Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 10/15 tsamba 3-4
  • Kodi Chipembedzo Chiri Mphamvu ya Makhalidwe Abwino?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chipembedzo Chiri Mphamvu ya Makhalidwe Abwino?
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mbali Yoipa
  • Mipanda Yosweka ya Makhalidwe Abwino
  • Kodi Zipembedzo za Dziko Zikupereka Chitsogozo Choyenera?
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
  • Chipembedzo Chichirikiza Mbali Ina
    Galamukani!—1994
  • Kodi Zipembedzo Zili ndi Phindu Lanji?
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Chifukwa Chake Chipembedzo cha Dziko Chidzatha
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 10/15 tsamba 3-4

Kodi Chipembedzo Chiri Mphamvu ya Makhalidwe Abwino?

M’KUYANKHA funso limeneli, mamiliyoni angavomerezane ndi George Bernard Shaw, yemwe analemba kuti “Chipembedzo chiri mphamvu yaikulu​—chisonkhezero chimodzi chokha chenicheni champhamvu m’dziko lapansi.” Mosiyanako, mkonzi wa Chingelezi wa mu zana la 19 John Ruskin, akumalemba pa maziko akuwona mtima, anasuliza kuti, “Chipembedzo chonyenga nthaŵi zonse chiri choipitsitsa koposa ponena za iye.” Ndi kawonedwe kati kamene mukulingalira kuti kali koyandikira ku chowonadi?

Monga chitsimikiziro cha mphamvu ya makhalidwe abwino a chipembedzo, ena angaloze kwa anthu amene anakhala “munthu wosinthidwa” pamene ‘anapereka moyo wawo kwa Yesu Kristu.’ Mmenemo ndi mmene magazini ya mitundu yonse inalongosolera “kutembenuka” kwa Charles Colson, amene analowetsedwa mu mlandu wa kugwiritsira ntchito udindo molakwa. Winawake angalozenso kwa awo amene amadzinenera kuti chipembedzo chawo chinawapulumutsa iwo ku moyo wa chisembwere kapena uchidakwa. M’maiko osakhala a Chikristu, mamiliyoni a maBaibulo agawiridwa, chimene mosakaikira chathandiza anthu ambiri kuwongolera miyoyo yawo mwamakhalidwe abwino. Mwachiwonekere, chipembedzo chapereka chisonkhezero chabwino chamakhalidwe abwino pa anthu oterowo.

Mbali Yoipa

Ku mbali ina, chipembedzo cha Hitler sichinali choletsa kwambiri kwa iye. Icho chinatsogolera anthu owona mtima kukudabwa kwakuti nchifukwa ninji pempho lopangidwa kwa Papa Pius XII la kumuchotsa Hitler silinayankhidwe. Catholic Telegraph-Register ya Cincinnati, Ohio, pansi pa mutu wakuti “Woleredwa Monga M’katolika Koma Womalakwira Chikhulupiriro Ikutero Lamya Yopita Kwa Papa,” inasimba kuti “Pempho linapangidwa kwa Pius XII kuti Reichsfuehrer Adolph Hitler achotsedwe.” Ngati kachitidwe kameneka kanachitidwa, kodi icho chikanayambukira zotulukapo za nkhondo ndi kuthandiza kupulumutsa kuvutika kwa anthu ambiri? Nchomvetsa chisoni kunena kuti, papa sanayankhe nkomwe.

Kukhala limodzi ndi munthu wa chiwalo chosiyana popanda kukwatirana mwalamulo kuli kofala m’maiko a Chikatolika mu South America. Ndipo mu North America mtsogoleri wa chipembedzo analembera mkonzi kuti: “Chipangeni Chisembwere Kukhala Chalamulo​—Liri Yankho Loyera.” (Philadelphia Daily News) Yang’ananinso pa mikhalidwe ku maiko ena a chiProtesitanti kumene kusinthana akazi, kugonana kwa otomerana, ndi kugonana kopanda ukwati kuli kofala. Timapeza chifukwa kaamba ka izi cholingaliridwa m’mawu ogwidwa a m’nyuzipepalawo: “Apasitala Akhala Chete pa Kugonana kwa Otomerana.” Nkhaniyo inanena kuti “Apasitala a ku America akhala mochimwa ali phe mu kulalikira ponena za kugonana kwa otomerana . . . Iwo akuchita mantha kuti angataye ena a ansembe awo.” (Telegraph, North Platte, Nebraska) Chotero kodi chipembedzo chonse chiri mphamvu kaamba ka makhalidwe abwino?

