Mabuku Ogawira
KONZEKERANI TSOPANO KUKHALA M’DZIKO LAPANSI LATSOPANO LA MULUNGU
Gulani ndi kuŵerenga—
MUNGATHE KUKHALA NDI MOYO KOSATHA M’PARADAISO PA DZIKO LAPANSI
Limaphatikizapo mayankho okhutiritsa maganizo Abaibulo a mafunso onga ngati:
● Kodi chimachitika nchiyani pa imfa?
● Kodi nchifukwa ninji Mulungu walola kuipa?
● Kodi ndimotani mmene Baibulo lingakuthandizireni kukhala ndi moyo wabanja wachimwemwe?
Limagogomezera chiyembekezo cha moyo wamuyaya m’Paradaiso wa padziko lapansi.
Lazithunzithunzi zokongola; losavuta kumva; lamasamba 256.
OGWIRIZANA M’KULAMBIRIDWA KWA MULUNGU YEKHA WOWONA
Lolinganizidwa kukulitsa ndi kuzamitsa chidziŵitso chanu cha Mawu a Mulungu.
Limakuthandizani kuphunzira mmene mungagwiritsirire ntchito ziphunzitso Zabaibulo mokwanira kwambiri m’moyo wanu.
Laling’ono; lamasamba 192.
AŴIRIŴA AMACHITA $5,60 ZOKHA.
Tumizani oda yanu ku Watch Tower, mukumagwiritsira ntchito keyala yapafupi koposa ya osonyezedwa patsamba lotsatira. Mitengo njokhoza kusintha.)