Tsoka la Nkhondo
KUMALO ena oonetsera zinthu zamakedzana otchedwa Imperial War Museum mumzinda wa London, ku England, alendo odzacheza amachita chidwi ndi koloko yapadera yokhala ndi poonetsera manambala oŵerengera. Koloko imeneyi si ya nthaŵi. Cholinga chake n’kudziŵitsa anthu za chinthu chachikulu kwambiri m’zaka za zana lino—nkhondo. Muvi wa koloko imeneyi ukamazungulira, chipangizo choŵerenga manambalacho chimawonjezera nambala ina pa mndandanda wa manambala ake pamasekondi 3.31 alionse. Nambala iliyonse imaimira mwamuna, mkazi, kapenanso mwana amene wafa chifukwa cha nkhondo m’zaka za zana la 20 lino.
Chipangizo choŵerenga chimenechi chinayamba ntchito yake yoŵerengera mu June 1989. Podzafika pakati pa usiku wa December 31, 1999, kuŵerengerako kudzatha. Panthaŵiyo chidzakhala chitaŵerengera anthu mamiliyoni zana limodzi, chiŵerengero chongoyerekeza cha anthu amene afa pankhondo m’zaka 100 zapitazo.
Tangoganizirani, anthu mamiliyoni zana limodzi! Chimenecho n’chiŵerengero choposa kuŵirikiza kaŵiri chiŵerengero cha anthu onse ku England. Komabe, chiŵerengerochi sichikuvumbula za mantha ndi zoŵaŵa zimene anthu ameneŵa anakumana nazo. Ndiponso sichikufotokoza za kuvutika kwa achibale ndi mabwenzi a anthu akufawo—amayi, abambo, alongo, abale, akazi amasiye, ndi ana amasiye zikwi zosaŵerengeka. Zimene chiŵerengero chimenechi chikutiuza n’zakuti: M’mbiri yonse ya anthu, mbadwo wathu uno ndiwo wakhala wowononga monyanyira kwambiri; ndipo nkhanza zake n’zosayerekezeka.
Mbiri ya m’zaka za zana la 20 imasonyezanso mmene anthu apitira patsogolo m’luso la kupha. M’mbiri yonse, ntchito yopanga zida zamakono inkachitika pang’onopang’ono mpaka kudzafika m’zaka za zana la 20 lino, ndipo kwapangidwa zida miyulumiyulu. Pamene nkhondo yoyamba yapadziko lonse inayamba mu 1914, magulu ankhondo a ku Ulaya anaphatikizapo amuna okwera pa akavalo, onyamula nthungo. Masiku ano, mothandizidwa ndi zipangizo zojambula zokhala ku masetilaiti, ndiponso makompyuta owayendetsa, mabomba ouluka akhoza kupha anthu kulikonse padziko lapansi mosaphonya m’pang’ono pomwe. Kuchokera nthaŵi imeneyo taona kupita patsogolo m’luntha lopanga mfuti, akasinja, sitima zankhondo za m’madzi, ndege zankhondo, zida zofalitsa tizilombo toyambitsa matenda, zida za mankhwala akupha, inde, ngakhalenso bomba la atomu.
Chodabwitsa n’chakuti mtundu wa anthu wakhala ndi luso kwambiri lopanga nkhondo imene tsopano yakhala maseŵera amene mtundu wa anthu sungathenso kuseŵera. Mofanana ndi munthu amene zochita zake zingam’dzetsere tsoka, nkhondo nayonso ikufuna kuwononga amene anaipatsa mphamvu zochuluka chonchi. Kodi nkhondo imeneyi ingalamulirike kapena kuthetsedwa? Nkhani zotsatira zidzayankha funso limeneli.
[Mawu a Chithunzi patsamba 11]
Chithunzithunzi cha U.S. National Archives
Chithunzithunzi cha U.S. Coast Guard
Mwachilolezo cha Imperial War Museum