ndapeza m’Baibulo chakuti pomadzaukitsidwa anthu ndidzaonanso ndi maso anga omwewa mayi wanga, akulu anga, ndi achimwene anga, chimandisangalatsa ndipo ndapindula nacho kwambiri. Baibulo limalonjeza kuti “maso a akhungu adzatsegudwa” ndi kutinso “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Yesaya 35:5; Machitidwe 24:15) Ndimati ndikaganiza zimenezo ndimamva bwino kwabasi ndipo ndikudikira mwachidwi tsogolo laulemerero limenelo mu Ufumu wa Mulungu!
[Chithunzi patsamba 15]
Bambo wanga, ndiwo ankaphunzira nane Baibulo
[Chithunzi patsamba 15]
Ndili m’khichini mwanga
[Chithunzi patsamba 15]
Ndili ndi mnzanga mu utumiki