Mutu 58
Mitanda ya Mikate ndi Chotupitsa
MAKAMU aakulu afika muunyinji wawo kwa Yesu m’Dekapoli. Ambiri ayenda mtunda wautali kudza kuchigawo chino chokhalidwa kwakukulukulu ndi Akunja kudzamumva ndi kudzachiritsidwa nthenda zawo. Iwo adza ndi mitanga yaikulu, kapena zotengera, zimene mwamwambo amagwiritsira ntchito kunyamulira kamba paulendo wodutsa zigawo za Akunja.
Komabe, potsirizira pake, Yesu akuitana ophunzira ake nati: “Ndimva nalo chifundo khamulo, chifukwa ali ndi ine chikhalire masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya: ndipo ngati ndiwauza amuke kwawo osadya kanthu, adzakomoka panjira; ndipo, ena a iwo achokera kutali.”
“Munthu adzatha kutenga kuti mikate yakukhutitsa anthu awa m’chipululu muno?” ophunzirawo akufunsa motero.
Yesu akufunsa kuti: “Muli nayo mikate ingati?”
“Isanu ndi iŵiri,” iwo akuyankha motero, “ndi tinsomba pang’ono.”
Polamulira anthuwo kuti akhale pansi, Yesu akutenga mikate ndi tinsomba, napemphera kwa Mulungu, nanyema, ndipo akuyamba kuzipereka kwa ophunzira ake. Iwo, nawonso, akupereka kwa anthu, ame- ne akudya nakhuta. Pambuyo pake, pamene makombo asonkhanitsidwa, pali mikate yodzala mitanga isanu ndi iŵiri, ngakhale kuti pafupifupi amuna 4,000, kuphatikizapo akazi ndi ana, adya!
Yesu akuuza makamuwo kumuka, nakwera iye ngalaŵa limodzi ndi ophunzira ake, nawolokera kugombe lakumadzulo kwa Nyanja ya Galileya. Kunoko Afarisi, panthaŵi ino otsagana ndi ziŵalo za kagulu ka chipembedzo ka Asaduki, akuyesa kupereka chiyeso kwa Yesu mwa kumfunsa kuti awawonetse chizindikiro cha kumwamba.
Atazindikira zoyesayesa zawo za kumuyesa, Yesu akuyankha kuti: “Madzulo munena, kudzakhala ngwe; popeza thambo liri lacheza. Ndipo mmaŵa, Lero nkwamphepo, popeza thambo liri lacheza chodera. Mudziŵa kuzindikira za pankhope ya thambo; koma zizindikiro za nyengo ino simungathe kuzindikira.”
Atatero, Yesu akuwatcha iwo mbadwo woipa ndi wachigololo ndipo akuwachenjeza iwo monga momwe anauzira Afarisi poyambapo kuti, palibe chizindikiro chimene chidzaperekedwa kwa iwo kusiyapo cha Yona. Pochoka, iye ndi ophunzira ake akuloŵa m’ngalaŵa napita cha ku Betsaida kugombe lakumpoto cha kummaŵa kwa Nyanja ya Galileya. Ali panjira ophunzirawo akutulukira kuti aiŵala kutenga mikate, popeza kuti ali ndi mtanda umodzi wokha wa mkate pakati pawo.
Pokumbukira chokumana nacho chake chaposachedwapa ndi Afarisi ndi Asaduki ochirikiza a Herode, Yesu akulangiza kuti: “Yang’anirani, penyani kuti mupeŵe chotupitsa mkate cha Afarisi, ndi chotupitsa mkate cha Herode.” Mwachiwonekere kutchulidwa kwa chotupitsa kukupangitsa ophunzirawo kuganiza kuti Yesu akunena za kuiŵala kwawo kudza ndi mikate, chotero iwo akuyamba kukangana za nkhaniyo. Powona kusamvetsetsa kwawo, Yesu akuti: “Bwanji mutsutsana chifukwa mulibe mkate?”
Osati kale kwambiri, Yesu anali atagaŵira mwanjira yozizwitsa mkate kwa anthu zikwi zingapo, akumachita chozizwitsa chomalizira chimenechi mwinamwake tsiku limodzi kapena aŵiri apitawo. Iwo ayenera kudziŵa kuti iye sali kudera nkhaŵa ndi kusoŵeka kwa mitanda ya mkate yeniyeni. “Simukumbukira kodi,” iye akuwakumbutsa, “pamene ndinagaŵira anthu zikwi zisanu mikate isanu ija, munatola mitanga ingati yodzala ndi makombo?”
“Khumi ndi iŵiri,” iwo akuyankha motero.
“Ndipo mikate isanu ndi iŵiri kwa anthu zikwi zinayi, munatola malichero angati odzala ndi makombo?”
“Asanu ndi aŵiri,” iwo akuyankha motero.
“Simudziŵitsa ngakhale tsopano kodi?” Yesu akufunsa motero. “Bwanji nanga simudziŵa kuti sindinanena kwa inu za mikate? Koma peŵani chotupitsa cha Afarisi ndi Asaduki.”
Potsirizira pake ophunzirawo akumvetsetsa. Chotupitsa, msanganizo umene umachititsa mkate kufufuma, linali liwu logwiritsiridwa ntchito kusonyeza kuipitsa. Chotero tsopano ophunzirawo akumvetsetsa kuti Yesu akugwiritsira ntchito phiphiritso, kuti akuwachenjeza kuti akhale ochenjera ndi “chiphunzitso cha Afarisi ndi Asaduki,” chiphunzitso chokhala ndi chiyambukiro choipitsa. Marko 8:1-21; Mateyu 15:32–16:12.
▪ Kodi nchifukwa ninji anthuwo ali ndi mitanga yaikulu ya chakudya?
▪ Atachoka mu Dekapoli, kodi Yesu akupanga maulendo otani a m’ngalaŵa?
▪ Kodi ndikumva kolakwa kotani kumene ophunzirawo ali nako ponena za mawu a Yesu onena za chotupitsa?
▪ Kodi Yesu akutanthauzanji ndi mawu akutiwo “chotupitsa cha Afarisi ndi Asaduki”?