Nyimbo 159
Kukhala Kwathu ndi Mtendere
1. Kwa oipa kulibe
Mtendere konse;
Ngakhaletu kukhamu
La Satanalo.
Mtendere uchokera
Kwa Yehovayo,
Umabwera kwa onse
Okonda M’lungu.
2. Tamandani Yehova
Wamtendereyo.
Athetsa nkhondo zonse,
’Gwirizanitsa.
Kalonga Wamtendere,
Kristu Mwanake.
Atalakika iye,
Mtendere udza.
3. Zonyansa zotuluka
Mkamwa tasiya.
Lupanga ndi mikondo
Ndi zolimira.
Tisungetu mtendere,
Tikhulukire.
Mwachikonditu monga
“Nkhosa” za Yesu.
4. Mtendere ndi chipatso
Chachilungamo,
Umboni wanzeruyo
Yodza kumwamba.
Yomwe tipempherera
Mtendere wathu,
Kuŵala kubweretsa
Chimwemwe chonse.