ZIMENE MUNGACHITE PA VUTO LA KUKWERA MITENGO KWA ZINTHU
Muzikhutira Ndi Zomwe Muli Nazo
Anthu amene amakhala okhutira amasangalala ndi zinthu zomwe ali nazo. Ndipo zinthu zikasintha, nawonso amasintha n’kuyamba kukhala moyo wogwirizana ndi mmene zinthu zilili.
N’CHIFUKWA CHIYANI KUCHITA ZIMENEZI N’KOFUNIKA?
Katswiri wina wamaganizo dzina lake Jessica Koehler ananena kuti anthu amene amakhala okhutira amakhala osangalala. Anapezanso kuti anthu oterewa, sachitira nsanje kwenikweni anzawo. Choncho n’zosadabwitsa kuti anthu amene amakhala okhutira sada nkhawa kwambiri. Ndipo ena mwa anthu amene amasangalala kwambiri ndi omwe alibe zinthu zambiri. Zili chonchonso makamaka kwa anthu amene amaona kuti kucheza ndi anthu am’banja lawo komanso anzawo n’kofunika kwambiri.
ZIMENE MUNGACHITE
Muzipewa kudziyerekezera ndi ena. Mukamadziyerekezera ndi munthu wina amene akuoneka ngati akukhala moyo wawofuwofu, mukhoza kukhala wosakhutira komanso wansanje. N’kuthekanso kuti zimene mukuganizazo si zoona chifukwa munthu winayo akhoza kukhala kuti ali ndi ngongole yaikulu. Mayi wina wa ku Senegal dzina lake Nicole, ananena kuti: “Sikuti ndimafunika zinthu zambiri kuti ndikhale wosangalala. Ndikakhala wokhutira ndikhoza kumasangalala ngakhale kuti anthu ena ali ndi zambiri kuposa ineyo.”
Tayesani izi: Muzipewa otsatsa malonda komanso zinthu zomwe anthu amaika pamalo ochezera zomwe zimangosonyeza katundu komanso ndalama zimene anthu ena ali nazo.
Muziyamikira. Anthu amene amakhala ndi mtima woyamikira amakhala okhutira ndipo sakhala ndi maganizo oti akufunika kuchitiridwa zambiri. Roberton wa ku Haiti ananena kuti: “Ndimaganizira zinthu zabwino zimene ena andichitira ineyo komanso anthu am’banja langa ndipo kenako ndimawayamikira. Ndimaphunzitsanso mwana wanga wazaka 8 kuti akapatsidwa chilichonse, azithokoza.”
Tayesani izi: Tsiku lililonse muzilemba chinthu chimene mukufuna kuyamikira. Chikhoza kukhala moyo wathanzi, banja logwirizana, anzanu abwino kapenanso kulowa kwa dzuwa kokongola.
Tonsefe nthawi zina timavutika kukhala okhutira ndi zomwe tili nazo. Koma kuchita zimenezi n’kothandiza. Tikasankha kukhala okhutira, timakhala osangalala, ndipo kusangalalako sitingakugule ndi ndalama.