Zamkatimu
April 2013
© 2013 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Ulamuliro wonse pa magazini ino n’ngwathu.
NKHANI YA PACHIKUTO N’zotheka Kuthetsa Nkhanza za M’banja Tsamba 8 Mpaka 11
16 Mukhoza Kulowa pa Webusaiti Yathu Mosavuta
MUNGAPEZE ZAMBIRI PA WEBUSAITI YA
ACHINYAMATA
ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA
Kodi Ndingatani Ngati Anzanga Amandivutitsa Kusukulu?
Mtsikana wina yemwe ali ndi zaka 20, dzina lake Celine, ananena kuti: “Sindidzaiwala mayina amene anzanga ankandipatsa komanso mawu amwano omwe ankandinena kusukulu. Zomwe ankandinenazo zinkandipangitsa kudziona kuti ndine munthu wachabechabe, wosafunika komanso wopanda nzeru. Ndimaona kuti zikanakhala bwino akanamandimenya kusiyana n’kundinena mawu achipongwewo.” Nkhani ya pa Intaneti imeneyi ikuyankha mafunso monga akuti: N’chifukwa chiyani ana ena amakonda kuvutitsa anzawo? Ndani amene nthawi zambiri amavutitsidwa? Kodi mungatani ngati anzanu amakuvutitsani?
(Fufuzani pa mawu akuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA/ACHINYAMATA)
ANA
Werengani nkhani zomwe zafotokozedwa pogwiritsa ntchito zithunzi. Gwiritsani ntchito nkhanizi kuthandizira ana anu kudziwa zambiri za anthu otchulidwa m’Baibulo komanso kuwathandiza kuti akhale ndi makhalidwe abwino.
(Fufuzani pa mawu akuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA/ANA)