Mu Dziko la Chipembedzo, kusoweka kwamphamvu ya makhalidwe abwino kumawonekera bwino kwa chipembedzo mkati mwa nthaŵi ya nkhondo. Onani zimene mukulingalira ponena za kudzinenera komveka bwinoku. Mu 1934 Walter W. Van Kirk, amene panthaŵiyo anali mlembi wa dipartimenti ya Federal Council of the Churches of Christ mu America, analemba kuti: “Alaliki ndi anthu wamba atenga chilumbiro cha kuima mu kulimbana ndi nkhondo . . . Nkhondo ya chipembedzo ya mtendere imeneyi ya matchalitchi imachokera pa chitsimikiziro chakuti nkhondo iri kotheratu yosiyana ndi kulalikira ndi kachitidwe ka Yesu.” (Religion Renounces War) Pambuyo pa kugwira mawu matchalitchi ambiri ndi atsogoleri a chipembedzo, bukhulo linamaliza kuti: “Matchalitchi, m’chenicheni, mwachimvekere anena kuti iwo sayenera kulingaliridwanso monga ogwirizana mu bizinesi lakupha ndi kusautsa anthu. Alaliki ali . . . kusamba manja awo a mwazi wa anzawo, iwo akulekana ndi Kaisara.”

Komabe, zoneneratu za kawonedwe kabwino zimenezo momvetsa chisoni sizinakhale zowona. Pamene Nkhondo ya Dziko II inaulika, palibe chipembedzo ndi chimodzi chomwe cha Dziko la Chipembedzo chinatenga kaimidwe kamphamvu ka ‘kutsutsa nkhondo.’ Kodi matchalitchi m’dera lanu adachita tero?

Mipanda Yosweka ya Makhalidwe Abwino

Pokhala titalingalira zizindikiro zina za mbali zonse ziŵiri, kodi inu simungavomereze kuti m’mikhalidwe yambiri, zipembedzo zotchuka za m’dziko sizinakhale magwero amphamvu kwambiri kaamba ka makhalidwe abwino? Magazini ya Look inalengeza kuti: “Matchalitchi . . . alephera kupereka utsogoleri wa makhalidwe abwino, ndipo chifukwa chakuti thayo lawo liri lalikulu koposa, kulephera kwawo kuli koipitsitsa.” The Courier-Mail ya ku Brisbane, Australia, inachitira ndemanga pa kulephera kwa zipembedzo za Dziko la Chipembedzo kupereka chitsenderezo ku mkhalidwe woipa wa kugonana: “Pamene chibwera kwa Mabishopo ndi Makanoni . . . kulemba kuti kugonana kunja kwa ukwati kungakhale m’chitidwe waufulu umene ‘umalengeza ulemerero wa Mulungu,’ . . . kuti chisembwere sichiri cholakwa mwa icho chokha ngakhalenso chigololo sichiri kwenikweni choipa; kenaka mwamuna wamba ndi mkazi, ndipo makamaka mnyamata ndi msungwana wachichepere, amakhala osokonezeka pakati pa chabwino ndi choipa. Chotulukapo cha kusatsa konseku kaamba ka Makhalidwe Abwino Atsopano kwakhala kwakuswa mipanda ya makhalidwe abwino.”

Ayi, m’chenicheni, zipembedzo zadziko siziri mphamvu yeniyeni kaamba ka makhalidwe abwino. Mosiyanako, iwo ayenera kutenga lina la thayo kaamba ka mkhalidwe woipa wa makhalidwe lerolino. Komabe, popeza chipembedzo chikuyembekezedwa kutanthauza “utumiki ndi kulambira kwa Mulungu kapena wapamwamba koposa m’chilengedwe,” kodi icho sichiyenera kukhala mphamvu kaamba ka ubwino m’maiko onse kumene icho chiriko? Nchiyani chimene chikusoweka? Ndimotani mmene chipembedzo chanu chingaperekere mphamvu yoteroyo lerolino?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena