Pulogalamu Yophunzitsa Luso la Kulankhula ndi Kuphunzitsa
KAYA ndinu wachichepere kapena wachikulire, mwamuna kapena mkazi, maphunziro ameneŵa adzakuthandizani kulankhula mogwira mtima ndi kukhala mphunzitsi waluso wa Mawu a Mulungu.
Woyang’anira sukulu ndiye amagaŵira nkhani kwa awo amene analembetsa m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Pamasamba atatu otsatirawa muonapo fomu yanu yolangizira zakalankhulidwe. Manambala a mfundo iliyonse amayenderana ndi maphunziro a pamasamba otsatirawo. M’maphunziro amenewo mudzapeza malongosoledwe osonyeza mmene mungadziŵire luso la kalankhulidwe ndi kaphunzitsidwe, ndi chifukwa chake mbali iliyonse ili yofunika kwambiri. Mupezanso malangizo othandiza mmene mungachitire zimene akulangizazo.
Mitundu (ya kala) imene ili pafomu yolangizira ikusonyeza mfundo zokhudza nkhani za (1) kuŵerengera omvera, (2) kukambirana kwa anthu aŵiri kapena oposerapo, kapena (3) nkhani yokambira mpingo. Woyang’anira sukulu adzakugaŵirani mfundo yoti mudzaikonzekere. Ndi bwino kukonzekera mfundo imodzi panthaŵi imodzi. Mudzapindula mwa kuchita “Zochita” zimene aika kumapeto kwa phunziro limene mwapatsidwalo. Ngati mwaonetsa kuti mwatsatira bwino malangizo operekedwa m’phunzirolo, mlangiziyo adzakugaŵirani mfundo ina.
Ngati nkhani yanu ndi yokambirana, sankhani mtundu wa makambirano. Mitundu ya makambirano yandandalikidwa patsamba 82, koma si mitundu yokhayo imene mungagwiritse ntchito. Mlangiziyo angakuuzeni kuti muyese mtundu wakutiwakuti wa makambirano kuti muphunzire kachitidwe kake, kapena angakupatseni mwayi wakuti musankhe nokha.
Kuŵerenga buku lino ndi kuchita “Zochita,” ngakhale pamene simukukonzekera nkhani ya m’sukulu, kungakuthandizeni kwambiri kupita patsogolo. Mwina mukhoza kumaŵerenga phunziro limodzi pamlungu kapena kuposerapo.
Kaya mwakhala mukukamba nkhani m’sukulu kwa nthaŵi yaitali chotani, kapena kulalikira m’munda zaka zambiri chotani, mukhoza kupitabe patsogolo. Pindulani mokwanira ndi maphunziro a m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.