Mungapeze buku lina
Nkhani Zabaibulo Zokondweretsa Ana
Kuyambira pakutulutsidwa kwake, Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo lakhala lokondweretsa achichepere ndi achikulire omwe. Achichepere amakondwera kuti nkhani 116 ziŵerengedwe kwa iwo mobwerezabwereza. Bukhuli liri ndi masamba 256, lachikuto chagolidi yachikasu limodzi ndi dzina m’zilembo zofiira, ndi zazikulu kwambiri. Liri ndi zithunzithunzi zazikulu zoposa 125 zimene unyinji wake ziri zamawonekedwe amitundu ingapo. Limachita $4,00 zokha, zopositira zaphatikizidwa. (Chiŵerengerochi chingathe kusintha.) Lemberani ku Watch Tower, mukumagwiritsira ntchito keyala kuchokera ku chikuto chakumbuyo.
Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
Bukhu limeneli limafola chowonadi chamaziko cha Baibulo ndipo limagogomezera chiyembekezo cha moyo wamuyaya m’paradaiso padziko lapansi. Limaphatikizapo mafunso onga akuti: Kodi chimachitika nchiyani pa imfa? Chiukiriro—cha ayani ndipo kuti? Kodi nchifukwa ninji Mulungu walola kuipa? Kodi Baibulo lingakuthandizeni motani kuti mukhale ndi moyo wa banja wachimwemwe? Lomveka mosavuta. Lazithunzithunzi zokongola, lamasamba akuru, 256. Lopezeka pa chopereka cha $4,00 (Zimbabwe). (Chiŵerengerochi chingathe kusintha.) Lemberani ku Watch Tower, mukumagwiritsira ntchito keyala kuchokera pa tsamba lomalizira.