Zochitika Padzikoli
Kafukufuku amene anachitidwa ndi bungwe la BBC, anasonyeza kuti “katangale ndi vuto limene anthu amakonda kwambiri kukamba.” Komabe, akuti vuto lalikulu limene anthu akukumana nalo padziko lonse si katangale koma umphawi. Kafukufukuyu anachitidwa m’mayiko 26 ndipo pa kafukufukuyu anafunsa anthu okwana 13,000.—BBC NEWS, BRITAIN.
“Matchalitchi ambiri ku America akugwiritsa ntchito kachipangizo kenakake kotchedwa GPS kuti adziwe kumene kuli zithunzi zawo zosonyeza Yesu ali khanda zikabedwa. Akuchita zimenezi chifukwa chakuti m’zaka zaposachedwapa anthu akhala akuba kwambiri zithunzi zimenezi m’dzikoli.”—THE WEEK, U.S.A.
“Komiti yolangiza dziko la America pa nkhani ya zakudya ndi mankhwala ikulimbikitsa boma kuti lisamalole anthu amene amadwala matenda ochititsa munthu kumangokhala wotopa kupereka magazi m’zipatala. Iwo akuchita zimenezi chifukwa chakuti anthu ena akhala akudandaula kuti anthu odwala matenda amenewa nthawi zina amakhalanso ndi matenda osachiritsika.”—THE WALL STREET JOURNAL, U.S.A.
Magetsi Opha Tizilombo
Akatswiri a sayansi ayamba kupanga magetsi enaake oti azigwiritsidwa ntchito m’zipatala ophera tizilombo toyambitsa matenda. Magetsiwa apangidwa pa yunivesite ya Strathclyde, ku Glasgow, m’dziko la Scotland. Njira imeneyi ndi yabwino kwambiri kusiyana ndi kusesa, kukolopa, kapena kugwiritsa ntchito mankhwala ophera tizilombo. Pulofesa John Anderson anafotokoza kuti magetsiwa amawapanga kuti aziwala mwanjira inayake ndipo akatero amapha mabakiteriya.
Kudula Mitengo Kukuwonjezera Vuto la Malungo
Kudula mitengo m’nkhalango za ku Africa kukuchititsa kuti vuto la malungo liwonjezeke ndi 50 peresenti. Lipoti limeneli linanenedwa ndi akatswiri amene anachita kafukufuku wokhudza nkhani imeneyi, m’zipatala 54 za ku Brazil. Pochita kafukufukuyu, iwo anagwiritsiranso ntchito zithunzi zojambulidwa ndi setilaiti zosonyeza mmene mitengo yakhala ikudulidwira. Udzudzu umene umafalitsa kwambiri malungo m’dera limeneli ndi wotchedwa Anopheles darlingi. Munthu amene anatsogolera pa kafukufukuyu, dzina lake Sarah Olson, ananena kuti: “Malo amene mitengo yake yadulidwa, amakhala ndi zithaphwi, zimene zimachititsa kuti udzudzuwu uziswana kwambiri.” Zinapezeka kuti m’madera amene anthu anadula kwambiri mitengo ndi mmenenso malungo anavuta kwambiri.
Nyama Yam’madzi Youluka
Zithunzi za nyama inayake yam’madzi yotchedwa squid, zasonyeza kuti nyamayi imatha kuuluka. Mwachitsanzo, akatswiri a nyama zam’madzi apeza kuti “nyama yotereyi yaitali masentimita 20, ikhoza kudumphira m’mwamba mpaka mamita awiri, kenako n’kuyenda mtunda winanso wa mamita 10, uku ikukupiza zipsepse ndi mchira wake.” (Scientific American) Zimene nyamayi imachita ikafuna kudumphira m’mwamba n’zakuti, imamwa madzi kenako n’kuwalavula mwamphamvu. Zimenezi zimachititsa kuti ikhale ndi mphamvu yodumphira m’mwamba. Zithunzi zikusonyeza kuti kenako nyamayi imauluka pogwiritsa ntchito zipsepse zake ngati mapiko.