Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g23 No. 1 tsamba 12-14
  • Mpweya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mpweya
  • Galamukani!—2023
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mpweya Ukuwonongeka
  • Dzikoli Linapangidwa M’njira Yoti Lizitha Kudzikonza Lokha
  • Zimene Anthu Akuchita Kuti Athetsa Vutoli
  • Kodi Baibulo Limatipatsa Chiyembekezo Chotani?
  • Bwenzi Kukanakhala Mpweya Wabwino!
    Galamukani!—1996
  • Mizinda Yaikulu Ikupuyira Pang’onopang’ono
    Galamukani!—1994
  • Kuipitsa Kodi Ndani Akukuchititsa?
    Galamukani!—1990
  • Kututa Kwakupha kwa Kuipitsa
    Galamukani!—1988
Onani Zambiri
Galamukani!—2023
g23 No. 1 tsamba 12-14
Banja likuyenda pa sinowo ndipo likuyang’ana nyanja yomwe m’mbali mwake muli mapiri.

KODI DZIKOLI LIDZAKHALANSO BWINO?

MPWEYA

TIMAFUNIKA mpweya, koma osati kuti tizingopuma basi. Mpweya umateteza dziko lathuli ku mphamvu yoipa yochokera ku dzuwa. Popanda mpweya, padzikoli pakhoza kuzizira kwambiri moti chilichonse chikhoza kuuma.

Mpweya Ukuwonongeka

Kuwonongeka kwa mpweya kukhoza kuchititsa kuti zamoyo zonse padzikoli zife. Mogwirizana ndi zimene Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse linanena, munthu mmodzi pa anthu 100 alionse ndi amene akupuma mpweya wabwino padzikoli.

Kuwonongeka kwa mpweya kukhoza kuyambitsa matenda monga chifuwa, khansa ya m’mapapo komanso matenda a mtima. Kuwonongeka kwa mpweya kumachititsa kuti anthu pafupifupi 7 miliyoni azimwalira asanakule chaka chilichonse.

Dzikoli Linapangidwa M’njira Yoti Lizitha Kudzikonza Lokha

Dzikoli linapangidwa m’njira yoti lizitha kupereka mpweya wabwino kwa chamoyo chilichonse. Koma zimenezi zimatheka ngati anthu akuyesetsa kuti asawononge chilengedwechi. Taganizirani zitsanzo zotsatirazi:

  • Timadziwa bwino kuti mitengo ya m’nkhalango imakwanitsa kuchotsa mpweya woipa wa kaboni dayokisaidi. Koma anthu ambiri sadziwa kuti mitengo yopezeka m’mbali mwa nyanja, ikhoza kuchotsa bwino kwambiri mpweyawu. Mitengoyi imachotsa mpweya wa kaboni dayokisaidi wochuluka kuwirikiza maulendo 5 kuposa umene mitengo yonse ya m’nkhalango zikuluzikulu imachotsa.

  • Kafukufuku wina wa posachedwapa, anasonyeza kuti ndere zina zikuluzikulu zam’madzi zimachotsa mpweya woipa wa kaboni dayokisaidi mumlengalenga. Nderezi zomwe zimakhala ngati masamba, zili ndi timatumba ting’onoting’ono tomwe timadzaza ndi mpweya ndipo timathandiza kuti masambawa aziyandama kuchoka m’mbali mwa nyanja ndipo amakafika kutali kwambiri chapakati pa nyanja. Akafika kumeneko, timatumba tija timaphulika ndipo masamba omwe ali ndi mpweya wa kaboni dayokisaidi amayamba kumira n’kufika pansi pa nyanja. Zimaoneka kuti masambawo amakwiririka pansi pa nyanjapo kwa zaka mahandiredi ambirimbiri.

  • Mumlengalenga mumatha kudziyeretsa mokha ngati muli mpweya woipa. Zimenezi zinaonekera bwino pamene panaikidwa lamulo loti anthu asamayendeyende pa nthawi ya mliri wa COVID-19. Mu 2020, pamene mafakitale ndi magalimoto zinasiya kutulutsa mpweya woipa, mpweya mumlengalenga unayamba kukhala wabwino kwambiri. Malinga ndi lipoti lina lomwe linatuluka mu 2020, mayiko oposa 80 peresenti mwa mayiko amene anaika lamulo loti anthu asamayendeyende, anafotokoza kuti anayamba kukhala ndi mpweya wabwino pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene anakhazikitsa lamuloli.—2020 World Air Quality Report.

    KODI MUKUDZIWA?

    Mpweya Wabwino Ukhoza Kubwereranso

    Tchati chosonyeza mmene mpweya wabwino unalili ku New Delhi, ku India. Mu January 2020 mpweyawu unali pa 120.1, ndipo unali woopsa kwa wina aliyense, koma pofika mu August 2020 unali utatsika ndipo unali wochepera pa 35.5 womwe ndi wabwinoko.

    Pamene analetsa anthu kuti asamachoke panyumba pa nthawi ya mliri wa COVID-19, mpweya woipa wochokera mumafakitale komanso magalimoto unachepa kwambiri mumzinda wa New Delhi ku India. Tinthu ting’onoting’ono topezeka mu mpweya totchedwa particulate matter (PM2.5) tinachepa. Tinthu ting’onoting’onoti tikhoza kuyambitsa matenda monga chifuwa ndi matenda ena oopsa kwambiri. Kusinthaku kunali kwa nthawi yochepa chabe komabe zinangosonyeza kuti mpweya umene wawonongeka mumlengalenga ukhoza kubwereranso mwakale.

    Chakumapeto kwa chaka cha 2019, ku New Delhi ku India kukuoneka mbuu chifukwa cha mpweya woipa.

    © Amit kg/​Shutterstock

    Chakumapeto kwa 2019

    Ku New Delhi ku India pamene analetsa anthu kuti asamachoke panyumba pa nthawi ya mliri wa COVID-19 kukuoneka kowala bwino chifukwa mpweya wasiya kuwonongedwa.

    © Volobotti/​Shutterstock

    Pamene anthu sankayenda pa nthawi ya COVID-19

Zimene Anthu Akuchita Kuti Athetsa Vutoli

Bambo akuimika njinga yake yomwe anakwera popita kuntchito.

Kuyenda panjinga yakapalasa kungathandize kuchepetsa kuwononga mpweya

Maboma akupitiriza kulimbikitsa mafakitale kuti achepetse kuwononga mpweya. Komanso asayansi akupitirizabe kupeza njira zatsopano zothandiza kukonza zinthu zimene anthu aipitsa. Mwachitsanzo, pali njira inayake imene amagwiritsa ntchito mabakiteriya pochotsa zinthu zina zomwe zimakhala m’mankhwala oopsa. Komanso akatswiri ena akulimbikitsa anthu kuti aziyenda wapansi kapena kukwera njinga yakapalasa m’malo moyenda pagalimoto. Akulimbikitsanso anthu kuti asamagwiritse ntchito kwambiri magetsi komanso kuti azigwiritsa ntchito zophikira zamakono.

Mzimayi akuphika atakhala pansi m’nyumba mwake. Akuphikira pa mbaula yomwe situlutsa utsi wambiri.

Maboma ena akupereka zophikira zamakono kwa anthu am’dziko lawo kuti achepetse kuwononga mpweya komabe anthu ambiri alibe mwayi wopeza zophikirazi

Koma zimenezi si zokwanira, ndipo zinaonekera bwino mu lipoti lina limene linalembedwa ndi mabungwe akuluakulu padziko lonse, kuphatikizapo Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse ndi World Bank.

Lipotili linanena kuti mu 2020, anthu pafupifupi 2.4 biliyoni padziko lonse ankagwiritsa ntchito njira zowononga mpweya pophika. M’madera ambiri, ndi anthu ochepa okha omwe angakwanitse kupeza zophikira zamakono kapena kumagwiritsa ntchito njira zina zophikira zosawononga chilengedwe.

Kodi Baibulo Limatipatsa Chiyembekezo Chotani?

“Mulungu woona Yehova, amene analenga kumwamba ndiponso . . . amene anapanga dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo, amene amapereka mpweya kwa anthu amene ali mmenemo.”—Yesaya 42:5.

Mulungu anapanga mpweya umene timapumawu komanso anakhazikitsa njira zachilengedwe zimene zimayeretsa mpweyawu ngati waipitsidwa ndipo zimenezi zimasonyeza kuti iye ali ndi mphamvu zopanda malire komanso amakonda kwambiri anthu. Ndiye kodi zingakhale zomveka kunena kuti iye sangakwanitse kukonza mpweya umene anthu awononga? Onani nkhani yakuti “Mulungu Akulonjeza Kuti Dzikoli Lidzakhalanso Bwino.”

DZIWANI ZAMBIRI

Mmene dziko lapansi limaonekera kuchokera kumwamba.

Kodi mumlengalenga munakhalapo bwanji? Onerani vidiyo yakuti Kodi Zinthu za Kumwamba ndi Padziko Lapansi Zinachita Kulengedwa? pa jw.org.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena