MUTU 29
Yehova Anasankha Yoswa
Mose anatsogolera mtundu wa Aisiraeli kwa zaka zambiri. Ndiyeno atatsala pang’ono kumwalira, Yehova anamuuza kuti: ‘Iweyo sudzalowetsa Aisiraeli m’Dziko Lolonjezedwa. Koma ndidzangokuonetsa dzikolo.’ Zitatero Mose anapempha Yehova kuti asankhe mtsogoleri wina woti azitsogolera anthuwo. Yehova anamuuza kuti: ‘Pita kwa Yoswa ndipo ukamuuze kuti ndi amene ndamusankha.’
Mose anauza Aisiraeli kuti iye watsala pang’ono kumwalira, ndipo Yehova wasankha Yoswa kuti awatsogolere polowa m’Dziko Lolonjezedwa. Ndiyeno Mose anauza Yoswa kuti: ‘Usachite mantha, Yehova akuthandiza.’ Atatero, Mose anapita pamwamba pa phiri la Nebo. Kumeneko Yehova anamuonetsa dziko limene analonjeza Abulahamu, Isaki ndi Yakobo. Kenako Mose anamwalira ali ndi zaka 120.
Ndiyeno Yehova anauza Yoswa kuti: ‘Muwoloke mtsinje wa Yorodano n’kulowa m’dziko la Kanani. Ndizikuthandiza ngati mmene ndinkachitira ndi Mose. Uziwerenga malamulo anga tsiku lililonse. Khala wolimba mtima ndipo usachite mantha. Pita ukachite zimene ndakuuza.’
Yoswa anatumiza anthu awiri kuti akaone mzinda wa Yeriko. Munkhani yotsatira tidzaona zimene zinachitika anthuwo atafika kumeneko. Atabwerako iwo ananena kuti nthawi yoti Aisiraeliwo alowe m’dziko la Kanani inali itakwana. Tsiku lotsatira, Yoswa anauza Aisiraeli kuti anyamuke. Kenako anauza ansembe omwe ananyamula likasa la pangano kuti atsogole kupita kumtsinje wa Yorodano. Pa nthawiyi n’kuti madzi a mumtsinjewu atasefukira. Koma ansembewo atangoponda m’madzimo, mtsinjewo unayamba kuuma. Iwo anayenda n’kufika mʼmphepete mwa mtsinjewo ndipo anaima pomwepo mpaka Aisiraeli onse anawoloka. Mwina zimene zinachitikazi zinawakumbutsa zomwe Yehova anachita pa Nyanja Yofiira.
Atayenda kwa zaka zambiri, Aisiraeli anafika m’Dziko Lolonjezedwa. Iwo anayamba kumanga nyumba ndi mizinda. Analima minda n’kudzala mphesa komanso zipatso zosiyanasiyana. Linalidi dziko loyenda mkaka ndi uchi.
“Yehova azidzakutsogolerani nthawi zonse ndipo adzakupatsani zinthu zofunika ngakhale mʼdziko louma.”—Yesaya 58:11