“Pitiriza m’Zinthu Zimene Unaphunzira”
Zimenezo ndizo zimene Mtumwi Paulo analembera Timoteo wachichepereyo. (2 Timoteo 3:14, NW) Pambuyo pa kuwerenga bukhu lino, mukudziwa zinthu zabwino zambiri zimene Mulungu wasungira awo amene akumkonda. Koma mufunikira kupitiriza kupita patsogolo m’njira yauzimu. Mboni za Yehova zidzakhala zokondwa kukuthandizani, ngati inu simuli kale kulandira chithandizo chimenecho. Ingolemberani kalata ku Watch Tower ku keyala yoyenerera, monga momwe andandalikidwira pansipa, mukumapempha chidziwitso chowonjezereka kapena kuti mmodzi wa Mboni za Yehova adze kunyumba kwanu ndi kuphunzira nanu Baibulo nthawi zonse popanda malipiro.