Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • sg phunziro 12 tsamba 58-63
  • Kulankhula Kochokera m’Maganizo ndi Kulankhula Mwadzidzidzi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulankhula Kochokera m’Maganizo ndi Kulankhula Mwadzidzidzi
  • Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Nkhani Yofanana
  • Kulankhula Kuchokera mu Mtima
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kugwiritsa Ntchito Autilaini
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Phindu la Kukonzekera
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kuyendera Limodzi ndi Omvetsera ndi Ntchito ya Notsi
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
Onani Zambiri
Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
sg phunziro 12 tsamba 58-63

Phunziro 12

Kulankhula Kochokera m’Maganizo ndi Kulankhula Mwadzidzidzi

1, 2. Kodi Yehova amatithandiza motani kukhala okhoza kulankhula?

1 “Musamadera nkhaŵa mudzalankhule bwanji kapena mudzanene chiyani; pakuti chimene mudzachilankhula, chidzapatsidwa kwa inu nthaŵi yomweyo; pakuti wolankhula si ndinu, koma Mzimu wa Atate wanu akulankhula mwa inu.” (Mat. 10:19, 20) Mawu amenewo ayenera kuti analimbikitsa kwambiri ophunzira a Yesu oyambirira aja. Ndipo mawuwo amalimbikitsabe atumiki a Mulungu ofalitsa uthenga wabwino lerolino pamene aitanidwa kukapereka umboni pamaso pa akuluakulu a boma. Izi sizitanthauza kuti Mboni zachikristu za Yehova lerolino zimapatsidwa “mawu a nzeru” ndi “mawu a chidziŵitso” mwa njira inayake ya chozizwitsa ayi. Sizichitikanso kwa iwo muja zinkakhalira kwa Mboni zachikristu za m’zaka za zana loyamba. (1 Akor. 12:8) Komabe, tikusangalala pokhala ndi mwayi wa maphunziro abwino kwambiri ateokalase ndipo, monga mwa lonjezo, mzimu wa Mulungu umatikumbutsa mayankho pamene akhala ofunikira.

2 Chifukwa cha zimene mumaphunzira pamaphunziro a Baibulo, pa Sukulu ya Utumiki Wateokalase ndi pamisonkhano ina ya mpingo, mumakundika zambiri m’nkhokwe yanu ya chidziŵitso cha Baibulo. Mumaphunzira ziphunzitso zoyambirira za chilungamo ndi mmene mungazigwiritse ntchito m’mikhalidwe yosiyanasiyana pamoyo wanu. Ndiyeno mwa kugwira ntchito mu utumiki wakumunda mumazoloŵera kulankhula kwa ena, mukumawaphunzitsa zimene inuyo mwaziphunzira. Kulankhula kumeneku mumakuchita kuchokera m’maganizo kapena mwadzidzidzi.

3. Fotokozani kusiyana pakati pa kulankhula kochokera m’maganizo ndi kulankhula mwadzidzidzi.

3 Ngakhale kuti njira zolankhulira ziŵirizo n’zofananako, kwenikweni izo n’zosiyana. Nali fanizo losonyeza bwino kusiyana kwake. Tinene kuti mwapeza mwininyumba ndipo muyamba kupereka ulaliki wanu umene mwakonzekera, umene mfundo zake zazikulu mwaziloŵetsa m’maganizo mwanu. Kupatulapo mfundo zazikulu zokhazo zimene muli nazo m’maganizo, simunaloŵeze pamtima mawu enieni oti mulankhulire nkhani yanuyo. Mukatero, mukulankhula kuchokera m’maganizo. Ndiyeno mwininyumbayo akufunsani funso limene simunalikonzekere. Komabe, chifukwa cha zimene mumaphunzira ku Nyumba ya Ufumu muli wokhoza kupereka yankho kapena mutha kufotokoza, potapa m’nkhokwe ya chidziŵitso chanu cha Baibulo. Kulankhula koteroko n’kumene timati kwamwadzidzidzi, koganizidwa ndi kulankhulidwa nthaŵi yomweyo.

4. Kodi n’kukonzekera kotani kumene kumafunika kuti nkhani yolankhula kuchokera m’maganizo ikhale yogwira mtima?

4 Kulankhula kuchokera m’maganizo. Chinsinsi cholankhulira nkhani yogwira mtima kuchokera m’maganizo ndicho kukonzekera, kaya ndi ulaliki wa kunyumba ndi nyumba kapena nkhani ya papulatifomu. Ngati mukalankhula nkhani yochokera m’maganizo, konzani autilaini yabwino yokhala ndi mfundo zazikulu zoŵerengeka chabe zoti mukazifutukule. Pansi pa mfundo zazikulu mungandandalike malingaliro ochirikiza, maumboni, malemba ndi mafanizo, kotero kuti mukhale wokonzeka kulankhula nkhani yophunzitsadi. Dziŵani pasadakhale mfundo zake zonse kupatulapo mawu enieni oti mukafotokozere nawo mfundozo.

5-7. Tchulani maubwino a kulankhula kochokera m’maganizo.

5 Kulankhula kochokera m’maganizo kuli ndi maubwino ake angapo. Umodzi ndi woti kumalola kusinthasintha. Mfundo zake sizikhala zoti n’kosatheka kuzisintha, muja zimakhalira ndi nkhani yoŵerenga kapena nkhani yoloŵeza pamtima. Ngati zinthu zina zichitika pamene nthaŵi yayandikira yoti mukambe nkhani yanu, mukhoza kusintha mfundo zina kuti muphatikizepo zatsopanozo. Tayerekezani kuti pamene mukuti munyamuke kumapita kupulatifomu, muzindikira kuti m’kati mwa omvetserawo mulinso okondwerera atsopano ambiri. Kulankhula kochokera m’maganizo kudzakulolani kusintha mfundo zina kuti muthandize atsopanowo kumvetsa bwino nkhani yanuyo. Kapena mwina mukuona kuti pakati pa omvetserawo pali anyamata ndi atsikana ambiri opita kusukulu. Mungasinthe mafanizo anu ndi kutanthauzira kwake kuti muwathandize kuona mmene nkhaniyo ikukhudzira miyoyo yawonso.

6 Ubwino wachiŵiri wolankhula kuchokera m’maganizo ndi wakuti kumasonkhezera maganizo anu. Kumakupatsani mpata woti muganizire malingaliro atsopano. Kaŵirikaŵiri, pamene mukhala ndi omvetsera oyamikira ndi olabadira, mumalimbikitsidwa ndipo m’maganizo mwanu mumafika malingaliro atsopano, amene mosavuta mukhoza kuwaphatikiza m’nkhani yanuyo imene mukuilankhula kuchokera m’maganizo.

7 Ubwino wachitatu wa kalankhulidwe kameneka ndi woti mumakhala ndi mpata woyang’ana omvetsera anu. Zimenezi zimatheketsa kutsatirana kwabwino pakati pa inu ndi iwo. Chotsatirapo chake n’choti adzakhala otchera khutu kwambiri ku zimene mukunena. Ndipo omvetserawo adzaona kuti nkhani yanuyo mukuimvetsa bwino kwenikweni, chifukwa maso anu samangokhala papepala nthaŵi zonse limene mwalembapo mfundo zanu. Komanso mutha kuona kuti omvetsera anu akulabadira motani. Ngati muona kuti chidwi chawo chikuzilala, mukhoza kuchitapo kanthu kena kuti muthetse vuto limenelo. Choncho nkhani yolankhula mwa mtundu umenewo imakhala yolimbikitsa, ya mzimu wokambirana, ndi yofika pamtima.

8-10. Kodi mbuna za kulankhula kochokera m’maganizo tingazipeŵe motani?

8 Ngakhale ndi choncho, kulankhula nkhani kochokera m’maganizo kuli ndi mbuna zake; koma tikhoza kuzipeŵa. Mwachitsanzo, wolankhula nkhaniyo angaphatikizemo malingaliro ochuluka kwambiri moti nkhani yake n’kudya nthaŵi. Ndiponso pokhala ndi ufulu woloŵetsamo malingaliro amene afika m’maganizo, mlankhuliyo angatayire nthaŵi yochuluka pamfundo zina kuposa zimene wakonzekera. Mungapeŵe zimenezi mwa kulemba nthaŵi pa autilaini yanuyo imene mungawonongere pagawo lililonse la nkhani yanu. Ndiyeno mamatirani ku nthaŵi zimenezo.

9 Palinso ngozi yolumpha mfundo zina, kunena mawu osamalizidwa kapena osalondola, kapena kunena zinthu zopanda umboni weniweni. Ngati muyang’ana pamanoti anu nthaŵi ndi nthaŵi popanda kufulumira, mutha kufotokoza mfundo zanu zonse bwinobwino popanda kulumpha zina kapena kutchula zinthu zosalondola. Mwakupanga autilaini yabwino, yokhala ndi mfundo zazikulu zoŵerengeka zoti muzifutukule mwa kugwiritsa ntchito maumboni ndi malemba ozichirikiza, mungapeŵe kunena zinthu zosatsimikizirika.

10 Ngakhale kuti n’kosafunikira kuloŵeza pamtima mawu enieniwo a nkhani yoti muilankhule kuchokera m’maganizo, mukhoza kuchita pulakatisi mawu ena oyenera, ndipo kumakhala kothandiza kusunga tsatanetsatane wa malingaliro m’maganizo. Mwa njira imeneyi mungapeŵe malankhulidwe opanda ulemu: ndi mawu osasankhidwa bwino. Ndipo ngati m’kalankhulidwe kanu ka tsiku ndi tsiku mumayesetsa kukhala ndi malankhulidwe oyenera, kudzakhala kosavuta popereka nkhani. Zoona, ngakhale pamenepo, mwina simungatchulebe bwino kwenikweni mawu muja zimakhalira ndi nkhani yoŵerenga. Koma mukhoza kuwongolera zimenezo ndi njira ya kalankhulidwe kanu. Ndiponso tsimikizani kuti mwabwereramo m’nkhani yanu kangapo musanakailankhule. Kwa ena kumakhala kokwanira kuchita zimenezo mwakachetechete, m’maganizo basi. Koma ambiri amakuona kukhala kothandiza kwambiri kuchita pulakatisi yolankhula nkhaniyo mofuula, makamaka pofuna kusunganso nthaŵi.

11, 12. N’chifukwa chiyani chili chitetezo ngati wolankhula nkhani akhala ndi autilaini?

11 M’kupita kwa nthaŵi, limodzinso ndi pulakatisi, mutha kufupikitsa autilaini yanu kuti ikhale ndi mawu oŵerengeka chabe pamfundo iliyonse ya nkhani yanu. Mutha kulemba zimenezo limodzi ndi malemba oti muwagwiritse ntchito pakadi kapena pepala yokuthandizani kukumbukira. Ngakhale kuti pankhani zina zazifupi, monga nkhani ya wophunzira m’sukulu yateokalase, ena angakonde kungoiloŵeza nkhaniyo, ndi bwino kukhalabe ndi autilaini yachidule imene ingamakukumbutseni ngati pakhala chododometsa china chimene chingakuiŵalitseni tsatanetsatane wa malingaliro anu. Koma nkhani zazitali, monga nkhani yapoyera, n’kwanzeru nthaŵi zonse kukhala ndi autilaini yokutsogolerani ndi kukukumbutsani polankhula.

12 Nkhani zolankhula kuchokera m’maganizo n’zothandiza kwambiri mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba. Chifukwa pamene mwininyumba adzutsa mfundo ina yotsutsa kapena adodometsa mwa njira ina, zimatheka kupatuka pang’ono pamfundo zimene mukukambiranazo, ndi kuti muyankhe nkhaniyo, kenako n’kupitiriza ndi nkhani imene mwakonzekera. Koma ngati muloŵeza pamtima mawu enieni a ulalikiwo, kudzakhala kovuta kuti mupatuke ndi kuyankha mfundo yotsutsayo, kenako mubwerere kuti mupitirize ndi nkhaniyo.

13-15. Kodi ndi liti pamene timalankhula nkhani mwadzidzidzi ndipo imafuna kukonzekera kotani?

13 Kulankhula mwadzidzidzi. Mawu akuti “dzidzidzi” akutanthauza “kusakonzekera, kusaganizapo pasadakhale, kuchita chinthu nthaŵi yomweyo.” Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti sipamakhala kukonzekera kwina kulikonse pankhani kapena mfundo yoti ikambidwe? Ayi, pakuti kuphunzitsa kogwira mtima kulikonse kumafuna kukonzekera. Komabe, nthaŵi zina simungadziŵe kuti mudzafunikira kulankhula nkhani, choncho simukhala wokonzekera kulankhula nkhaniyo. Zimenezo zingakhale pamene mwininyumba amene mupeza mu ulaliki wa kunyumba ndi nyumba adzutsa funso. Kapena zingakhale pamaulendo obwereza, pamaphunziro a Baibulo apanyumba, pochita umboni wa mwamwayi, kapena mutaitanidwa kukaonekera pamaso pa bwalo la milandu kapena pa bungwe la akuluakulu. M’zochitika zoterozo, kasanjidwe ndi kaumbidwe ka nkhaniyo kamakhala kamwadzidzidzi, koma chidziŵitso chanu chochokera m’maphunziro ateokalase chidzapereka maziko a zoti munene. Choncho imene tingati ndi nkhani ya mwadzidzidzi imadaliranso kukonzekera pasadakhale, ngakhale kuti kukonzekerako sikunali kwa chochitikacho.—Yes. 50:4.

14 Ngati mwauzidwa kuti mudzapemphedwa kuti mulankhule, ngakhale patangotsala mphindi zochepa kwambiri, alipo masitepe ofunikira amene mungatenge kuti mukonzekere. Choyamba, sankhani mfundo imodzi kapena ziŵiri zoti mulankhule. Sankhani zifukwa zochirikiza, kuphatikizapo malemba angapo oyenerera. Ndiyeno ganizirani mawu oyamba achidule. Tsopano, ngati kuli kofunika, muli wokonzeka kuyamba kulankhula. Zimenezo zingakhale zofunika, mwachitsanzo pamene wolankhula nkhani ya wophunzira akufunika msangamsanga kuti atenge malo a wina m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase.

15 Pali zitsanzo m’Malemba za atumiki a Yehova amene anaitanidwa mwadzidzidzi kuti achitire umboni choonadi. Mmodzi wa oterowo anali Stefano, amene anatengedwa momuumiriza kupita naye ku khothi lalikulu la Ayuda kumene anakamuimba mlandu ndi mboni zonama. Zimene analankhula mwadzidzidzi tingaziŵerenge m’chaputala 7 cha buku la Machitidwe. Mtumwi Paulo anagwidwa ndi Aatene, namka naye kwa Areopagi kukafunsidwa za chikhulupiriro chake. Kulankhula kwake kwamwadzidzidzi komabe kogwira mtima timakupeza m’Machitidwe chaputala 17.

16-18. N’chifukwa chiyani ophunzira ayenera kuchita pulakatisi kalankhulidwe ka nkhani kochokera m’maganizo, m’malo molemba nkhani yonse kapena kuloŵeza pamtima nkhani zawo?

16 Njira yabwino koposa. Nthaŵi zina atsopano amafuna kuchita kulemba nkhani yawo yonse ya wophunzira. Imeneyo si ndiyo njira yabwino kwenikweni, ndipo iwo ayenera kuyesetsa kusiya njirayo mwamsanga. Chifukwa chake n’chakuti njira imeneyo imaletsa munthu kuyang’ana omvetsera ndipo samalankhula mwachibadwa. Inde, nthaŵi zina timalankhula nkhani zolembedwa, koma chitani pulakatisi zimenezo pamene mwapatsidwa nkhani yoŵerenga. Nkhani zinazo zilankhuleni momasuka kuchokera panotsi.

17 Ophunzira ena amayesa kuloŵeza pamtima nkhani, popanda notsi zilizonse. Koma nkhani zoloŵeza pamtima zili ndi zoipa zake zotsimikizika, simutha kusintha, siyimveka mwachibadwa ndipo m’posavuta kuiŵala mbali ina yofunika kwambiri. Kuloŵeza kungakhale koyenera pamasentensi angapo ofunika kwambiri, monga m’mawu oyamba kapena mawu omalizira, koma si bwino kuyesa kuloŵeza nkhani yonse.

18 Nthaŵi zonse njira yabwino koposa ndiyo yolankhula kuchokera m’maganizo. Ndiyo njira imene timagwiritsa ntchito mu utumiki wakumunda, mmene timaphunziradi kuganiza tilikuyenda. Ngakhalenso pamisonkhano yampingo, mudzaona kuti kulankhula kochokera m’maganizo ndiyo njira imene timagwiritsa ntchito kaŵirikaŵiri. Chifukwa chake n’chakuti imalola munthu kupereka uthenga woona, wolunjika komanso wobala zipatso zabwino pambuyo pake. Choncho chitani pulakatisi njira imeneyo mosalekeza. Ndipo ngakhale kuti nthaŵi zina tingapemphedwe kulankhula nkhani yamwadzidzidzi, tidzakhala wokonzeka kutero, chifukwa Yehova ndiye amatikonzekeretsa ponse paŵiri kulankhula nkhani kochokera m’maganizo ndi mwadzidzidzi. Njira zonse ziŵirizo zili ndi malo ake mu utumiki wathu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena