Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 6/15 tsamba 21-23
  • Iwo Anatsimikiziridwa za Chikondi cha Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Iwo Anatsimikiziridwa za Chikondi cha Yehova
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Umboni wa Chikondi cha Yehova
  • Kami​—Pomalizira
  • Gawo 9: 551 B.C.E. kupita mtsogolo—Kufufuza kwa Kum’mawa kaamba ka Njira Yolondola
    Galamukani!—1989
  • Kodi Tikanatani Pakadapanda Abulu?
    Galamukani!—2006
  • Njira Imene Ikuthandiza Kulalikira Anthu Omwe Sapezeka Pakhomo
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016
  • Yehova Amadalitsa Kuwumirira
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 6/15 tsamba 21-23

Iwo Anatsimikiziridwa za Chikondi cha Yehova

MAFUNDE a akulu anali kukuta chombo chogwidwa mu namondwe wamphamvu pa nyanja. Nkhondo ya masiku 14 ndi madzi aukali inasiya okwerawo ndi oyendetsa opanda chiyembekezo, kupatulapo mmodzi. Iye anali ndi chidaliro kuti Yehova adzamuchinjiriza iye, pamene mawu otonthoza, “Usawope, Paulo” analira m’maganizo ake. Mkati mwa maora osankha otsatirawo, chombocho chinaima, kulola onse kupita kumtunda. Kachiŵirinso mtumwi Paulo anali ndi chifukwa cha kukhalira wotsimikiziridwa za chikondi cha Yehova.​—Machitidwe 27:20-44.

Kodi inu mofananamo muli otsimikiziridwa za chikondi cha Mulungu? Phunziro lokhazikika la Mawu a Mulungu ndi kugwiritsira ntchito zimene mwaphunzira kulimbikitsa ena kuli kofunika koposa. Komabe, kuti mukhaledi otsimikiziridwa za chikondi cha Yehova, inu m’chenicheni muyenera kukhalira pa zonena za Yehova mwa kukumana ndi kuchita kwake m’malo mwanu. Mmodzi amene watsimikiziridwa zolimba za ichi ali woyang’anira woyendayenda wogwira ntchito m’mapiri okwezeka a ku Bolivia amene, mofanana ndi ambiri ena, wakumana ndi chisamaliro cha Yehova.

“Akumagwira ntchito kunja kwa Oruro,” iye akulongosola, “Ndinayenera kuchezera mpingo mu Kami, mzinda wa migodi makilomita 100 kutali. Msewu wokhotakhota wa mapiri umafika pa utali wa mamita 4,600 ndipo ungakhale wowopsya, makamaka ngati kwagwa mvula. Kutentha nthaŵi zambiri kumatsika kufika ku −10° C. kapena kutsikirapo.

“Mbale wina, Aníbal, anayenera kunditenga ine pa njinga yake yamoto, ndipo tinanyamuka 6:00 a.m., okonzekera kaamba ka ulendo wathu wa maora asanu. Kuchokera pamene tinanyamuka kunali kugwa mvula, ndipo matope anapitiriza kuwundana pakati pa magudumu ndi fender, kutibweretsa ife ku kuima. Kokha pambuyo pa kuchotsa matopewo mosamalitsa tinakhoza kunyamukanso. Pamene tinali kuyenda pa chishalo kumbuyo kwa Aníbal, ndinayesera kuchinjiriza nsapato zanga ndi talauza, koma ndinalisiya pamene inanyowa kotheratu.

Umboni wa Chikondi cha Yehova

“Maora asanu ndi limodzi anali atapita pamene injini inasiya kugwira ntchito, pa phiri lotsetsereka, ndipo tinayamba kubwerera m’mbuyo. Ndikumadumphapo, tinayesera m’njira iriyonse kugwira makina olemerawo m’matope otererawo. Ngakhale kuli tero, ichi chinatsimikizira kukhala chosaphula kanthu, ndipo mitima yathu inakhumudwa pamene njinga yamotoyo inagwera m’ngalande yakuya yoposa mamita 90! Modera nkhaŵa tinayang’ana pansi. Mosakhulupirira, makinawo anaima asanagunde pansi kwenikweni. Komabe, sitikanatha kudzutsa iyo popanda thandizo.

“Maora anapita, koma tinali ndi chiyembekezo chochepa chakuti winawake adzadutsa m’msewu wachipululu umenewo. Kenaka mwamuna wokhala ndi bulu ndi ma llama anawonekera. Akumawona kuvutika kwathu, iye analankhula m’chinenero cha Quechua: ‘Inde, ndiri nazo zingwe zina.’ Iye anamangilira zingwe za chikopa kumbuyo kwa bulu ndi ku njinga yamotoyo. Kenaka, tinanyamula kuchokera pansipo pamene iye analimbikitsa buluyo kukoka. Pomalizira pake, pambuyo pa kuvutika kwambiri kwa buluyo, tinabwereranso pa msewu, zipumi zathu ziri zowala ndi thukuta. Ndimotani mmene tinakamthokozera iye? Tinampatsa iye bukhu la Nkhani za Baibulo, ndipo iye anakondweretsedwa ndi bukhulo kotero kuti anafuna kubwezera chiyanjocho ndi mbatata kuchokera mu katundu wake!

“Injini inayamba, ndipo tinali oyamikira koposa kwa Yehova. Titayenda pataliko, tinalingalira za kuima, popeza injiniyo inayamba kufooka. Tinafika pa shopu ya kofi ya payokha. ‘Nkuti kumene mukupita?’ mwiniwakeyo anafunsa. Tinamuuza iye ndi kulongosola vuto lathu. ‘Ndiri ndi spark plug ndi ziwiya zina ndidzakubwerekani,’ iye anatero. Sitinathe kukhulupirira makutu athu​—awa anali malo kumene mabwenzi ndipo osayerekeza alendo otheratu, kaŵirikaŵiri sakhulupiriridwa. Ndi spark plug yatsopanoyo injiniyo inayamba kuyenda bwino.

“Tsopano kunada, ndipo ndinayamba kuzindikira, pamene miyendo yanga inayamba kusiya kugwira ntchito m’malo ozizira koposa. Kenaka, pamene tinali kukwera pa malo okwezeka, injiniyo inasiyanso. Ponse paŵiri kupompa choyambitsira ndi kukankha njinga yamotoyo kwa makilomita atatu zinatsimikizira kukhala zosaphula kanthu. Titatopa kotheratu, tinakhala pansi mphepete mwa msewu. Komabe miyendo yanga sinali yosiya kugwira ntchito! Koma tinali okhumudwitsidwa ndipo osowa chochita ponena za chimene tidzachita. Tinapuma pang’ono ndipo kenaka tinayesera kuyambitsanso injiniyo. Kodi iyo ikagwira ntchito?

“Kukudabwitsidwa kwathu injiniyo inayambadi. Ngakhale kuli tero, kunayamba kugwa mvula tsopano, ndipo pa mtunda wotsatira inaimanso. Kachiŵirinso tinakhala pansi mphepete mwa msewu, pa nthaŵi ino mu mvula yambiri. Tinapumanso kachiŵiri. Ndi zikaikiro zina tinayeseranso injiniyo​—ndipo inayambanso! Mwamsanga tinali kudutsa malo apamwamba kwambiri a ulendo wathu. Ndinadzimva kukhala wa mpumulo, ndi kumalingalira kuti ngakhale ngati injiniyo itasiyanso, tingadutse kupita ku Kami. Koma pa malo otsetsereka chogwirira cha mabureki chinathyokera m’manja mwa Aníbal! Mwamsanga ndi kumadumphapo pamene ndinagwiririra ku kaliyala ya kumbuyo, ndinaika mapazi anga onse aŵiri pansi ndi kutsetserekera pansi pa phiri. M’njira imeneyi ndinakhoza kubweretsa tonsefe ku kuima. Ichi chinachitika pa malo ena owonjezereka aŵiri otsetsereka.

Kami​—Pomalizira

“Inali 3:00 a.m. pamene pomalizira tinafika ku Kami. Tinali pa msewu kwa maora 21. Kupeza abale kukakhala vuto, popeza umenewu unali ulendo wanga woyamba. Tinagogoda pa zitseko koma tinawuzidwa: ‘Chokani! Tikugona!’ Pambuyo pa kugogoda pa zitseko zoŵerengeka, ndinamva kuti chinthu chabwino koposa kuchita chikakhala kugona pansi pa denga lolenjekeka ndi kufufuza kaamba ka abalewo m’mawa. Ndikumadziponya pansi, ndinagona tulo tofa nato. Pamene ndinadzuka ndinadzipeza nditazungulidwa ndi anthu. Ndinaimirira, ndipo mwamuna wamphamvu anabwera ndi kundikupatira ine mwamphamvu. Inde, iwo anali abale athu! Aníbal anali atawapeza iwo. Sindikanatha kulankhula popeza malingaliro anga anadzaza mkati mwanga.

“Asakutaya nthaŵi, iwo ananyamula katundu wathu, kuphatikizapo njinga yamoto yokutidwa ndi matopeyo, imene mbale m’chenicheni anainyamula kupita nayo ku malo ake. Ochereza anga anali okwatirana aŵiri odzichepetsa, mkaziyo atavala siketi yaitali yopetedwa bwino, yochindikala koposa. ‘Mudzatenga kama yathu,’ iwo anatero. Sindinafune kuti iwo agone pansi, makamaka popeza mkaziyo anali ndi pakati. Koma iwo anawumirira.

“Chinthu chotsatira chimene ndinadziŵa, inali 8:00 a.m. Winawake anali kugogoda pa chitseko. ‘Abale akonzekera kaamba ka utumiki,’ ndinawuzidwa tero. Ndikumawona nkhope zawo zoyembekezera zikumawala ndi chiyamikiro, ndinalibe chosankha china koma kutulutsa thupi langa lopweteka kunja kwa kama ndi kuyamba ulendowo. Ndipo unali ulendo wotenthetsa mtima chotani nanga! Pamene ndinatsagana ndi abalewo mu utumiki wawo, iwo anangodzazidwa ndi chimwemwe ndi kutenthedwa maganizo. Ndinasinkhasinkha pa mmene analiri ofunika maulendo amenewa, mosasamala kanthu za zonse zimene timapitamo​—monga ‘mitsinje ya madzi m’dziko louma.’​—Yesaya 32:2.

“Tsiku lotsatira tinachezera mudzi kumene pasitala wa evangelical anawopsyeza kuphwanya misonkhano yathu pamene ndinafikako. Pambuyo pa nkhani ya Baibulo, munthu wonenepa anandipatsa chanza cha chiBoliviaa ndipo ananena kuti: ‘Mbale, uli ndi chowonadi!’ Pambuyo pake, ndinafunsa ndani amene iye anali. ‘Ndi pasitala,’ iwo anatero.

“Ulendo wokuchezera ku Kami unatha mofulumira, ndipo tinali kuchoka. Abalewo anali atakonza njinga yamotoyo ndi kuchapa zovala zathu zonse zamatope. Pamene tinatchula mwamuna amene anatibwereka ife zipangizoyo, iwo anadabwa, popeza iye amadziŵika monga mmodzi wa omwe sathandiza nkomwe. Pambuyo pa kukupatirana kwambiri ndi kugwirana chanza, tinanyamuka ndipo mwamsanga tinabwerera kukawona mwini wa shopu ya kofi wachifundoyo. Pambuyo pa kubwezera chirichonse, tinamfunsa iye: ‘Kodi ndi ndalama zingati zimene tiri mu ngongole kwa inu?’ ‘Palibe chirichonse,’ iye anayankha. ‘Ndinali wachimwemwe kuthandiza!’

“Pamene tinabwerera ku Oruro, maora asanu pambuyo pake, tinalingalira zakuti chinali chofunika chotani nanga kusagonjera ndiponso mmene Yehova mozizwitsa anatisamalirira ife. Aníbal anasonkhezeredwa mozama ndi chokumana nachocho kotero kuti iye anafuula: ‘Ndingapereke china chirichonse kuti tibwererekonso!’ Iye wachita chimenecho, akumatenga oyang’anira oyendayenda ena ndi njinga yake yamoto kupita ku Kami ndi malo ena. Inde, tinali ndi chifukwa champhamvu cha kukhala otsimikiziridwa mokulira za chikondi cha Yehova.”​—Monga momwe yakambidwa ndi woyang’anira wadera Ricardo Hernández.

[Mawu a M’munsi]

a Chanza cha chiBolivia chimapangidwa ndi kupatsana moni wa pamanja, kumenya pang’ono pa msana, ndipo kenaka kupatsananso moni wa pamanja.

[Zithunzi patsamba 23]

Msewu wokhotakhota wa m’phiri womatsogolera ku mzinda wa mgodi wa Kami

Msewu kupyola m’mapiri kupita ku Kami

Abulu angakhale othandiza kwambiri m’nthaŵi ya ngozi!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena