‘Ukhalebe mu Zimene Waziphunzira’
Izi n’zimene mtumwi Paulo analembera mnyamatayo Timoteo. (2 Timoteo 3:14) Popeza kuti mwawerenga bukuli, mwadziwa zinthu zabwino zambiri zimene Mulungu wasungira anthu amene amam’konda. Koma mufunikabe kupita patsogolo mwauzimu. Mboni za Yehova n’zokonzeka kukuthandizani ngati palibe wina amene akukuthandizani. Tangolemberani Mboni za Yehova kugwiritsa ntchito imodzi ya maadiresi ali pansipa, ngati mukufuna kudziwa zambiri kapena ngati mukufuna kuti wa Mboni za Yehova azibwera kunyumba kwanu kudzaphunzira nanu Baibulo nthawi zonse kwaulere.